Salimo 115:1-18

  • Ulemerero uyenera kuperekedwa kwa Mulungu yekha

    • Mafano opanda moyo (4-8)

    • Dziko lapansi linaperekedwa kwa anthu (16)

    • “Akufa satamanda Ya” (17)

115  Ife sitikuyenera, inu Yehova, ife sitikuyenera,Koma ulemerero ukuyenera kupita ku dzina lanu+Chifukwa cha kukhulupirika kwanu komanso chikondi chanu chokhulupirika.+   Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+   Mulungu wathu ali kumwamba.Iye amachita chilichonse chimene chamusangalatsa.   Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva komanso golide,Ntchito ya manja a anthu.+   Pakamwa ali napo koma sangalankhule.+Maso ali nawo koma sangaone.   Makutu ali nawo koma sangamve.Mphuno ali nayo koma sanganunkhize.   Manja ali nawo koma sakhudza kanthu.Mapazi ali nawo koma sangayende.+Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+   Anthu amene amawapanga adzafanana nawo,+Chimodzimodzinso anthu onse amene amakhulupirira mafanowo.+   Aisiraeli inu, khulupirirani Yehova,+Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.+ 10  Inu nyumba ya Aroni,+ khulupirirani Yehova,Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu. 11  Inu amene mumaopa Yehova, khulupirirani Yehova,+Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.+ 12  Yehova akutikumbukira ndipo adzatidalitsa.Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli.+Adzadalitsa nyumba ya Aroni. 13  Yehova adzadalitsa anthu onse amene amamuopa,Aangʼono ndi aakulu omwe. 14  Yehova adzakuchulukitsani,Inuyo komanso ana anu.*+ 15  Yehova akudalitseni,+Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+ 16  Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+ 17  Akufa satamanda Ya,+Ngakhalenso aliyense amene amatsikira kulichete.+ 18  Koma ife tidzatamanda YaKuyambira panopa mpaka kalekale. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anu aamuna.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.