Salimo 104:1-35

  • Kutamanda Mulungu chifukwa cha zinthu zodabwitsa zimene analenga

    • Dziko lapansi lidzakhalapo kwamuyaya (5)

    • Vinyo komanso chakudya zimasangalatsa munthu (15)

    • “Ntchito zanu ndi zochuluka” (24)

    • “Mukachotsa mzimu wawo, zimafa” (29)

104  Moyo wanga utamande Yehova.+ Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri.+ Mwavala ulemu ndi ulemerero.+   Mwadzifunditsa kuwala+ ngati chofunda,Mwatambasula kumwamba ngati nsalu yopangira tenti.+   Iye amamanga zipinda zake pamadzi amumlengalenga+ pogwiritsa ntchito matabwa,Amapanga mitambo kukhala galeta lake,+Amayenda pamapiko a mphepo.+   Iye amachititsa kuti angelo ake akhale amphamvu,*Amachititsa atumiki ake kuti akhale moto wopsereza.+   Iye wakhazikitsa dziko lapansi pamaziko ake.+Silidzasunthidwa pamalo ake* mpaka kalekale.+   Munaliphimba ndi madzi ozama ngati kuti mwaliphimba ndi nsalu.+ Madziwo anakwera kupitirira mapiri.   Chifukwa cha kudzudzula kwanu, madziwo anathawa.+Atamva mabingu anu anayamba kuthawa mopanikizika kwambiri   Kupita kumalo amene munawakonzera.Mapiri anakwera+ ndipo zigwa zinatsika.   Munawaikira malire kuti asapitirire malirewo,+Kuti asadzamizenso dziko lapansi. 10  Amatulutsa madzi mu akasupe kuti apite mʼzigwa*Ndipo madziwo amadutsa pakati pa mapiri. 11  Akasupewo amapereka madzi kwa zilombo zonse zakutchire.Abulu amʼtchire amapha ludzu lawo mmenemo. 12  Mbalame zamumlengalenga zimamanga zisa zawo pafupi ndi akasupewo,Ndipo zimaimba mʼmitengo ya masamba ambiri. 13  Mulungu amathirira mapiri kuchokera mʼzipinda zake zamʼmwamba.+ Dziko lapansi ladzaza ndi zipatso za ntchito zanu.+ 14  Amameretsa msipu kuti ngʼombe zidye,Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke mʼnthaka 15  Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,+Mafuta amene amachititsa kuti nkhope ya munthu isalale,Ndiponso chakudya chimene chimapereka mphamvu kwa munthu.*+ 16  Mitengo ya Yehova imalandira madzi okwanira,Mikungudza ya ku Lebanoni imene iye anadzala, 17  Mbalame zimamanga zisa zawo mmenemo. Nyumba ya dokowe+ imakhala mʼmitengo ya junipa.* 18  Mʼmapiri aatali ndi mmene mumakhala mbuzi zamʼmapiri.+Ndipo mʼmapanga ndi mmene mbira zimathawiramo.+ 19  Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.Dzuwa limadziwa bwino nthawi yoyenera kulowa.+ 20  Mumabweretsa mdima ndipo usiku umayamba,+Nthawi imene nyama zonse zakutchire zimayendayenda. 21  Mikango yamphamvu* imabangula pofunafuna nyama,+Ndipo imapempha chakudya kwa Mulungu.+ 22  Dzuwa likatuluka,Nyamazi zimachoka ndipo zimakagona mʼmalo amene zimakhala. 23  Munthu amapita kuntchito yake,Ndipo amagwira ntchito mpaka madzulo. 24  Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+ Zonsezo munazipanga mwanzeru.+ Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga. 25  Pali nyanja, yomwe ndi yakuya komanso yaikulu kwambiri,Mmene muli zamoyo zosawerengeka, zazikulu ndi zazingʼono zomwe.+ 26  Sitima zimayenda mmenemo,Ndipo Leviyatani*+ munamupanga kuti azisewera mmenemo. 27  Zonsezi zimayembekezera inuKuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.+ 28  Zimasonkhanitsa zimene mwazipatsa.+ Mukatambasula dzanja lanu, zimakhutira ndi zinthu zabwino.+ 29  Mukabisa nkhope yanu, zimasokonezeka. Mukachotsa mzimu wawo,* zimafa ndipo zimabwerera kufumbi.+ 30  Mukatumiza mzimu wanu zimalengedwa,+Ndipo mumachititsa kuti zinthu zonse padziko lapansi zikhale zatsopano. 31  Ulemerero wa Yehova udzakhalapobe mpaka kalekale. Yehova adzakondwera ndi ntchito zake.+ 32  Amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+ 33  Ndidzaimbira Yehova+ moyo wanga wonse.Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.+ 34  Zimene ndimaganiza zizimusangalatsa. Ine ndidzasangalala chifukwa cha Yehova. 35  Ochimwa adzachotsedwa padziko lapansi,Ndipo oipa sadzakhalaponso.+ Moyo wanga utamande Yehova. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye amapanga angelo ake kukhala mizimu.”
Kapena kuti, “Silidzagwedezeka.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wa munthu.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Kapena kuti, “Mikango yamphamvu yamanyenje.”
Kapena kuti, “mpweya wawo; mphamvu ya moyo wawo.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.