Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Kuti Ndizikonda Masewera Olimbitsa Thupi?

Ndingatani Kuti Ndizikonda Masewera Olimbitsa Thupi?

 N’chifukwa chiyani ndiyenera kuchita masewera olimbitsa thupi?

 M’mayiko ena, achinyamata sakonda kuchita masewera olimbitsa thupi ndipo zimenezi zimaika thanzi lawo pangozi. Mpake kuti Baibulo limatilangiza kuti “kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Taganizirani mfundo zotsatirazi:

  •   Masewera olimbitsa thupi angakuchititseni kuti muzisangalala. Tikamachita masewerawa, thupi lathu limatulutsa timadzi tinatake tomwe timachititsa kuti tizikhala osangalala komanso tizimva bwino. Mpake kuti anthu ena amati masewera olimbitsa thupi ndi mankhwala ochepetsera nkhawa.

     “Ndikayamba ndi kuthamanga m’mamawa, tsiku langa limandiyendera bwino kwambiri. Ndimaona kuti ndimakhala wosangalala.”—Regina.

  •   Masewera olimbitsa thupi angakuthandizeni kuti mukhale athanzi. Kuchita masewera olimbitsa thupi moyenera kungachititse kuti mukhale amphamvu, athanzi komanso kuti musamadziderere.

     “Ndimamva bwino ndikachita masewera ozendewera chinachake. Ndimadzipititsa m’mwamba n’kudzitsitsa pansi maulendo 10 tsiku lililonse. Chaka chatha sindinkakwanitsa ngakhale ulendo umodzi. Koma chomwe chikundisangalatsa kwambiri n’choti ndikuyesetsa kusamalira thanzi langa.”—Olivia.

  •   Masewera olimbitsa thupi akhoza kutalikitsa moyo wanu. Thupi lanu likakhala lomasuka, mtima wanu komanso kapumidwe kanu, zimagwira ntchito bwino. Mukamachita masewera olimbitsa thupi ojowajowa, zingakuthandizeni kuti musamadwale matenda a mtima omwe amapha anthu ambiri, amuna ndi akazi omwe.

     “Tikakhala ndi ndandanda yabwino yochitira masewera olimbitsa thupi, timasonyeza kuyamikira thupi limene Mlengi wathu anatipatsa.”—Jessica.

 Mfundo yofunika kwambiri: Masewera olimbitsa thupi angakuthandizeni kuti mudzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo, ndipotu angakuthandizeni ngakhale panopa. Mtsikana wina dzina lake Tonya ananena kuti: “Ukachita masewera enaake olimbitsa thupi, umaona kuti sunataye nthawi yako. Ine ndimati ndikasiya ntchito zanga n’kuchita masewera olimbitsa thupi, sindimanong’oneza bondo.”

Mukamainyalanyaza galimoto yanu ikhoza kuwonongekeratu, n’chimodzimodzinso ngati mutanyalanyaza kuchita masewera olimbitsa thupi, thanzi lanu lingakhale pangozi

 Kodi chikundilepheretsa n’chiyani?

 Pali zambiri zomwe zingakulepheretseni kuti muzichita masewera olimbitsa thupi, monga:

  •   Kusaona kufunika kwake. “Ukakhala wamng’ono umangoganiza kuti zonse zili bwino. Sumaganiza n’komwe kuti nthawi ina ungadzakumane ndi mavuto okhudza thanzi. Umaona kuti mavuto okhudza thanzi ndi a anthu akuluakulu.”—Sophia.

  •   Kusowa nthawi. “Popeza ndimakhala otanganidwa, ndimafunika kupatula nthawi yokonza chakudya chabwino komanso yogona. Koma kuti ndipeze nthawi yochita masewera olimbitsa thupi, zimandivuta kwambiri.”—Clarissa.

  •   Kusowa ndalama yolipirira malo ochitirako masewerawa. “Ngati ukufuna kuti uzipita kumalo ochitira masewera olimbitsa thupi, umafunika kulipira ndipo ndalama zake zimakhala zambiri.”—Gina.

 Zoti muganizire:

 Kodi ndi vuto lalikulu liti lomwe limakulepheretsani kuchita masewera olimbitsa thupi? N’zoona kuti sizophweka kuthetsa vutolo, komabe zotsatirapo zake zimakhala zabwino.

 Ndingatani kuti ndizikwanitsa kuchita masewera olimbitsa thupi?

 Taonani zina mwa mfundo zomwe zingakuthandizeni:

  •   Muzikumbukira kuti ndi udindo wanu kusamalira thanzi lanu.—Agalatiya 6:5.

  •   Musamasinthesinthe maganizo. (Mlaliki 11:4) Mwachitsanzo, m’malo modikira kuti mukalipire kaye kwinakwake kochitira masewera olimbitsa thupi, mukhoza kungopeza masewera enaake omwe amakusangalatsani oti mukhoza kumachitira kunyumba kwanu, ndipo musamaphonye nthawi yochitira masewerawo.

  •   Muzifunsa nzeru kwa ena, kuti mudziwe zomwe amachita kuti azilimbitsa thupi lawo.—Miyambo 20:18.

  •   Muzikhala ndi ndandanda ya zomwe mukufuna kukwaniritsa ndipo muzilemba zomwe zatheka.—Miyambo 21:5.

  •   Pezani mnzanu woti muzichita naye masewera olimbitsa thupi. Mnzanuyo akhoza kumakulimbikitsani komanso kukuthandiza kuti muzitsatira ndandanda yanu.—Mlaliki 4:9, 10.

  •   Muziyembekezera kuti padzakhala mavuto ena ndi ena, ndipo zimenezi zisadzakugwetseni ulesi.—Miyambo 24:10.

 Muzikhala ndi malire

 Baibulo limanena kuti amuna komanso akazi asamachite zinthu “mopitirira malire.” (1 Timoteyo 3:2, 11) Choncho, muzidziikira malire pochita masewera olimbitsa thupi. Nthawi zambiri anthu amene amachita masewerawa mowonjeza, sapindula chilichonse. Mtsikana wina dzina lake Julia ananena kuti: “Mnyamata amene amangoganizira zoti azioneka wamasozi kwambiri koma alibe nzeru, samandisangalatsa.”

 Muzisamalanso ndi malangizo a anthu amene amalimbikitsa kuti muzichita masewera olimbitsa thupi modzipha. Zimenezi zikhoza kukuvulazani ndiponso kukuchititsani kuiwala kuti “zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

 Ndipotu zinthu zina zomwe cholinga chake n’kukulimbikitsani, zikhoza kukukhumudwitsani. Mtsikana wina dzina lake Vera ananena kuti: “Atsikana ambiri amasunga zithunzi za anthu omwe maonekedwe awo amawasangalatsa n’cholinga choti ziziwalimbikitsa kupangabe masewerawa mpaka atafika pooneka ngati anthuwo. Koma akaona kuti sakufikapo, amakhumudwa. Ndi bwino kuti cholinga cha masewera olimbitsa thupi chizikhala kusamalira thanzi, osati kusintha mmene umaonekera.”