Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi MʼBaibulo Muli Nkhani Zotani?

KODI MUNGAPEZE BWANJI MALEMBA MʼBAIBULO?

MʼBaibulo muli mabuku 66 ndipo lili ndi zigawo ziwiri. Chigawo choyamba (ena amati Chipangano Chakale) chinalembedwa mʼChiheberi ndi Chiaramu. Chigawo chachiwiri ndi cha Malemba a Chigiriki (ena amati Chipangano Chatsopano). Buku lililonse linagawidwa mʼmachaputala ndi mavesi. Mukapeza lemba, mudzaona kuti limayamba ndi dzina la buku kenako chaputala nʼkumaliza ndi vesi kapena mavesi. Mwachitsanzo, Genesis 1:1 likutanthauza kuti buku la Genesis chaputala 1 vesi 1.