Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika?

 Kodi mumaona kuti ndinu munthu wotani?

  • Wosangalala

    “Ndimayesetsa kuti ndizikhala wosangalala ngakhale zinthu zitakhala kuti sizikundiyendera kwenikweni. Tsiku lililonse ndimapeza chifukwa chondipangitsa kukhala wosasangalala.”—Valerie.

  • Wongokhalira kudandaula

    “Ndikamva nkhani inayake yabwino, m’malo mosangalala ndimafulumira kuganiza kuti sizingankhale zoona.”—Rebecca.

  • Wovomereza Mmene Zinthu Zilili

    “Munthu ukakhala kuti nthawi zonse umayembekezera kuti zinthu ziyenda bwino umakhumudwa zikapanda kukuyendera bwino. Komanso ukakhala womangokhalira kudandaula moyo umaumva kuwawa. Ine ndimaona kuti bola kukhala munthu wovomereza mmene zinthu zilili pa nthawiyo chifukwa zimandithandiza kuti ndizisangalala poyenera kusangalala komanso kukhumudwa pa zifukwa zomveka.”—Anna.

 Kodi kupewa kumangoganizira zolakwika n’kofunika bwanji?

Baibulo limanena kuti “munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.” (Miyambo 15:15) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene amapewa kumangoganizira zolakwika ndipo amayesetsa kuona zinthu moyenera, amakhala osangalala. Nthawi zambiri amakhalanso ndi anzawo ambiri ocheza nawo. Ndipotu palibe amene angasangalale kumacheza ndi munthu amene nthawi zambiri amakhala wokhumudwa kapena wodandaula.

Komabe mavuto salephera ngakhale kwa anthu amene nthawi zambiri amakhala osangalala ndipo amaona kuti zawo ziyenda bwino basi. Mwachitsanzo:

  • Mungamade nkhawa mukamvera nkhani zokhudza nkhondo, zauchigawenga kapenanso zokhudza kuphwanya malamulo.

  • Mwina mukukumana ndi mavuto m’banja mwanu.

  • N’kuthekanso kuti muli ndi zofooka zanu zomwe mukulimbana nazo.

  • Mwinanso mnzanu wina anakuchitirani kapena kukulankhulani zinthu zokhumudwitsa.

M’malo mongonyalanyaza mavuto ngati amenewa kapenanso kumawaganizira kwambiri mpaka kufika pokusokonezani, mungachite bwino kudziikira malire. Kuona zinthu moyenera kukhoza kukuthandizani kupewa kumangoganizira zinthu zolakwika n’kuvomereza kuti ndi mmene moyo ulili.

Munthu umatha kupirira mphepo ya mkuntho chifukwa choti sukukayikira kuti pakapita nthawi isiya ndipo dzuwa liwalanso

 Zimene mungachite

  • Musamakokomeze kapena kunyalanyaza zomwe mumalakwitsa.

    Baibulo limanena kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlaliki 7:20) Munthu aliyense amalakwitsa kapena kulephera zinazake, ndipo zimenezi sizitanthauza kuti ndinu wolephera.

    Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Yesetsani kulimbana ndi mavuto anuwo koma musayembekezere kuti mukhoza kumachita bwino pa chilichonse. Mnyamata wina dzina lake Caleb ananena kuti: “M’malo moganizira kwambiri za zinthu zomwe ndimalakwitsa, ndimayesetsa kuphunzirapo kanthu n’kuona zimene ndingachite kuti ndizichita bwino.”

  • Musamadziyerekezere ndi anthu ena

    Baibulo limanena kuti: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.” (Agalatiya 5:26) Nthawi zina mukhoza kukhumudwa kuona zinthuzi zimene anzanu akutumizirana zosonyeza kuti anali kuphwando kapena kwinakwake kokasangalala koma inuyo sanakuitaneni. Zimenezi zingachititse kuti muyambe kuwaona anzanuwo ngati adani anu.

    Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Muzidziwa kuti anzanu sangakuitanireni ku zochitika zilizonse. Komanso zithunzi zimene anthu amaika pa intaneti kapena kutumizira m’mafoni sizimasonyeza zonse zokhudza mmene zinthu zinalilidi. Mtsikana wina dzina lake Alexis ananena kuti: “Pa intaneti anthu amaikapo zithunzi zobeba zokhazokha kuti ena asirire. Nthawi zambiri zithunzi zosonyeza zinthu zina zosasangalatsa zomwe zinachitika samaziikapo.”

  • Muziyesetsa kukhala mwamtendere, makamaka ndi anthu a m’banja lanu.

    Baibulo limanena kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:18) N’zoona kuti simungathe kusintha zimene anthu ena amachita, koma inuyo mukhoza kusintha mmene mumachitira zinthu ena akakuchitirani zinazake. Mukhoza kusankha kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu.

    Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: M’malo mowonjezera mavuto m’banja lanu, muziyesetsa kukhala mwamtendere ngati mmene mungachitire ndi mnzanu wina aliyense. Mtsikana wina dzina lake Melinda ananena kuti: “Palibe amene salakwitsa zinthu, ndipo tonsefe nthawi zina tikhoza kukhumudwitsa anzathu. Timangofunika kusankha kuti tipangapo chiyani, tichita zinthu mwamtendere kapena ayi.”

  • Muzikhala ndi mtima woyamikira.

    Baibulo limanena kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akolose 3:15) Mtima woyamikira ungakuthandizeni kuti muziona zinthu zomwe zikuyenda bwino pa moyo wanu m’malo momangoganizira zinthu zomwe sizikuyenda bwino.

    Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Muzidziwa mavuto anu, koma zimenezi zisakuchititseni kuiwala zabwino zomwe mumachita. Mtsikana wina dzina lake Rebecca ananena kuti: “Tsiku lililonse ndimalemba m’kabuku kanga chinthu chabwino chimodzi chomwe chachitika. Zimenezi zimandithandiza kudziwa kuti ngakhale ndili ndi mavuto, palinso zabwino zambiri zoti n’kuziganizira.”

  • Muzisamala ndi anthu ocheza nawo.

    Baibulo limanena kuti: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Ngati anthu omwe mumakonda kucheza nawo amakonda kulankhula zolakwika, zokayikitsa kapena zokhumudwitsa, nanunso mukhoza kutengera zomwezo.

    Mungatani kuti muziona zinthu moyenera: Ngati anzanu akumana ndi mavuto omwe akuwachititsa kukhala osasangalala, muziwathandiza. Koma mavuto a anzanuwo asamakusokonezeni. Mtsikana wina dzina lake Michelle ananena kuti: “Tisamacheze kwambiri ndi anthu amene amakonda kuona zinthu molakwika. Kucheza kwambiri ndi anthu otere kungangowonjezera mavuto athu.”

 Werengani nkhani zina zomwe zingakuthandizeni

Baibulo limanena kuti tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Kodi nanunso nthawi zina mumalephera kukhala wosangalala chifukwa choti m’dzikoli muli mavuto ambiri? Ngati ndi choncho, werengani nkhani yakuti “N’chifukwa Chiyani Panopa Timakumana ndi Mavuto Ambiri?