Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 12

Kodi Akufa Adzakhalanso ndi Moyo?

“Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa nthawi ikubwera imene onse amene ali mʼmanda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.”

Yohane 5:​28, 29

“Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe.”

Machitidwe 24:15

“Ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inatambasulidwa. Koma panali mpukutu wina umene unatambasulidwa, womwe ndi mpukutu wa moyo. Akufa anaweruzidwa potengera zimene zinalembedwa mʼmipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo. Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Imfa komanso Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense payekha anaweruzidwa mogwirizana ndi ntchito zake.”

Chivumbulutso 20:12, 13