Salimo 86:1-17

  • Palibe mulungu amene angafanane ndi Yehova

    • Yehova ndi wokonzeka kukhululuka (5)

    • Mitundu yonse ya anthu idzalambira Yehova (9)

    • ‘Ndilangizeni za njira yanu’ (11)

    • “Ndithandizeni kuti ndiziopa dzina lanu ndi mtima wonse” (11)

Pemphero la Davide. 86  Tcherani khutu* inu Yehova ndipo mundiyankhe,Chifukwa ndavutika komanso ndasauka.+   Tetezani moyo wanga chifukwa ndine wokhulupirika.+ Pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani,Chifukwa ndinu Mulungu wanga.+   Ndikomereni mtima inu Yehova,+Chifukwa ndimaitana inu tsiku lonse.+   Chititsani kuti mtumiki wanu asangalale,*Chifukwa ndimayangʼana kwa inu, Yehova.   Inu Yehova ndinu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+Mumasonyeza chikondi chokhulupirika chochuluka kwa onse amene amaitana inu.+   Mvetserani pemphero langa inu Yehova.Ndipo mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+   Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndidzaitana inu,+Chifukwa inu mudzandiyankha.+   Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu,+Palibe aliyense amene wachita zinthu zofanana ndi zimene inu mwachita.+   Mitundu yonse ya anthu imene munapangaIdzabwera nʼkudzagwada pamaso panu, inu Yehova,+Ndipo idzalemekeza dzina lanu.+ 10  Chifukwa inu ndinu wamkulu ndipo mumachita zinthu zodabwitsa.+Inu nokha ndinu Mulungu.+ 11  Ndilangizeni inu Yehova, za njira yanu.+ Kuti ndiyende mʼchoonadi chanu.+ Ndithandizeni kuti ndiziopa dzina lanu ndi mtima wonse.*+ 12  Ndimakutamandani ndi mtima wanga wonse, inu Yehova Mulungu wanga,+Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale, 13  Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika chimene mumandisonyeza ndi chachikuluNdipo mwapulumutsa moyo wanga ku dzenje la Manda.*+ 14  Inu Mulungu, anthu onyada andiukira.+Gulu la anthu ankhanza likufuna kuchotsa moyo wanga,Ndipo iwo sakulemekezani.*+ 15  Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima,Wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka ndiponso wokhulupirika.*+ 16  Ndiyangʼaneni ndipo mundikomere mtima.+ Patsani mtumiki wanu mphamvu,+Ndipo pulumutsani mwana wa kapolo wanu wamkazi. 17  Ndisonyezeni chizindikiro cha* ubwino wanu,Kuti anthu amene amadana nane aone ndipo achititsidwe manyazi, Chifukwa inu Yehova ndi amene mumandithandiza komanso kundilimbikitsa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Weramani ndipo mumvetsere.”
Kapena kuti, “moyo wa mtumiki wanu usangalale.”
Kapena kuti, “Ndipatseni mtima wosagawanika.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “sanaike inu patsogolo pawo.”
Kapena kuti, “wachoonadi.”
Kapena kuti, “umboni wa.”