Salimo 46:1-11

  • “Mulungu ndi pothawira pathu”

    • Ntchito zodabwitsa za Mulungu (8)

    • Mulungu akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi (9)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Mogwirizana ndi kaimbidwe ka Alamoti.* Nyimbo. 46  Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu,+Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.+   Nʼchifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,Ndiponso ngakhale mapiri atagwera mʼnyanja yakuya nʼkumira,+   Ngakhale madzi amʼnyanjayo atawinduka nʼkuchita thovu,+Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha kuwinduka kwa nyanjayo. (Selah)   Pali mtsinje umene nthambi zake zimachititsa kuti anthu amumzinda wa Mulungu asangalale,+Chihema chachikulu chopatulika cha Wamʼmwambamwamba.   Mulungu ali mumzindawo+ ndipo sungagonjetsedwe. Mulungu adzauthandiza mʼbandakucha.+   Mitundu ya anthu inachita phokoso, maufumu anagonjetsedwa.Iye analankhula mokweza mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+   Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.* (Selah)   Bwerani mudzaone ntchito za Yehova,Mmene wachitira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.   Akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi.+ Wathyola uta ndi kupindapinda mkondo.Ndipo wawotcha pamoto magaleta ankhondo.* 10  “Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu. Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu,+Ndidzakwezedwa padziko lapansi.”+ 11  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.+ (Selah)

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Mabaibulo ena amati, “zishango.”