Salimo 77:1-20

  • emphero la pa nthawi yamavuto

    • Kuganizira mozama ntchito za Mulungu (11, 12)

    • ‘Kodi pali mulungu winanso wamkulu amene angafanane ndi inu Mulungu?’ (13)

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.* Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 77  Ndidzafuulira Mulungu,Ndithu, ndidzafuulira Mulungu, ndipo iye adzandimvetsera.+   Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndimafunafuna Yehova.+ Usiku ndimakweza manja anga kwa iye ndipo sindisiya.* Palibe chimene chimanditonthoza.   Ndikakumbukira Mulungu ndimabuula.+Ndimavutika kwambiri mumtima ndipo mphamvu zanga zimatha.*+ (Selah)   Mumatsegula zikope zanga.Ndavutika mumtima, moti sindingathe kulankhula.   Ndikuganizira masiku akale,+Ndikuganizira zaka zakale kwambiri.   Usiku ndimakumbukira nyimbo yanga.*+Ndimaganiza mumtima mwanga,+Ndipo ndimafufuza mwakhama.   Kodi Yehova adzatitaya mpaka kalekale?+ Kodi sadzatisonyezanso kukoma mtima kwake?+   Kodi chikondi chake chokhulupirika chatha mpaka kalekale? Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa ku mibadwomibadwo?   Kodi Mulungu waiwala kusonyeza kukoma mtima kwake,+Kapena kodi mkwiyo wake wachititsa kuti chifundo chake chithe? (Selah) 10  Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundivutitsa* ndi zakuti:+ Wamʼmwambamwamba wasiya kutithandiza”? 11  Ndidzakumbukira ntchito za Ya,Ndidzakumbukira zochita zanu zodabwitsa zakale. 12  Ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zonse,Ndipo ndiziganizira mwakuya zochita zanu.+ 13  Inu Mulungu, njira zanu ndi zoyera. Kodi pali mulungu winanso wamkulu amene angafanane ndi inu Mulungu?+ 14  Inu ndinu Mulungu woona amene mumachita zinthu zodabwitsa.+ Mwasonyeza ku mitundu ya anthu kuti ndinu wamphamvu.+ 15  Ndi mphamvu zanu* mwapulumutsa* anthu anu,+Ana aamuna a Yakobo ndi a Yosefe. (Selah) 16  Madzi anakuonani, inu Mulungu,Madzi anakuonani ndipo anavutika.+ Ndipo madzi akuya anayamba kuvutika kwambiri. 17  Mitambo inagwetsa madzi. Mʼmitambo yakuda munamveka mabingu,Ndipo mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+ 18  Phokoso la bingu lanu+ linali ngati la mawilo a galeta.Kungʼanima kwa mphezi kunaunika padziko lapansi.+Dziko lapansi linanjenjemera komanso kugwedezeka.+ 19  Msewu wanu unadutsa panyanja,+Ndipo njira yanu inadutsa pamadzi ambiri.Koma palibe amene anatha kuzindikira mmene mapazi anu anaponda. 20  Munatsogolera anthu anu ngati nkhosa,+Kudzera mwa Mose ndi Aroni.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “sindichita dzanzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu wanga umakomoka.”
Kapena kuti, “nyimbo yoimbidwa ndi zingwe.”
Kapena kuti, “zikundilasa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwawombola.”