Salimo 127:1-5

  • Popanda Mulungu, chilichonse nʼchopanda phindu

    • “Yehova akapanda kumanga nyumba” (1)

    • Ana ndi mphoto yochokera kwa Mulungu (3)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Solomo. 127  Yehova akapanda kumanga nyumba,Omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.+ Yehova akapanda kulondera mzinda,+Alonda amakhala maso pachabe.   Mukudzuka mʼmawa pachabe,Mukungovutika kugwira ntchito mpaka usiku,Mumapeza chakudya movutikira,Chifukwa Mulungu amapereka zinthu zofunika kwa anthu amene amawakonda komanso amawapatsa tulo tabwino.+   Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.+Chipatso cha mimba ndi mphoto yochokera kwa Mulungu.+   Ana a bambo wachinyamata,+Ali ngati mivi mʼdzanja la mwamuna wamphamvu.   Wosangalala ndi mwamuna amene wadzaza kachikwama kake ka mivi ndi mivi imeneyo.+ Abambo oterowo sadzachita manyazi,Chifukwa ana awo adzalankhula ndi adani pageti la mzinda.

Mawu a M'munsi