Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yomwa Mowa?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yomwa Mowa?

Baibulo silimaletsa kumwa mowa pang’ono ngati malamulo akuvomereza kutero. Komabe limaletsa kuledzera.—Salimo 104:15; 1 Akorinto 6:10.

Kodi mungatani ngati mukukakamizidwa kuti mumwe pamene malamulo kapena makolo anu sakukulolani?

 Ganizirani zimene zingachitike pambuyo pomwa mowa

Anzanu ena angaganize kuti kumwa mowa n’kofunika kuti munthu asangalale. Koma kodi chingachitike n’chiyani pambuyo pomwa mowa?

  • Kuphwanya malamulo. Potengera kumene mumakhala, ngati mutamwa mowa pamene malamulo sakukulolani kutero, mukhoza kulipira chindapusa, kuimbidwa mlandu, kulandidwa laisensi yoyendetsera galimoto, kupatsidwa chilango chogwira ntchito zosiyanasiyana m’dera lanu, kapena kutsekeredwa m’ndende kumene.—Aroma 13:3.

  • Kuononga mbiri. Mowa umapangitsa munthu kuyamba kuchita zinthu mopanda manyazi. Chifukwa cha mowa, munthu akhoza kunena kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake akhoza kunong’oneza nazo bondo. (Miy. 23:31-33) Masiku ano zipangizo zamakono zachuluka kwambiri, choncho zomwe mungachite zingafalikire mosavuta ndipo zikhoza kukhudza mbiri yanu kwa nthawi yayitali.

  • Kulephera kudziteteza. Kumwa mowa kungachititse kuti anthu ena akuchitireni nkhanza mosavuta komanso kukugwiririrani. Kungachititsenso kuti muzingoyendera maganizo a anzanu zimene zingakuikeni m’mavuto kapena kuchita zinthu zosemphana ndi malamulo.

  • Kukonda kwambiri mowa. Kafukufuku wina akusonyeza kuti munthu akayamba kumwa mowa ali wamng’ono kwambiri, n’zosavuta kuti azidalira kwambiri mowa akafuna kuchita zinthu. Kumwa mowa n’cholinga chofuna kuthana ndi kupanikizika maganizo, kusungulumwa kapena kuboweka ndi zinazake, kumayambitsa chizolowezi chimene kumakhala kovuta kwambiri kuchisiya.

  • Imfa. M’chaka china posachedwapa, munthu mmodzi ankafa pamaminitsi 52 aliwonse m’dziko la United States pangozi zochitika chifukwa choyendetsa galimoto munthu atamwa mowa. Nthawi inayake chaka chilichonse achinyamata oposa 1,500 osapitirira zaka 21 ankafa pangozi za galimoto chifukwa chomwa mowa. Izi zinachitika kwa zaka 5 zotsatizana. Ngakhale kuti inuyo simunamwe mowa, mukhoza kuika moyo wanu pangozi ngati mutakwera galimoto imene woyendetsa wake wamwa mowa.

 Sankhani zochita

Mukhoza kupewa zinthu zoopsa zomwe zingachitike chifukwa chomwa mowa mosayenera ngati mutasankhiratu zimene mukufuna kuchita.

Mfundo ya M’Baibulo: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Ndi kupanda nzeru kumwa mowa kenako n’kumayendetsa galimoto kapena kuchita zina zake zimene zimafuna kuti munthu azichite akuganiza bwinobwino.

Chosankha: ‘Ndingamwe mowa pokhapokha ngati kuchita zimenezi sikukuphwanya malamulo komanso pamene zinthu zili bwino.’

Mfundo ya M’Baibulo: ‘Mumakhala akapolo a amene mumamumvera.’ (Aroma 6:16) Ngati mukumwa mowa chifukwa chakuti anzanu akumwa, ndiye kuti mukulola anzanuwo kuti azikusankhirani zochita. Ngati mukumwa mowa n’cholinga chofuna kuthana ndi kupanikizika kapena kuboweka, ndiye kuti simukudziphunzitsa luso lotha kulimbana ndi mavuto bwinobwino.

Chosankha: ‘Sindingalole kumwa mowa chifukwa choti anzanga akundikakamiza.’

Mfundo ya M’Baibulo: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.” (Miyambo 23:20) Ngati anzanu ndi amakhalidwe oipa, sangamalemekeze zimene mwasankha. N’zosavuta kuyamba kumwa kwambiri mowa mukakhala ndi anzanu omwe ndi zidakwa.

Chosankha: ‘Anthu omwe amamwa mowa mwauchidakwa sangakhale anzanga apamtima.’