Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 16

Kodi Mungatani Kuti Musamade Nkhawa?

“Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuthandiza. Iye sadzalola kuti munthu wolungama agwe.”

Salimo 55:22

“Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino, koma onse amene amachita zinthu mopupuluma amasauka.”

Miyambo 21:5

“Usachite mantha, chifukwa ndili ndi iwe. Usade nkhawa chifukwa ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa, ndithu ndikuthandiza, ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.”

Yesaya 41:10

“Ndi ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pangʼono pokha chifukwa cha kuda nkhawa?”

Mateyu 6:27

“Musamadere nkhawa za mawa, chifukwa mawalo lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Mavuto a tsiku lililonse ndi okwanira pa tsikulo.”

Mateyu 6:34

“Muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri.”

Afilipi 1:10

“Musamade nkhawa ndi chinthu chilichonse. Mʼmalomwake, nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu, muzimuchonderera kuti azikutsogolerani pa chilichonse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu pamene mukutsatira Khristu Yesu.”

Afilipi 4:6, 7