Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndimakonda Kuvala Zovala Zotani?

Kodi Ndimakonda Kuvala Zovala Zotani?

N’chifukwa chiyani muyenera kusamala ndi zovala zimene mumakonda kuvala? Chifukwa chake ndi choti zovala zimene mumavala zimanena zambiri za inuyo. Ndiye kodi anthu angaganize zotani ataona zovala zimene inuyo mumavala?

 Maganizo olakwika amene anthu amakhala nawo pa nkhani ya mafasho

1: Ndikhoza kumangotengera mafasho a pa TV ndiponso pa Intaneti.

Mtsikana wina dzina lake Theresa anati: “Nthawi zina ndimakopeka ndi zovala zinazake ndikaona pa TV kapena pa Intaneti zovala zimene amalonda akutsatsa. Ndiye ukazolowera kuona malonda amenewa, zimakulowa m’mutu moti nawenso umayamba kuona kuti zovalazo ndi zabwino.”

Si atsikana okha amene amakumana ndi vutoli. Buku lina linanena kuti: “Nawonso anyamata amakopeka kwambiri akaona malonda a zovala pa TV kapena pa Intaneti. Ndiye popeza otsatsa malonda anatulukira zimenezi, amayesetsa kuwakopa ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa anyamata aang’ono.”—The Everything Guide to Raising Adolescent Boys

Zimene mungachite: Baibulo limati: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Mungachite bwino kumachita zimene lembali likunena. Musamangokhulupirira chilichonse chimene amalonda amanena. Mwachitsanzo, ngati akutsatsa chovala chinachake n’kumanena kuti muzioneka wokopa komanso wokongola kwambiri mukavala chovalacho, mungachite bwino kudzifunsa kuti:

  • ‘Kodi ndi ndani amene angapinduledi ndikagula chovalachi?’

  • ‘Kodi ndikavala chovala chimenechi, anthu aziganiza kuti ndine munthu wolongosoka?’

  • ‘Kodi chovalacho chipangitsa anthu kumaganiza kuti ndine munthu wa khalidwe lotani?’

Mfundo imene ingakuthandizeni: Kwa mlungu umodzi, mumvetsere komanso kuonera malonda onena za zovala zomwe zangotuluka kumene. Kenako dzifunseni kuti, ‘Kodi amene akutsatsa malondawo akulimbikitsa anthu kukhala ndi moyo wotani? Kodi akugwiritsa ntchito mawu okopa n’cholinga choti muziona kuti mukufunika kugula chovalacho basi?’ Mtsikana wina dzina lake Karen anati: “Wachinyamata aliyense amafuna kuti azioneka bwino komanso kuti anthu ena azimugomera. Ndiye popeza otsatsa malonda amazindikira zimenezi, cholinga chawo chimakhala kukopa achinyamata kuti azingogula chovala chilichonse chomwe chatuluka.”

2: Ndikhoza kumavala chovala chilichonse chimene chalowa mufasho kuti ndisaoneke wotsalira.

Mnyamata wina dzina lake Manuel anati: “Zimakhala zosavuta kuyamba kuvala zovala zinazake ukaona kuti anthu ambiri akuvala zovala zomwezo. Ngati utakhala kuti wekhawekha ukamavala zovala zachikale, anthu amayamba kukunena.” Mtsikana wina dzina lake Anna ananenanso zomwezi. Anati: “Ambiri amavala zovala zomwe zili mufasho n’cholinga choti azioneka ofanana ndi ena.”

Zimene mungachite: Baibulo limati: “Musamatengere nzeru za nthawi ino.” (Aroma 12:2) Nanunso mungachite bwino kuyesetsa kutsatira malangizo amenewa. Choncho onaninso zovala zimene muli nazo n’kudzifunsa kuti:

  • ‘Kodi ndimayang’ana chiyani ndikamagula zovala zanga?’

  • ‘Kodi ndimakonda kugula zovala zopangidwa ndi kampani inayake, moti chilichonse chimene kampaniyo yatulutsa ndimachiona kuti ndi chabwino?’

  • ‘Kodi ndikufuna kuti anthu azigoma akaona mmene ndimavalira?’

Mfundo imene ingakuthandizeni: M’malo momangoganiza kuti pali zovala za mitundu iwiri basi, zomwe zili mufasho komanso zomwe zatuluka mufasho, mungachite bwino kudziwa kuti pali zovala zinanso zabwino zomwe zingachititse kuti anthu azikupatsani ulemu. Kuzindikira mfundo imeneyi kungakuthandizeni kuti musamangovala zovala zomwe zafala n’cholinga choti anthu azikuonani kuti ndinu wozindikira.

3: Ndikufuna kuti maso a anthu asamachoke pa ine.

Mtsikana wina dzina lake Jennifer anati: “Kunena zoona, nthawi zina ndimafuna nditavala zovala zazifupi kapena zothina.”

Zimene mungachite: Baibulo limati: “Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwakunja, . . . Koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima.” (1 Petulo 3:3, 4) Mogwirizana ndi mfundoyi, taganizirani izi: Kodi chingakhale chokopa kwambiri n’chiyani pakati pa kuvala zovala zoti anthu azingokucheukira ndi kukhala munthu wamakhalidwe abwino?

Mfundo imene ingakuthandizeni: Chinthu chimene chingachititse kuti anthu azikopeka nanu komanso kukulemekezani ndi kuvala zovala zoyenera. N’zoona kuti anthu ambiri sangagwirizane ndi mawu amenewa. Komabe taganizirani izi:

Kodi munayamba mwachezapo ndi munthu amene amangokhalira kudzichemerera komanso kunena za iyeyo? N’kutheka kuti zimenezo zinakukwanani kwambiri, chifukwa ankakhala ngati akuona kuti inuyo si wofunika kwenikweni.

Mofanana ndi kucheza, munthu amene amavala zovala zokopa ena, amakhala ngati munthu amene amangokhalira kudzichemerera moti anthu amafika potopa naye n’kumusiya

Ndiye mukamavala zovala zokopa anthu ena, mumakhala ngati munthu ameneyu. Zovala zanu zimakhala zikuuza anthu kuti, “Muziyang’ana ine.” Zimenezi zingachititse kuti anthu ena aziona kuti ndinu wodzikonda. Zingachititsenso kuti athu ena akuchitireni zachipongwe kapena aziganiza kuti mukuwakopa kuti mukhale nawo pachibwenzi kapena mugone nawo.

Munthu sumatsatsa chinthu chimene sukugulitsa. Ndiye m’malo movala zovala zokopa anthu ena, mungachite bwino kumavala modzilemekeza. Mtsikana wina dzina lake Monica anati: “Sikuti kuvala modzilemekeza kumatanthauza kuti uzivala ngati agogo ako. Koma kumangotanthauza kuvala zovala zoti anthu akakuona, asamachite manyazi.”