Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 7

Kodi Baibulo Linaneneratu Zinthu Ziti Zokhudza Masiku Ano?

“Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina . . . Zonsezi ndi chiyambi cha mavuto aakulu.”

Mateyu 24:​7, 8

“Kudzakhala aneneri ambiri abodza ndipo adzasocheretsa anthu ambiri. Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.”

Mateyu 24:11, 12

“Mukadzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo, musadzachite mantha. Zimenezi zikuyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.”

Maliko 13:7

“Kudzachitika zivomerezi zamphamvu ndipo kudzakhala miliri ndi njala mʼmalo osiyanasiyana. Kudzaoneka zinthu zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.”

Luka 21:11

“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi ena, onenera ena zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, ochitira anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.”

2 Timoteyo 3:​1-5