Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 9

Nʼchifukwa Chiyani Anthufe Timavutika?

“Si nthawi zonse pamene anthu othamanga kwambiri amapambana pampikisano komanso pamene amphamvu amapambana pankhondo. Si nthawi zonse pamene anthu ochenjera amapeza chakudya, ndiponso si nthawi zonse pamene anthu anzeru amakhala ndi chuma. Komanso anthu odziwa zinthu, si nthawi zonse pamene zinthu zimawayendera bwino, chifukwa nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”

Mlaliki 9:​11

“Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi ndipo uchimowo unabweretsa imfa. Choncho imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa . . .”

Aroma 5:​12

“Nʼchifukwa chake Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.”

1 Yohane 3:8

“Dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo.”

1 Yohane 5:​19