Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

A4

Dzina la Mulungu MʼMalemba a Chiheberi

Dzina la Mulungu mʼzilembo zakale za Chiheberi zomwe zinkagwiritsidwa ntchito Ayuda asanapite ku ukapolo ku Babulo

Dzina la Mulungu mʼzilembo za Chiheberi zomwe zinkagwiritsidwa ntchito Ayuda atabwerera kuchoka ku ukapolo ku Babulo

Dzina la Mulungu limene limalembedwa pogwiritsa ntchito zilembo 4 za Chiheberi יהוה, limapezeka pafupifupi nthawi 7,000 mʼMalemba a Chiheberi. MʼBaibuloli, zilembo 4 zimenezi zamasuliridwa kuti “Yehova.” Dzina limeneli ndi lomwe limapezeka kwambiri mʼBaibulo kuposa dzina lililonse. Ngakhale kuti anthu omwe anauziridwa kulemba Baibulo anagwiritsa ntchito mayina ena aulemu monga akuti “Wamphamvuyonse,” “Wamʼmwambamwamba” komanso “Ambuye,” iwo ankalemba zilembo 4 zimenezi akafuna kutchula dzina lenileni la Mulungu.

Yehova Mulungu ndi amene anatsogolera anthu olemba Baibulo kuti azigwiritsa ntchito dzina lake. Mwachitsanzo, anatsogolera mneneri Yoweli kulemba kuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32) Ndiponso, Mulungu anachititsa wolemba Masalimo wina kulemba kuti: “Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) Ndipotu dzina la Mulunguli limapezeka nthawi 700 mʼbuku la Masalimo lokha, lomwe ndi buku la ndakatulo ndiponso nyimbo zomwe anthu a Mulungu ankaimba komanso kuziloweza. Ndiyeno nʼchifukwa chiyani dzina la Mulungu silipezeka mʼMabaibulo ambiri? Nʼchifukwa chiyani mʼBaibuloli anasankha kulemba dzina la Mulungu kuti “Yehova”? Nanga dzina la Mulungu loti Yehova, limatanthauza chiyani?

Mawu ena ochokera mʼbuku la Masalimo omwe ali mu Mpukutu wa ku Nyanja Yakufa amene analembedwa mu nthawi ya Yesu. Mawu ena alembedwa mʼnjira imene ankalembera Chiheberi, Ayuda atabwera kuchokera ku ukapolo ku Babulo, koma zilembo 4 zoimira dzina la Mulungu zalembedwa mʼChiheberi chakale

Nʼchifukwa chiyani dzinali silipezeka mʼMabaibulo ambiri? Pali zifukwa zosiyanasiyana. Anthu ena amaona kuti Mulungu Wamphamvuyonse safunika kukhala ndi dzina lapadera lomutchulira. Ena anatengera mwambo wa Chiyuda wosafuna kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, mwina chifukwa choopa kuti angapeputse dzinalo. Pomwe enanso amaganiza kuti popeza katchulidwe kenikeni ka dzina la Mulungu sikakudziwika, ndi bwino kumagwiritsa ntchito mayina aulemu monga “Ambuye” kapena “Mulungu.” Koma zifukwa zonsezi nʼzosamveka tikaganizira mfundo zotsatirazi:

  • Anthu amene amanena kuti Mulungu Wamphamvuyonse safunikira kukhala ndi dzina lake lenileni, ayenera kudziwanso mfundo yakuti mʼMabaibulo amene analipo ngakhale Khristu asanabwere, mumapezeka dzina lenileni la Mulungu. Monga mmene taonera kale, Mulungu anatsogolera anthu kuti alembe dzinali mʼMawu ake nthawi zoposa 7,000. Izi zikusonyezeratu kuti Mulungu amafuna kuti tidziwe dzina lake nʼkumaligwiritsa ntchito.

  • Omasulira Baibulo amene anachotsa dzina la Mulungu pofuna kulemekeza mwambo wa Chiyuda, amaiwala mfundo ina yofunika kwambiri. Nʼzoona kuti alembi ena a Chiyuda ankakana kutchula dzina la Mulungu koma sanalichotse mʼMabaibulo awo. Mʼmipukutu yakale yomwe inapezeka mʼdera la Qumran, lomwe lili pafupi ndi Nyanja Yakufa, dzina la Mulungu limapezekamo kambirimbiri. Omasulira Baibulo ena amavomereza kuti dzina la Mulungu linkapezeka mʼmipukutu yoyambirira koma mʼmalo onse amene linkapezekamo ankalichotsa nʼkumaikamo dzina la ulemu lakuti “AMBUYE” mʼzilembo zazikulu. Koma funso ndi lakuti, nʼchifukwa chiyani omasulira Baibulo amenewa anachita zimenezi ngakhale ankadziwa kuti dzinali linkapezeka mʼmipukutu ya Baibulo kambirimbiri? Kodi ndi ndani anawapatsa mphamvu yochotsa dzina la Mulungu mʼBaibulo? Omasulirawa ndi amene angadziwe mayankho a mafunso amenewa.

  • Nʼzodabwitsa kuti anthu amene amati dzina la Mulungu siliyenera kugwiritsidwa ntchito chifukwa sitidziwa katchulidwe kake kenikeni, amatha kugwiritsa ntchito dzina la Yesu. Komatu ophunzira a Yesu ankatchula dzinali mosiyana kwambiri ndi mmene timatchulira masiku ano. Akhristu a Chiyuda ankatchula dzina la Yesu kuti Ye·shuʹa‛. Ndipo dzina lakuti “Khristu,” ankalitchula kuti Ma·shiʹach, kapena “Mesiya.” Akhristu olankhula Chigiriki ankatchula dzinali kuti I·e·sousʹ Khri·stosʹ, ndipo olankhula Chilatini ankalitchula kuti Ieʹsus Chriʹstus. Koma motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, omasulira Malemba a Chigiriki anaika dzinali mʼBaibulo. Zimenezi zikusonyeza kuti Akhristu oyambirira ankatsatira mmene anthu ankatchulira dzinali pa nthawiyo mʼchilankhulo chawo. Choncho Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inaona kuti nʼzomveka kutchula dzina la Mulungu kuti “Yehova” ngakhale kuti sitikudziwa bwinobwino mmene ankatchulira dzinali mʼChiheberi chakale.

Nʼchifukwa chiyani omasulira Baibulo la Dziko Latsopano anasankha kulemba dzina la Mulungu kuti “Yehova”? MʼChichewa, zilembo 4 zoimira dzina la Mulungu (יהוה) amazilemba kuti YHWH. Zilembo 4 zoimira dzina la Mulungu zilibe mavawelo chifukwa mawu onse a mʼChiheberi chakale anali opanda mavawelo. Koma anthu ambiri atayamba kugwiritsa ntchito mawu a Chiheberi, owerenga anayamba kuikirira mavawelo.

Patadutsa zaka pafupifupi 1,000 kuchokera pamene anamaliza kulemba Malemba a Chiheberi, akatswiri a maphunziro a Chiyuda anakonza njira yodziwira mmene angatchulire mawu a Chiheberi komanso tizizindikiro towathandiza kudziwa mavawelo omwe angagwiritse ntchito powerenga Chiheberi. Pa nthawi imeneyi Ayuda ambiri ankaganiza kuti nʼkulakwa kutchula dzina la Mulungu moti anapeza mawu ena oti aziwagwiritsa ntchito akafuna kutchula dzinalo. Zikuoneka kuti pamene ankakopera zilembo 4 za Chiheberi zija anaphatikiza zilembozi ndi mavawelo amʼmawu omwe ankawagwiritsa ntchito akafuna kutchula dzina la Mulungu. Choncho mavawelo amene anawaikawo sathandiza kudziwa bwinobwino mmene dzinali ankalitchulira poyambirira mʼChiheberi. Ena amanena kuti dzinali linkatchulidwa kuti “Yahweh,” pomwe ena amanena kuti linkatchulidwa mʼnjira zina. Mumpukutu wina wa ku Nyanja Yakufa womwe uli ndi mbali ya buku la Levitiko mʼChigiriki, anamasulira dzina la Mulungu kuti Iao. Kuwonjezera pa kalembedwe kameneka, olemba Baibulo a Chigiriki amanena kuti dzinali linkatchulidwanso kuti Iae, I·a·beʹ, komanso I·a·ou·eʹ. Komabe zoona zake nʼzakuti sitidziwa mmene atumiki a Mulungu akale ankatchulira dzinali mʼChiheberi. (Genesis 13:4; Ekisodo 3:15) Chomwe tikudziwa nʼchakuti Mulungu ankagwiritsa ntchito dzina lake mobwerezabwereza polankhula ndi anthu ake, anthuwo ankamutchula ndi dzina lake komanso ankaligwiritsa ntchito akamauza ena za iye.—Ekisodo 6:2; 1 Mafumu 8:23; Salimo 99:9.

Ndiye nʼchifukwa chiyani mʼBaibuloli analemba dzinali kuti “Yehova”? Nʼchifukwa chakuti mʼChichewa akhala akugwiritsa ntchito kalembedwe ka dzina la Mulungu kameneka kwa nthawi yaitali.

Dzina la Mulungu pa Genesis 15:2 mʼBaibulo limene William Tyndale anamasulira, mu 1530

William Tyndale ndi amene anayamba kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu mʼmabuku 5 oyambirira a Baibulo la Chingelezi lomwe analimasulira mʼchaka cha 1530. Iye anagwiritsa ntchito mawu akuti “Iehouah.” Patapita nthawi chilankhulo cha Chingelezi chinasintha zomwe zinachititsa kuti kalembedwe ka dzinalo kasinthe. Mwachitsanzo mʼchaka cha 1612, womasulira Baibulo wina dzina lake Henry Ainsworth anagwiritsa ntchito mawu akuti “Iehovah,” pomasulira buku la Masalimo. Kenako mʼchaka cha 1639, pamene buku lake linakonzedwanso nʼkusindikizidwa limodzi ndi mabuku 5 oyambirira a Baibulo, dzina lija lakuti “Iehouah,” linalowedwa mʼmalo ndi lakuti “Yehova.” Mu 1901, omasulira Baibulo la American Standard Version anagwiritsiranso ntchito dzina lakuti “Yehova” pamene pankapezeka dzinali mʼMalemba a Chiheberi.

Pofotokoza chifukwa chimene anagwiritsira ntchito dzina lakuti “Yehova” mʼmalo mwa “Yahweh,” katswiri wamaphunziro a Baibulo, dzina lake Joseph Bryant Rotherham ananena mʼbuku lake limene analemba mu 1911 kuti anasankha kutero “pofuna kugwiritsa ntchito mawu amene anthu owerenga Baibulo akuwadziwa.” (Studies in the Psalms) Mʼchaka cha 1930, katswiri winanso wamaphunziro a Baibulo dzina lake A. F. Kirkpatrick anafotokoza mfundo yofanana ndi imeneyi ponena za dzina lakuti “Yehova.” Iye anati: “Akatswiri oona za galamala amasiku ano amanena kuti dzinali linayenera kutchulidwa kuti Yahveh kapena Yahaveh; koma YEHOVA ndi katchulidwe kamene nʼkodziwika kwambiri mʼChingelezi ndipo chofunika kwambiri si katchulidwe kolondola ka dzinali koma chofunika nʼkudziwa kuti ndi dzina la Mulungu lenileni osati laulemu ngati lakuti ‘Ambuye.’”

Zilembo 4 Zoimira Dzina la Mulungu YHWH: “Amachititsa Kukhala”

Mneni HWH: “kukhala”

Kodi dzina loti Yehova limatanthauza chiyani? MʼChiheberi dzina lakuti Yehova linachokera ku mneni amene amatanthauza “kukhala,” ndipo akatswiri ambiri amaphunziro amaona kuti mawuwa mʼChiheberi amatanthauza chinthu chimene chimachititsa kuti chinachake chichitike. Choncho a mʼKomiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano anaona kuti dzina la Mulungu limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Akatswiri ali ndi maganizo osiyanasiyana okhudza tanthauzo la dzinali, ndipo sitinganene kuti maganizo awowo ndi olakwika. Komabe tanthauzo la dzina la Mulunguli ndi logwirizana ndi udindo wake monga Mlengi wa zinthu zonse komanso yemwe amakwaniritsa cholinga chake. Sikuti Mulungu anangolenga zinthu zakumwamba ndi dziko lapansi, koma iye akupitiriza kuchita zinthu pofuna kukwaniritsa cholinga chake ndiponso zimene amafuna.

Choncho dzina loti Yehova silimangotanthauza zimene zili pa Ekisodo 3:14 zakuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala” kapena “Ndidzakhala Amene Ndidzasankhe Kukhala.” Mawu amenewa satanthauzira mokwanira dzina la Mulungu. Mʼmalomwake akungosonyeza mmene Mulungu alili kuti amatha kukhala chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse cholinga chake. Choncho ngakhale kuti imeneyi ndi mbali ina ya tanthauzo la dzina la Mulungu lakuti Yehova, sikuti limangotanthauza kuti amasankha kukhala chilichonse chimene akufuna basi. Limatanthauzanso zimene amachita pogwiritsa ntchito zinthu zimene analenga kuti akwaniritse cholinga chake.