Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 11

Kodi Chimachitika Nʼchiyani Munthu Akamwalira?

“Mpweya wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.”

Salimo 146:4

“Chifukwa amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse . . . Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, chifukwa ku Manda kumene ukupitako kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu kapena nzeru.”

Mlaliki 9:5, 10

“[Yesu] anauza ophunzira akewo kuti: ‘Mnzathu Lazaro ali mʼtulo, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa.’ Apa Yesu ankatanthauza kuti Lazaro wamwalira. Koma iwo ankaganiza kuti akunena za kugona tulo teniteni. Kenako Yesu anawauza mosapita mʼmbali kuti: ‘Lazaro wamwalira.’ ”

Yohane 11:11, 13, 14