Salimo 23:1-6
Nyimbo ya Davide.
23 Yehova ndi Mʼbusa wanga.+
Sindidzasowa kanthu.+
2 Amandigoneka mʼmalo odyetsera ziweto a msipu wambiri.Amanditsogolera kumalo opumira a madzi ambiri.*+
3 Amanditsitsimula.*+
Amanditsogolera munjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.+
4 Ngakhale ndikuyenda mʼchigwa chamdima wandiweyani,+Sindikuopa kanthu,+Chifukwa inu muli ndi ine.+Chibonga chanu ndi ndodo yanu zikundipangitsa kumva kuti ndine wotetezeka.*
5 Mumandipatsa chakudya patebulo pamaso pa adani anga.+
Ndimatsitsimulidwa mukandidzoza mafuta kumutu.+Kapu yanga ndi yodzaza bwino.+
6 Ndithu, masiku onse a moyo wanga ndidzasangalala ndi ubwino wanu komanso chikondi chanu chokhulupirika,+Ndipo ndidzakhala mʼnyumba ya Yehova kwa moyo wanga wonse.+
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “a madzi odikha.”
^ Kapena kuti, “Amatsitsimula moyo wanga.”
^ Kapena kuti, “Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimandilimbikitsa.”