Salimo 103:1-22
Salimo la Davide.
103 Moyo wanga utamande Yehova.Chilichonse cha mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.
2 Moyo wanga utamande Yehova,Ndisaiwale zinthu zonse zimene wachita.+
3 Iye amakukhululukira zolakwa zako zonse+Ndipo amachiritsa matenda ako onse.+
4 Iye amawombola moyo wako kudzenje,*+Ndipo amakuveka chikondi chake chokhulupirika komanso chifundo ngati chisoti chachifumu.+
5 Iye amakupatsa zinthu zabwino+ nthawi yonse ya moyo wako, zimene umakhutira nazo,Kuti ukhalebe wachinyamata ndi wamphamvu ngati chiwombankhanga.+
6 Yehova amachita chilungamo+ kwa anthu onse oponderezedwaNdipo amaweruza milandu yawo mwachilungamo.+
7 Anadziwitsa Mose njira zake,+Ndipo ana a Isiraeli anawadziwitsa zochita zake.+
8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,*+Wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.*+
9 Iye sadzakhalira kutipezera zifukwa nthawi zonse,+Kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.+
10 Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu,+Kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.+
11 Mofanana ndi mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,Chikondi chokhulupirika chimene amasonyeza anthu amene amamuopa ndi chachikulu kwambiri.+
12 Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa,Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.+
13 Mofanana ndi bambo amene amasonyeza chifundo kwa ana ake,Yehova wasonyezanso chifundo kwa anthu amene amamuopa.+
14 Chifukwa iye akudziwa bwino mmene anatipangira,+Amakumbukira kuti ndife fumbi.+
15 Masiku a moyo wa munthu ali ngati masiku a udzu.+Iye amaphuka ngati duwa lakutchire.+
16 Koma mphepo ikawomba limafa,Ndipo zimangokhala ngati panalibepo.*
17 Koma Yehova adzapitiriza kusonyeza chikondi chake chokhulupirika mpaka kalekaleKwa anthu amene amamuopa,+Ndipo adzapitiriza kusonyeza chilungamo chake kwa ana a ana awo.+
18 Adzapitiriza kuchita zimenezi kwa anthu amene amasunga pangano lake,+Ndi kwa anthu amene amatsatira malamulo ake mosamala.
19 Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba.+Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.+
20 Tamandani Yehova, inu angelo ake onse+ amphamvu,Amene amamvera mawu ake komanso kuchita zimene wanena.+
21 Tamandani Yehova, inu magulu ake onse a angelo,+Atumiki ake amene amachita chifuniro chake.+
22 Tamandani Yehova, inu ntchito zake zonse,Mʼmalo onse amene iye akulamulira.
Moyo wanga wonse utamande Yehova.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kumanda.”
^ Kapena kuti, “ndi wachisomo.”
^ Kapena kuti, “ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo pamalo amene linali salidziwanso.”