Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 14

Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama?

“Munthu amene amakonda zosangalatsa adzasauka. Amene amakonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.”

Miyambo 21:17

“Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsa.”

Miyambo 22:7

“Ndi ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi nʼkuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo? Akapanda kutero, angayale maziko koma osatha kuimaliza ndipo onse oona angayambe kumuseka nʼkumanena kuti: ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma zamukanika kumaliza.’”

Luka 14:28-30

“Anthu onsewo atakhuta, iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.’”

Yohane 6:12