Salimo 34:1-22

  • Yehova amapulumutsa atumiki ake

    • “Tiyeni tonse tikweze dzina lake” (3)

    • Mngelo wa Yehova amateteza (7)

    • “Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino” (8)

    • ‘Palibe fupa lake ngakhale limodzi limene linathyoledwa’ (20)

Salimo la Davide, pa nthawi imene anachita zinthu ngati wamisala+ pamaso pa Abimeleki, moti anamuthamangitsa ndipo Davideyo anathawa. א [Aleph] 34  Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.Sindidzasiya kumutamanda ndi pakamwa panga. ב [Beth]   Monyadira, ndidzapereka ulemu kwa Yehova.*+Ofatsa adzamva ndipo adzasangalala. ג [Gimel]   Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine,+Tiyeni tonse tikweze dzina lake. ד [Daleth]   Ndinapemphera kwa Yehova ndipo iye anandiyankha.+ Anandipulumutsa ku zinthu zonse zimene zimandichititsa mantha.+ ה [He]   Amene anamukhulupirira anasangalala,Ndipo nkhope zawo sizinachite manyazi. ז [Zayin]   Munthu wonyozekayu anaitana ndipo Yehova anamva. Anamupulumutsa ku mavuto ake onse.+ ח [Heth]   Mngelo wa Yehova amamanga msasa kuzungulira anthu onse amene amaopa Mulungu,+Ndipo amawapulumutsa.+ ט [Teth]   Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.+Wosangalala ndi munthu amene amathawira kwa iye. י [Yod]   Opani Yehova, inu oyera ake onse,Chifukwa onse amene amamuopa sasowa kanthu.+ כ [Kaph] 10  Ngakhale mikango yamphamvu* ingakhale ndi njala chifukwa chosowa chakudya.Koma anthu amene akufunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.+ ל [Lamed] 11  Bwerani kuno ana anga, ndimvetsereni.Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.+ מ [Mem] 12  Kodi ndi ndani pakati panu amene amakonda moyo,Ndipo angakonde atakhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+ נ [Nun] 13  Ndiyetu muteteze lilime lanu ku zinthu zoipa,+Komanso milomo yanu kuti isalankhule chinyengo.+ ס [Samekh] 14  Siyani kuchita zinthu zoipa ndipo muzichita zabwino.+Yesetsani kukhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+ ע [Ayin] 15  Maso a Yehova ali pa olungama,+Ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.+ פ [Pe] 16  Koma Yehova amakwiyira anthu ochita zoipa,Iye adzawawononga ndipo sadzakumbukiridwanso padziko lapansi.+ צ [Tsade] 17  Olungama anafuula ndipo Yehova anamva,+Iye anawapulumutsa mʼmavuto awo onse.+ ק [Qoph] 18  Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+Iye amapulumutsa anthu amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.*+ ר [Resh] 19  Mavuto* a munthu wolungama ndi ambiri,+Koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.+ ש [Shin] 20  Amateteza mafupa onse a munthu wolungamayo.Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+ ת [Taw] 21  Munthu woipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzafa.Anthu odana ndi munthu wolungama adzapezeka olakwa. 22  Yehova amawombola moyo wa atumiki ake.Palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeke wolakwa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ndidzadzitamandira mwa Yehova.”
Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”
Kapena kuti, “amene akhumudwa.”
Kapena kuti, “Masoka.”