Salimo 10:1-18

  • Yehova amathandiza anthu ovutika

    • Anthu oipa amanena modzikuza kuti: “Kulibe Mulungu” (4)

    • Anthu ovutika amayangʼana kwa Yehova (14)

    • “Yehova ndi Mfumu mpaka muyaya” (16)

ל [Lamed] 10  Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali? Nʼchifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya mavuto?+   Modzikuza, munthu woipa amathamangitsa munthu wovutika,+Koma adzakodwa mumsampha wa ziwembu zake.+   Chifukwa munthu woipa amanena za zolinga zake* zadyera modzitamandira,+Ndipo amadalitsa munthu wadyera.נ [Nun]Iye amanyoza Yehova.   Chifukwa cha kudzikweza, munthu woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+   Zochita zake zikupitiriza kumuyendera bwino,+Koma zigamulo zanu sangathe kuzimvetsa.+Iye amanyogodola adani ake onse.   Mumtima mwake amanena kuti: “Sindidzagwedezeka.*Ku mibadwomibadwo,Tsoka silidzandigwera.”+ פ [Pe]   Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi kuopseza ena.+Pansi pa lilime lake pali mavuto ndi zopweteka ena.+   Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi.Amachoka pamene wabisalapo nʼkupha munthu wosalakwa.+ ע [Ayin] Maso ake akuyangʼanayangʼana munthu woti amuchite chiwembu.+   Amadikirira anthu pamalo amene iye amabisala ngati mkango umene uli pamalo ake amene umabisala.*+ Amadikirira kuti agwire munthu wovutika. Amagwira munthu wovutikayo pomukulunga ndi ukonde wake.+ 10  Munthu wovutikayo amaponderezedwa ndipo amawerama ndi chisoni.Anthu ovutikawo amagwidwa ndi dzanja lake lamphamvu. 11  Mumtima mwake amanena kuti: “Mulungu waiwala zoipa zimene ndimachita.+ Iye wayangʼana kumbali. Sakuona chilichonse.”+ ק [Qoph] 12  Nyamukani, inu Yehova.+ Inu Mulungu, chitanipo kanthu.+ Musaiwale anthu ovutika.+ 13  Nʼchifukwa chiyani munthu woipa wanyoza Mulungu? Mumtima mwake amanena kuti: “Simudzandiimba mlandu.” ר [Resh] 14  Koma inu mumaona mavuto ndi masautso. Mumayangʼana nʼkuchitapo kanthu.+ Munthu wovutika amayangʼana kwa inu,+Mumathandiza mwana wamasiye.+ ש [Shin] 15  Thyolani dzanja la munthu woipa ndi wankhanza,+Kuti mukamafufuza zoipa zakeMusazipezenso. 16  Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Mitundu ya anthu yawonongedwa, yachotsedwa padziko lapansi.+ ת [Taw] 17  Koma inu Yehova mudzamva pempho la anthu ofatsa.+ Mudzalimbitsa mitima yawo+ ndipo mudzawamvetsera mwatcheru.+ 18  Mudzaweruza mwachilungamo mwana wamasiye komanso anthu oponderezedwa,+Kuti munthu wamba wochokera kufumbi asadzawachititsenso mantha.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “za zokhumba za moyo wake.”
Kapena kuti, “Sindidzadzandira.”
Kapena kuti, “uli paziyangoyango.”