Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?

Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?

 N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kofunika?

  •   Nthawi ili ngati ndalama. Ikatayika, imakhala kuti yataika basi siibwereranso. Komabe mukaigawa bwino, mukhoza kutsala ndi mpata wokwanira wochitira zinthu zomwe zimakusangalatsani.

     Lemba lothandiza: “Waulesi amalakalaka zinthu, chonsecho moyo wake ulibe chilichonse. Koma anthu akhama adzanenepa.”​—Miyambo 13:4.

     Mfundo yofunika kwambiri: Mukamagwiritsa ntchito nthawi yanu moyenera, mumakhala ndi ufulu wambiri wochitira zinthu zina.

  •   Kudziwa kugwiritsa ntchito bwino nthawi ndi luso lapadera lomwe lingadzakuthandizeni mukadzakula. Lusoli lingadzakuthandizeni kuti muzikhalitsa mukalembedwa ntchito. Ndiponso ngati mumapanga bizinezi, kodi mungapitirize kukhalabe ndi wantchito yemwe nthawi zonse amafika mochedwa pantchito?

     Lemba lothandiza: “Munthu wokhulupirika pa chinthu chaching’ono alinso wokhulupirika pa chinthu chachikulu.”​—Luka 16:10.

     Mfundo yofunika kwambiri. Mmene mumagawira nthawi yanu, zimathandiza anthu kudziwa kuti ndinu munthu wotani.

 Komabe sikuti kugawa bwino nthawi n’kophweka. Tiyeni tione mavuto ochepa omwe amakhalapo.

 Vuto loyamba: Anzanu

 Cynthia ananena kuti: “Nthawi zonse anzanga akandiuza kuti tipite kwinakwake tikacheze, ndimayesetsa kuti ndisalephere ngakhale nditakhala kuti ndili ndi zochita zina. Ndimangoti, ‘Ntchito zinazi ndikangozigwira mwapatalipatali ndikafika kunyumba.’ Koma zotsatira zake palibe chimene chimayenda.”

 Vuto lachiwiri: Zosokoneza

 Ivy ananena kuti: “TV ikhoza kukuwonongetsa nthawi chifukwa nthawi zina amaonetsa mafilimu komanso zinthu zina zabwino moti umalephera kuugwira mtima.”

 Marie ananena kuti: “Ndimawononga nthawi yambiri ndikuseweretsa tabuleti ndipo ndimaisiya pokhapokha batire lithe moto. Ndimadzimvera chisoni bwanji.”

 Vuto lachitatu: Kuchita zinthu mozengereza

 Beth ananena kuti: “Nthawi zina ndimangogwa ulesi kulemba homuweki kapena kumalizitsa zinazake zofunika. Ndimangotanganidwa ndi zinthu zosafunika ndipo pamapeto pake ndimadzipanikiza kuti ndimalizitse homuweki. Ndimalephera kugawa bwino nthawi yanga.”

Mukamagawa bwino nthawi yanu simukhala wopanikizika koma m’pamene mumakhala womasuka kwambiri

 Zimene mungachite

  1.   Lembani ntchito zomwe mukufunika kugwira. Mukhoza kulemba ntchito zapakhomo zomwe mukufunika kugwira komanso homuweki. Lembaninso kuchuluka kwa nthawi yomwe mungafunike pa wiki, kuti mumalize ntchitozi.

     Lemba lothandiza: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

  2.   Lembani zinthu zomwe mumakonda kuchita pa nthawi yanu yopuma. Zikhoza kukhala zinthu monga kucheza ndi anzanu pa intaneti kapena kuonera TV. Ndiyeno lembaninso kuchuluka kwa nthawi yomwe mumawononga pa wiki, mukuchita zinthuzi.

     Lemba lothandiza: “Pitirizani kuyenda mwanzeru . . . , ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”​—Akolose 4:5.

  3.   Konzani pulogalamu. Mukaona zomwe mwalemba pa 1 ndi 2, kodi nthawi yanu yambiri mwaiika pa zinthu zofunika? Kapena mukufunika kuchotserako pa nthawi yomwe mumachita zosangalatsa?

     Zimene zingakuthandizeni: Tsiku lililonse muzilemba pulogalamu ya zimene mukufuna kuchita ndipo muzichonga chomwe chatheka.

     Lemba lothandiza: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”​—Miyambo 21:5.

  4.   Muzitsatira pulogalamu yanu. Kuti mupeze nthawi yochitira zinthu zina, mungafunike kuti nthawi zina muzikana anzanu akakupemphani kuti mukacheze kapena kukapezeka paphwando linalake. Ndipotu pamapeto pake mudzaona kuti muli ndi nthawi yambiri ndipo simungakhale wopanikizika.

     Lemba lothandiza: “Musakhale aulesi pa ntchito yanu.”​—Aroma 12:11.

  5.   Pezani nthawi yosangalalako koma musaithamangire. Mtsikana wina dzina lake Tara ananena kuti: “Nthawi zina ndikamaliza zinthu ziwiri zomwe zili pa pulogalamu yanga, ndimati, ‘Eya, ndionereko TV kwa 15 minitsi yokha kenako ndikamalizitsa kwatsalaku.’ Koma ndimapezeka kuti ndakomedwa, m’malo mwa 15 minitsi, ndimakhala 30 minitsi mpaka nthawi imangopita. Ndikamazindikira, ndimakhala nditawononga maola awiri ndikuonera TV.”

     Mmene mungathetsere vutoli: Muziona kuti zosangalatsa zili ngati zinthu zongowonjezera zomwe mungachite mukamapuma, pambuyo poti mwamaliza ntchito zofunika kwambiri patsikulo.

     Lemba lothandiza: “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa . . . kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.”​—Mlaliki 2:24.