Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

B1

Uthenga wa MʼBaibulo

Yehova Mulungu ndi amene ali woyenera kulamulira ndipo ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndi anthu chidzakwaniritsidwa.

Chaka cha 4026 B.C.E. Chitadutsa

“Njoka” inakayikira zoti Yehova ndi wolamulira wabwino. Yehova analonjeza kuti padzakhala “mbadwa ” kapena “mbewu” imene mʼkupita kwa nthawi idzaphwanya mutu wa njoka yomwe ndi Satana. (Genesis 3:1-5, 15, mawu amʼmunsi) Komabe Yehova walola kuti anthu adzilamulire motsogoleredwa ndi mphamvu ya “njoka.”

Mu 1943 B.C.E.

Yehova anauza Abulahamu kuti “mbadwa” yolonjezedwa idzachokera mwa ana ake.—Genesis 22:18.

Chaka cha 1070 B.C.E. Chitadutsa

Yehova anatsimikizira Mfumu Davide, kenako anatsimikiziranso mwana wake Solomo, kuti “mbadwa” yolonjezedwayo idzachokera mʼbanja lake.—2 Samueli 7:12, 16; 1 Mafumu 9:3-5; Yesaya 9:6, 7.

Mu 29 C.E.

Yehova anasankha Yesu kukhala “mbadwa” yolonjezedwa kuti adzakhale pampando wachifumu wa Davide.—Agalatiya 3:16; Luka 1:31-33; 3:21, 22.

Mu 33 C.E.

Pofuna kulepheretsa kuti pasakhale “mbadwa” yolonjezedwa, Satana, yemwe ndi njoka, anapha Yesu. Koma Yehova anaukitsa Yesu yemwe kenako anapita kumwamba. Kumeneko Yehova analandira moyo wangwiro wa Yesu, womwe umathandiza kuti anthu azitha kukhululukidwa machimo ndiponso kuti mbadwa za Adamu zidzalandire moyo wosatha.—Genesis 3:15; Machitidwe 2:32-36; 1 Akorinto 15:21, 22.

Cha mʼma 1914 C.E.

Yesu anaponya njoka, yemwe ndi Satana, padziko lapansi kuti akhalepo kwa kanthawi kochepa.—Chivumbulutso 12:7-9, 12.

Mʼtsogolo

Yesu adzamanga Satana kwa zaka 1,000, kenako adzamuwononga, zomwe zikuimira kuphwanya mutu wa Satana. Ndiyeno cholinga choyambirira cha Yehova chokhudza dziko lapansi ndi anthu chidzakwaniritsidwa. Dzina lake lidzayeretsedwa ndipo zimenezi zidzasonyeza kuti iye ndi woyenera kulamulira.—Chivumbulutso 20:1-3, 10; 21:3, 4.