Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

A7-A

Zinthu Zikuluzikulu Zimene Yesu Anachita Ali Padziko Lapansi—Zimene Zinachitika Yesu Asanayambe Utumiki Wake

Zochitika za MʼMauthenga Abwino 4, Zondandalikidwa Motsatira Nthawi Imene Zinachitika

Matchati otsatirawa ali ndi mapu osonyeza mmene Yesu anayendera komanso malo omwe analalikirako. Zizindikiro zangati mivi pamapu, sizikusonyeza njira zenizeni zimene anadutsa koma zikungosonyeza madera amene anafikako. Chizindikiro cha “c.” chikutanthauza “cha mʼma.”

Zimene Zinachitika Yesu Asanayambe Utumiki Wake

NTHAWI

MALO

ZIMENE ZINACHITIKA

MATEYU

MALIKO

LUKA

YOHANE

3 B.C.E.

Yerusalemu, mʼkachisi

Mngelo Gabirieli anauza Zekariya za kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi

   

1:5-25

 

c. 2 B.C.E.

Nazareti; Yudeya

Mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti adzabereka Yesu; Mariya anapita kukaona Elizabeti

   

1:26-56

 

2 B.C.E.

Dera lakumapiri la Yudeya

Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi ndi kupatsidwa dzina; Zekariya analosera; Yohane azidzakhala mʼchipululu

   

1:57-80

 

2 B.C.E., mwina pa 1 Oct.

Betelehemu

Kubadwa kwa Yesu; “Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama”

1:1-25

 

2:1-7

1:1-5, 9-14

Pafupi ndi Betelehemu; Betelehemu

Mngelo anauza abusa nkhani yabwino; angelo anatamanda Mulungu; abusa anapita kukaona mwana

   

2:8-20

 

Betelehemu; Yerusalemu

Yesu anadulidwa (tsiku la 8); makolo ake anapita naye kukachisi (patatha masiku 40)

   

2:21-38

 

1 B.C.E. kapena 1 C.E.

Yerusalemu; Betelehemu; Iguputo; Nazareti

Okhulupirira nyenyezi anakaona Yesu; banja linathawira ku Iguputo; Herode anapha ana aamuna; banja linabwerera nʼkukhazikika ku Nazareti 2:1-23

2:1-23

 

2:39, 40

 

12 C.E., Pasika

Yerusalemu

Yesu ali ndi zaka 12 kukachisi akufunsa aphunzitsi

   

2:41-50

 
 

Nazareti

Anabwerera ku Nazareti; anapitiriza kumvera makolo ake; anaphunzira ukalipentala; Mariya anabereka ana ena 4 aamuna komanso ana aakazi (Mat. 13:55, 56; Maliko 6:3)

   

2:51, 52

 

29, kumayambiriro

Chipululu, Mtsinje wa Yorodano

Yohane Mʼbatizi anayamba utumiki wake

3:1-12

1:1-8

3:1-18

1:6-8, 15-28