Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 5

Kodi MʼBaibulo Muli Uthenga Wotani?

“Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, komanso pakati pa mbadwa yako ndi mbadwa yake. Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”

Genesis 3:​15

“Kudzera mwa mbadwa yako, mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.”

Genesis 22:18

“Ufumu wanu ubwere. Zofuna zanu zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.”

Mateyu 6:​10

“Mulungu amene amapereka mtendere aphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwapa.”

Aroma 16:20

“Zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzasonyeza kuti ali pansi pa ulamuliro wa Mulungu, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”

1 Akorinto 15:28

“Tsopano malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu ndi kwa mbadwa yake . . . , amene ndi Khristu. Ndiponso ngati muli ophunzira a Khristu, ndinudi mbadwa za Abulahamu.”

Agalatiya 3:​16, 29

“Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake ndipo iye adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.”

Chivumbulutso 11:15

“Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, imene imadziwika kuti Mdyerekezi komanso Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa padziko lapansi ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”

Chivumbulutso 12:9

“Kenako anagwira chinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana, nʼkumumanga kwa zaka 1,000.”

Chivumbulutso 20:2