Salimo 41:1-13

  • Pemphero la munthu amene akudwala pabedi lake

    • Mulungu amasamalira anthu amene akudwala (3)

    • Kuukiridwa ndi mnzanga wapamtima (9)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 41  Wosangalala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.   Yehova adzamuteteza nʼkusunga moyo wake. Anthu ena adzaona kuti akusangalala,+Ndipo Mulungu sadzamupereka kwa adani ake.*+   Yehova adzathandiza munthu woganizira wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.+Mudzamusamalira bwino kwambiri pa nthawi imene akudwala.   Ine ndinati: “Inu Yehova, ndikomereni mtima.+ Ndichiritseni,+ chifukwa ndakuchimwirani.”+   Koma adani anga amanena zoipa zokhudza ine kuti: “Kodi ameneyu afa liti kuti dzina lake liiwalike?”   Mmodzi wa iwo akabwera kudzandiona, sanena zinthu moona mtima. Amasonkhanitsa nkhani zoipa.Akatero amachoka nʼkukafalitsa nkhani zoipazo.   Onse amene amadana nane akunongʼonezana zokhudza ine.Akupangana zoti andichitire chiwembu. Iwo akuti:   “Chinthu chochititsa mantha chamuchitikira.Tsopano popeza iye ali chigonere, sadzadzukanso.”+   Ngakhale munthu amene ndinkakhala naye mwamtendere, amene ndinkamukhulupirira,+Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.+ 10  Koma inu Yehova, ndikomereni mtima nʼkundidzutsa,Kuti ndiwapatse chilango chifukwa cha zimene anachita. 11  Mdani wanga akapanda kundigonjetsa nʼkufuula mosangalala, Ndidzadziwa kuti mukusangalala nane.+ 12  Koma ine mumandithandiza chifukwa choti ndine wokhulupirika,+Ndipo mudzasangalala nane mpaka kalekale.*+ 13  Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,Kuyambira panopo mpaka kalekale.*+ Ame! Ame!

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kwa adani ake kuti achite naye zimene akufuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzandiika pamaso panu mpaka kalekale.”
Kapena kuti, “Kuyambira kalekale mpaka kalekale.”