Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 6

Kodi Baibulo Linaneneratu Zinthu Ziti Zokhudza Mesiya?

ULOSI

“Iwe Betelehemu Efurata, . . . mwa iwe mudzatuluka munthu amene ndidzamusankhe kuti akhale wolamulira mu Isiraeli.”

Mika 5:2

KUKWANIRITSIDWA KWAKE

“Yesu atabadwa ku Betelehemu wa ku Yudeya, pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Herode, okhulupirira nyenyezi ochokera Kumʼmawa anabwera ku Yerusalemu.”

Mateyu 2:1

ULOSI

“Iwo akugawana zovala zanga, ndipo akuchita maere pa zovala zanga.”

Salimo 22:18

KUKWANIRITSIDWA KWAKE

“Asilikaliwo atamukhomerera Yesu pamtengo, anatenga malaya ake akunja nʼkuwagawa zigawo 4. . . . Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anawombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi. Choncho iwo anakambirana kuti: ‘Malayawa tisawangʼambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.’ ”

Yohane 19:23, 24

ULOSI

“Amateteza mafupa onse a munthu wolungamayo. Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.”

Salimo 34:20

KUKWANIRITSIDWA KWAKE

“Atafika pa Yesu, anapeza kuti wafa kale ndiye sanamuthyole miyendo.”

Yohane 19:33

ULOSI

“Iye anabayidwa chifukwa cha zolakwa zathu.”

Yesaya 53:5

KUKWANIRITSIDWA KWAKE

“Mmodzi wa asilikaliwo anamubaya ndi mkondo munthiti ndipo nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi.”

Yohane 19:34

ULOSI

“Iwo anandilipira ndalama 30 zasiliva.”

Zekariya 11:12, 13

KUKWANIRITSIDWA KWAKE

“Kenako mmodzi wa ophunzira 12 aja, amene ankadziwika kuti Yudasi Isikariyoti, anapita kwa ansembe aakulu nʼkuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?” Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.”

Mateyu 26:14, 15; 27:5