Salimo 37:1-40

  • Anthu amene amadalira Yehova zinthu zimawayendera bwino

    • Usakhumudwe chifukwa cha anthu oipa (1)

    • “Uzisangalala chifukwa cha Yehova” (4)

    • “Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako” (5)

    • “Ofatsa adzalandira dziko lapansi” (11)

    • Olungama sadzasowa chakudya (25)

    • Olungama adzakhala padziko lapansi kwamuyaya (29)

Salimo la Davide. א [Aleph] 37  Usakhumudwe* chifukwa cha anthu oipaKapena kuchitira nsanje anthu ochita zoipa.+   Iwo adzafota mwamsanga ngati udzu+Ndipo adzanyala ngati msipu wobiriwira. ב [Beth]   Uzikhulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino.+Ukhale padziko lapansi* ndipo uzichita zinthu mokhulupirika.+   Uzisangalala* chifukwa cha Yehova,Ndipo adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka. ג [Gimel]   Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,*+Uzimudalira ndipo iye adzakuthandiza.+   Iye adzachititsa kuti kulungama kwako kuwale ngati mʼmawa,Ndipo chilungamo chako adzachichititsa kuti chiwale ngati dzuwa masana. ד [Daleth]   Khala chete pamaso pa Yehova+Ndipo umuyembekezere moleza mtima. Usakhumudwe ndi munthuAmene amakonza ziwembu nʼkuzikwaniritsa popanda vuto lililonse.+ ה [He]   Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.+Usapse mtima nʼkuchita zoipa.*   Chifukwa anthu oipa adzaphedwa,+Koma amene akuyembekezera Yehova adzalandira dziko lapansi.+ ו [Waw] 10  Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso.+Udzayangʼana pamene ankakhala,Ndipo sadzapezekapo.+ 11  Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.+ ז [Zayin] 12  Munthu woipa amakonzera chiwembu munthu wolungama,+Ndipo amamukukutira mano. 13  Koma Yehova adzamuseka,Chifukwa akudziwa kuti mapeto ake adzafika.+ ח [Heth] 14  Oipa asolola malupanga awo ndipo akunga mauta* awo,Kuti agwetse oponderezedwa ndi osauka,Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zolungama. 15  Koma lupanga lawo lidzalasa mtima wawo womwe,+Mauta awo adzathyoledwa. ט [Teth] 16  Zinthu zochepa zimene munthu wolungama ali nazo ndi zabwinoKusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+ 17  Chifukwa manja a anthu oipa adzathyoledwa,Koma Yehova adzathandiza anthu olungama. י [Yod] 18  Yehova amadziwa mavuto amene anthu osalakwa akukumana nawo,*Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+ 19  Pa nthawi ya tsoka sadzachita manyazi,Ndipo pa nthawi ya njala adzakhala ndi chakudya chochuluka. כ [Kaph] 20  Koma oipa onse adzatheratu,+Adani a Yehova adzasowa mofulumira ngati malo okongola odyetsera ziweto amene msipu wake wobiriwira suchedwa kufota.Iwo adzatha mofulumira ngati utsi. ל [Lamed] 21  Munthu woipa amabwereka zinthu za ena koma osabweza,Koma wolungama amakhala wowolowa manja* ndipo amagawira ena zinthu zake.+ 22  Anthu amene Mulungu wawadalitsa adzalandira dziko lapansi,Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+ מ [Mem] 23  Yehova akasangalala ndi njira za munthu+Amamusonyeza zoyenera kuchita pa moyo wake.+ 24  Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu,+Chifukwa Yehova wamugwira dzanja kuti amuthandize.*+ נ [Nun] 25  Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula,Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+ 26  Nthawi zonse amakongoza ena zinthu zake mokoma mtima,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso. ס [Samekh] 27  Pewani kuchita zoipa ndipo muzichita zabwino,+Mukatero mudzakhala padziko lapansi mpaka kalekale. 28  Chifukwa Yehova amakonda chilungamo,Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+ ע [Ayin] Adzawateteza nthawi zonse.+Koma mbadwa za anthu oipa zidzaphedwa.+ 29  Olungama adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.+ פ [Pe] 30  Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,*Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+ 31  Chilamulo cha Mulungu wake chili mumtima mwake.+Iye adzachitsatira nthawi zonse.+ צ [Tsade] 32  Woipa amayangʼanitsitsa munthu wolungama,Ndipo amafuna kuti amuphe. 33  Koma Yehova sadzasiya wolungama mʼmanja mwa woipayo+Kapena kumupeza wolakwa akamaweruzidwa.+ ק [Qoph] 34  Yembekezera Yehova ndi kutsatira njira zake,Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi. Oipa akamadzaphedwa,+ iwe udzaona.+ ר [Resh] 35  Ine ndaona munthu wankhanza komanso woipaZinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+ 36  Koma anafa mwadzidzidzi ndipo sanapezekenso.+Ndinamufunafuna ndipo sindinamupeze.+ ש [Sin] 37  Onani munthu wosalakwa,*Ndipo yangʼanitsitsani munthu wolungama,+Chifukwa tsogolo la munthu ameneyo lidzakhala lamtendere.+ 38  Koma anthu onse ochimwa adzawonongedwa.Mʼtsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+ ת [Taw] 39  Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya mavuto.+ 40  Yehova adzawathandiza nʼkuwapulumutsa.+ Adzawalanditsa kwa oipa nʼkuwapulumutsa,Chifukwa athawira kwa iye.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Usakwiye.”
Kapena kuti, “mʼdzikoli.”
Kapena kuti, “Uzipeza chisangalalo chako chachikulu.”
Kapena kuti, “Pereka njira yako kwa Yehova.”
Mabaibulo ena amati, “chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoipa.”
Kapena kuti, “zingwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amadziwa masiku a anthu osalakwa.”
Kapena kuti, “amakomera ena mtima.”
Kapena kuti, “akumuthandiza ndi Dzanja Lake.”
Kapena kuti, “pamalankhula zinthu zanzeru chapansipansi.”
Kapena kuti, “munthu wokhulupirika.”