Salimo 31:1-24

  • Kuthawira kwa Yehova

    • “Ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu” (5)

    • “Yehova Mulungu wa choonadi” (5)

    • Ubwino wa Mulungu ndi wochuluka (19)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 31  Ndathawira kwa inu Yehova.+ Musalole kuti ndichite manyazi.+ Ndipulumutseni chifukwa cha chilungamo chanu.+   Tcherani khutu lanu* kwa ine. Ndilanditseni mofulumira.+ Mukhale malo anga otetezeka apaphiri,Mukhale malo a mpanda wolimba kuti mundipulumutse.+   Chifukwa inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+Chifukwa cha dzina lanu,+ mudzanditsogolera ndi kundilozera njira.+   Mudzandipulumutsa mu ukonde umene anditchera mwachinsinsi,+Chifukwa inu ndinu malo anga achitetezo.+   Ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.+ Mwandiwombola, inu Yehova Mulungu wa choonadi.*+   Ndimadana ndi anthu amene amadzipereka kwa mafano achabechabe komanso opanda pake.Koma ine ndimadalira Yehova.   Ndidzasangalala kwambiri chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika,Chifukwa mwaona kusautsika kwanga.+Mukudziwa mavuto aakulu amene ndili nawo.*   Simunandipereke mʼmanja mwa adani,Koma mwachititsa kuti ndiime pamalo otetezeka.*   Ndikomereni mtima inu Yehova, chifukwa ndavutika kwambiri. Maso anga afooka chifukwa cha chisoni,+ chimodzimodzinso thupi langa lonse.*+ 10  Moyo wanga ndi wodzaza ndi chisoni+Ndipo zaka za moyo wanga nʼzodzaza ndi kubuula.+ Mphamvu zanga zikuchepa chifukwa cha zolakwa zanga,Mafupa anga afooka.+ 11  Adani anga onse amandinyoza,+Makamaka anthu oyandikana nawo. Ndipo anthu ondidziwa amachita nane mantha.Akandiona ndili panja amandithawa.+ 12  Iwo anandiiwala* ngati kuti ndinafa.Ndili ngati chiwiya chosweka. 13  Ndamva mphekesera zambiri zoipa.Ndikuchita mantha chifukwa ndikuopsezedwa kuchokera kumbali zonse.+ Akasonkhana pamodzi kuti alimbane nane,Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+ 14  Koma ine ndimakhulupirira inu Yehova.+ Ndipo ndikunena kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”+ 15  Moyo wanga uli* mʼmanja mwanu. Ndilanditseni mʼmanja mwa adani anga komanso kwa anthu amene akundizunza.+ 16  Ndikomereni mtima, ine mtumiki wanu.+ Ndipulumutseni ndi chikondi chanu chokhulupirika. 17  Inu Yehova, musalole kuti ndichite manyazi pamene ndikukuitanani.+ Anthu oipa achite manyazi.+Apite ku Manda* ndipo akhale chete.+ 18  Milomo yonena mabodza isowe chonena,+Milomo imene imalankhula modzikweza komanso monyoza wolungama. 19  Ubwino wanu ndi wochuluka kwambiri!+ Ubwino umenewu mwasungira anthu amene amakuopani,+Ndipo mwausonyeza kwa anthu amene amathawira kwa inu, pamaso pa anthu onse.+ 20  Mudzawabisa mʼmalo otetezeka pafupi ndi inu,+Kuwachotsa kwa anthu amene awakonzera chiwembu.Mudzawabisa mʼmalo anu otetezekaKuti anthu amene akuwanyoza asawapeze.*+ 21  Yehova atamandike,Chifukwa mʼnjira yodabwitsa, wandisonyeza chikondi chokhulupirika+ mumzinda umene wazunguliridwa ndi adani.+ 22  Koma ine ndinapanikizika nʼkunena kuti: “Ndifa ndipo simudzandionanso.”+ Koma inu munamva kuchonderera kwanga kopempha thandizo pamene ndinafuulira kwa inu.+ 23  Kondani Yehova, inu nonse amene muli okhulupirika kwa iye!+ Yehova amateteza okhulupirika,+Koma aliyense wodzikuza amamulanga kwambiri.+ 24  Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu,+Inu nonse amene mukuyembekezera Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Weramani nʼkumvetsera.”
Kapena kuti, “Mulungu wokhulupirika.”
Kapena kuti, “mavuto a moyo wanga.”
Kapena kuti, “pamalo otakasuka.”
Kapena kuti, “moyo wanga komanso mʼmimba mwanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anandichotsa mumtima mwawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nthawi zanga zili.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ku mikangano ya malilime.”