Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 17

Kodi Baibulo Lingathandize Bwanji Banja Lanu?

AMUNA/ABAMBO

“Mofanana ndi zimenezi, amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondera matupi awo. Mwamuna amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, chifukwa palibe munthu amene anadanapo ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda . . . Aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha.”

Aefeso 5:28, 29, 33

“Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.”

Aefeso 6:4

AKAZI

“Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”

Aefeso 5:33

“Inu akazi, muzigonjera amuna anu, chifukwa zimenezi ndi zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye.”

Akolose 3:18

ANA

“Ana inu, muzimvera makolo anu mogwirizana ndi zimene Ambuye amafuna, chifukwa kuchita zimenezi nʼkoyenera. ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’ Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Lonjezo lake ndi lakuti: ‘Kuti zinthu zikuyendereni bwino, ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.’”

Aefeso 6:1-3

“Ana inu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, chifukwa zimenezi zimasangalatsa Ambuye.”

Akolose 3:20