Pitani ku nkhani yake

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu? (Gawo 1)

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu? (Gawo 1)

 Kodi mukudziwa wachinyamata aliyense amene akuvutika ndi matenda aakulu? Kodi inuyo muli ndi matenda aakulu kapena ndinu wolumala ndipo mumalephera kusangalala ndi zinthu zimene achinyamata anzanu amasangalala nazo?

 Ngati zili choncho, n’zachibadwa ngati nthawi zina mumakhumudwa. Komabe, pali mfundo ziwiri za m’Baibulo zolimbikitsa kwambiri.

  •   Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wanu, akudziwa mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Kuwonjezera pamenepa, iye “amakuderani nkhawa.”​—1 Petulo 5:7.

  •   Yehova Mulungu ali ndi cholinga chothetsa matenda onse. Mungawerenge zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi palemba la Yesaya 33:24 komanso la Chivumbulutso 21:​1-4.

 Achinyamata ambirimbiri omwe akuvutika ndi matenda kapena kulumala amakwanitsa kupirira chifukwa chokhulupirira Mulungu pamodzi ndi malonjezo ake. Taonani zitsanzo 4 zotsatirazi.

 YEIMY

 Pamene ndinkafika zaka 11 n’kuti nditayamba kale kuyenda panjinga ya olumala. Ndimalephera kugwira ntchito ina iliyonse, ngakhale kunyamula zinthu zing’onozing’ono.

 Ndili ndi zaka 5, madokotala anandipeza ndi matenda enaake amene amafooketsa kwambiri thupi. Nthawi zina ndimakhumudwa kwambiri chifukwa sinditha kuchita zinthu zimene ana a msinkhu wangawu amachita. Komabe, makolo anga ndiponso anthu a mumpingo mwathu amandithandiza, kundilimbikitsa kuti ndiziiwalako vuto langali komanso amandithandiza kuti nthawi zonse ubwenzi wanga ndi Yehova uzikhala wolimba. Ndimagwira ntchito yolalikira uthenga wabwino nthawi zonse ndipo nthawi zambiri Akhristu anzanga amayenda nane tikamakaphunzitsa anthu Baibulo.

 Yesu ananena kuti tsiku lililonse lili ndi zinthu zake zodetsa nkhawa. (Mateyu 6:34) Choncho ndimayesetsa kupewa kudera nkhawa kwambiri zinthu zamawa. Komanso ndimasankha kuchita zinthu zimene ndikudziwa kuti ndikwanitsadi. Ndikuyembekezera mwachidwi dziko latsopano limene Mulungu walonjeza, lomwe tidzasangalale ndi “moyo weniweniwo” popanda matenda amene akundisowetsa mtenderewa.​—1 Timoteyo 6:19.

Zoti Muganizire: Yeimy amaona kuti zimamuyendera bwino chifukwa ‘amasankha kuchita zinthu zokhazo zimene angakwanitse.’ Kodi inuyo mungamutsanzire bwanji?​—1 Akorinto 9:26.

 MATTEO

 Msana wanga unayamba kundivuta ndili ndi zaka 6. Poyamba madokotala ankati palibe vuto koma changokhala chizindikiro chakuti ndikukula. Koma patapita chaka, madokotala anadzazindikira kuti ndili ndi chotupa mumsana.

 Ndinachitidwa opaleshoni, koma dokotalayo anakwanitsa kuchotsa mbali yochepa chabe ya chotupacho. Patangopita miyezi iwiri, chotupacho chinakulanso ngati mmene chinalili poyamba. Kungoyambira nthawi imeneyo, madokotala akhala akundiunika maulendo ambirimbiri ndiponso kundipatsa chithandizo maulendo ambirimbiri, koma zonse sizinaphule kanthu.

 Nthawi zina chotupacho chimachititsa kuti ndizimva ululu wokhala ngati ndikubaidwa ndi mpeni m’thupi lonse, makamaka mumsana ndi m’chifuwa. Komabe, ndimayesetsa kuti ndisamangokhalira kudandaula za vuto langali. Ndimayesetsa kuganizira zoti anthu enanso anapirira mavuto oopsa kuposa vuto langali, ndipo iwo sankangokhalira kudandaula. Chinthu china chofunika kwambiri chimene chimandithandiza kuti ndisamandaule n’chakuti sindikayikira zakuti tsiku lina Yehova Mulungu adzakwaniritsa zimene analonjeza zoti adzathetsa mavuto onse.​—Chivumbulutso 21:4.

Zoti Muganizire: Kodi kuganizira zoti Mulungu adzathetsa mavuto onse kungakuthandizeni bwanji kupirira, ngati mmene kwathandizira Matteo?​—Yesaya 65:17.

 BRUNA

 Popeza matenda anga alibe zizindikiro zoonekera, anthu amaganiza kuti ndine waulesi. Komatu si dala. Ndimavutika kuchita chilichonse, kaya kugwira ntchito, kuphunzira ngakhalenso kudzuka pabedi.

 Pamene ndinali ndi zaka 16, ndinapezeka ndi matenda enaake aakulu omwe amandivutitsa kwambiri. Matendawa amachititsa kuti ndizivutika kugwira ntchito, kupita kumisonkhano yachikhristu komanso kulalikira. Nthawi zambiri ndimawerenga lemba la 1 Petulo 5:​7, lomwe limati: ‘Mumutulireni Mulungu nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ Ndimalimbikitsidwa ndikaganizira mfundo yakuti Yehova amadera nkhawa komanso kusamalira munthu aliyense payekha. Mfundo imeneyi ikundilimbikitsabe mpaka lero.

Zoti Muganizire: Kodi kum’tulira Yehova nkhawa zanu kungakuthandizeni bwanji, ngati mmene Bruna amachitira?​—Salimo 55:22.

 ANDRÉ

 Anthu ena amangonditenga ngati kamwana ka zaka 10. Koma palibe kanthu, poti ndi mmene ndimaonekera.

 Pamene ndinali ndi zaka ziwiri, madokotala anandipeza ndi matenda a khansa inayake yomwe sipezekapezeka. Khansayo inayamba mumsana kenako inakafika mubongo. Madokotala anayesetsa kundithandiza kuti nthendayo isapitirire kukula, koma chithandizo chomwe ankandipatsacho chinachititsa kuti ndisamakule bwinobwino. Ndine wamtali mamita 1.37 okha ndipo ndimangooneka ngati kamwana moti anthu ambiri sakhulupirira ndikawauza kuti ndili ndi zaka 18.

 Koma mumpingo wachikhristu anthu amandisonyeza ulemu. Mosiyana ndi anzanga akusukulu, Akhristuwo samandinyoza kapena kundichitira zinthu ngati ndine mwana. Nanenso ndimayesetsa kuti ndisamangokhalira kudandaula za vuto langali. Ndimasangalala kwambiri podziwa kuti chinthu chabwino kwambiri chimene munthu aliyense ayenera kuyesetsa kuti achipeze, ineyo ndinachipeza. Chinthu chimenechi n’kudziwa Yehova. Ndimadziwa kuti pavuto lililonse limene ndingafunike kulipirira, Yehova alipo ndipo andithandiza. Komanso kuganizira za madalitso abwino kwambiri amene tidzasangalala nawo m’dziko latsopano limene Yehova Mulungu watilonjeza kumandithandiza kuti ndisamangokhalira kudandaula za matenda angawa.​—Yesaya 33:24.

Zoti Muganizire: Mogwirizana ndi zimene André ananena, n’chifukwa chiyani ‘kudziwa Yehova n’chinthu chabwino kwambiri chimene munthu aliyense ayenera kuyesetsa kuti achipeze’?​—Yohane 17:3.