Salimo 55:1-23

  • Pemphero loperekedwa pa nthawi imene waukiridwa ndi mnzako

    • Kunyozedwa ndi mnzako wapamtima (12-14)

    • “Umutulire Yehova nkhawa zako” (22)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. 55  Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa,+Ndipo musanyalanyaze pempho langa lakuti mundichitire chifundo.*+   Ndimvetsereni ndipo mundiyankhe.+ Mtima wanga suli mʼmalo chifukwa cha nkhawa zanga,+Ndipo ndikuvutika mumtima mwanga   Chifukwa cha zimene mdani wanga akunenaKomanso chifukwa chakuti woipa akundipanikiza. Iwo andiunjikira mavuto,Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+   Mtima wanga ukundipweteka kwambiri,+Ndipo ndikuopa imfa.+   Ndagwidwa ndi mantha ndipo ndikunjenjemera,Komanso ndikunthunthumira.   Nthawi zonse ndimanena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa! Ndikanaulukira kutali nʼkukakhala malo otetezeka.   Ndikanathawira kutali.+ Ndikanapita kukakhala mʼchipululu.+ (Selah)   Ndikanathawira kumalo otetezeka,Kutali ndi mphepo yamphamvu, kutali ndi mphepo yamkuntho.”   Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani mapulani awo,*+Chifukwa ndaona zachiwawa ndi mikangano mumzinda. 10  Masana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.Ndipo mumzindawo muli chidani ndi mavuto.+ 11  Mmenemo muli mavuto okhaokha.Ndipo kuponderezana ndi chinyengo sizimachoka kubwalo la mzindawo.+ 12  Chifukwa amene akundinyoza si mdani.+Akanakhala mdani ndikanapirira. Amene wandiukira si munthu wodana nane kwambiri.Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala. 13  Koma ndi iwe, munthu ngati ine ndemwe,*+Mnzanga weniweni amene ndikumudziwa bwino.+ 14  Tinali mabwenzi apamtima.Tinkayenda limodzi ndi gulu la anthu kupita kunyumba ya Mulungu. 15  Iwo awonongedwe!+ Atsikire ku Manda* ali amoyo.Chifukwa mʼmalo amene amakhala komanso mʼmitima yawo muli zoipa. 16  Koma ine ndidzafuulira Mulungu,Ndipo Yehova adzandipulumutsa.+ 17  Usiku, mʼmawa ndi masana ndimavutika ndipo ndimabuula,*+Koma Mulungu amamva mawu anga.+ 18  Iye adzandipulumutsa* kwa anthu amene akundiukira nʼkundipatsa mtendere,Chifukwa gulu la anthu landiukira.+ 19  Mulungu adzamva ndipo adzawapatsa chilango,+Amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale.+ (Selah) Iwo adzakana kusintha,Anthu amene sanaope Mulungu.+ 20  Iye* anaukira anthu amene anali naye pamtendere.+Iye anaphwanya pangano lake.+ 21  Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta amumkaka,+Koma mumtima mwake amakonda nkhondo. Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta,Koma ali ngati malupanga akuthwa.+ 22  Umutulire Yehova nkhawa zako,+Ndipo iye adzakuthandiza.+ Iye sadzalola kuti munthu wolungama agwe.*+ 23  Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipawo mʼdzenje lakuya.+ Anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso achinyengowo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+ Koma ine ndidzakhulupirira inu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ndipo musabisale ndikamapemphera kuti mundithandize.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sokonezani lilime lawo.”
Kapena kuti, “munthu wofanana ndi ine.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “ndimabangula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzandiwombola.”
Ameneyu ndi mnzake wakale amene watchulidwa muvesi 13 ndi 14.
Kapena kuti, “adzandire.”