Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndine Munthu Wodalirika?

Kodi Ndine Munthu Wodalirika?

 Sankhani zogwirizana ndi inuyo

  •  Kodi ndimachita zinthu . . . nthawi zonse, nthawi zambiri, nthawi zina, kapenanso sindichita

    •  moona mtima

    •  pa nthawi yake

    •  mwakhama

    •  mwadongosolo

    •  m’njira yothandiza

    •  moganizira ena

    •  mwaulemu

    •  mwachikondi

  •   Pa makhalidwe amenewa, kodi ndi khalidwe liti limene mumachita bwino kwambiri?

     Pitirizani kuchita bwino pa khalidwe limenelo.—Afilipi 3:16.

  •   Nanga ndi khalidwe liti limene mukufunikira kuyesetsa kwambiri kuti mukhale nalo?

 Mfundo zotsatirazi zikuthandizani kuti muyesetse kukhala ndi khalidwe limenelo.

 Kodi munthu wodalirika amakhala wotani?

 Munthu wodalirika amachita zinthu zimene akufunika kuchita kaya ndi panyumba, kusukulu ngakhalenso m’dera limene akukhala. Munthu wodalirika amadziwanso kuti zochita zake zingakhudze ena komanso iyeyo. Choncho akalakwitsa zinthu, amavomereza, amapepesa komanso amayesetsa kuti akonze zimene analakwitsazo.

 Baibulo limati: “Pakuti aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”—Agalatiya 6:5.

 N’chifukwa chiyani ndiyenera kuyesetsa kuti ndikhale wodalirika?

 Munthu wodalirika amachita zinthu mwanzeru ndipo anthu amamulemekeza, amamuona kuti ndi woganiza bwino komanso amamulola kuchita zinthu zina zimene achinyamata ena sangaloledwe kuchita.

 Baibulo limati: “Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu.”—Miyambo 22:29.

Munthu wodalirika nthawi zambiri amakhala wowolowa manja ndipo amakhala ndi anzake odalirikanso.

 Baibulo limati: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.”—Luka 6:38.

Munthu wodalirika amasangalala chifukwa chokwanitsa kuchita zinthu, ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamadzikayikire.

 Baibulo limati: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake.”—Agalatiya 6:4.

 Kodi ndingatani kuti ndikhale munthu wodalirika kwambiri?

 Kuti musavutike kuyankha funsoli, taonani mawu otsatirawa amene achinyamata anzanu ananena. Kodi ndi mawu ati amene akufotokoza bwino mmene inuyo mumamvera?

 “Zimakhala zokhumudwitsa kwambiri akamakutenga ngati mwana wamng’ono yemwe sangachoke pakhomo ngakhale kwa nthawi yochepa. Ndikangochoka pakhomo ngakhale kwa ola limodzi lokha, Bambo ndi Mayi amayembekezera kuti ndiwaimbire foni n’kuwadziwitsa kumene ndili.”—Kerri.

 “Nthawi zambiri makolo anga amandilola mosavuta ndikawapempha kuti ndipite koyenda ndi anzanga.”—Richard.

 “Ndikaona achinyamata a msinkhu wangawu akuchita zinthu zinazake, ndimadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani makolo anga amandikaniza kuchita zimenezi?’”—Anne.

 “Makolo anga nthawi zambiri amandilola kuchita zimene ndikufuna. Ndimawayamikira kwambiri chifukwa chondipatsa ufulu umenewu.”—Marina.

 Mfundo yoona: Achinyamata ena amapatsidwa ufulu wambiri kuposa anzawo ena. N’chiyani chimene chimachititsa kuti pakhale kusiyana kumeneku?

 Zimene zimachititsa: Kuti mupatsidwe ufulu wochulukirapo, nthawi zambiri zimadaliranso kuti mukhale munthu wodalirika kwambiri.

 Mwachitsanzo, taonani zimene ananena achinyamata awiri omwe tawatchula chakumayambiriro.

 Richard: “M’mbuyomu, makolo anga ankandikayikira kuti sindingachite zinthu moyenera ngati atandipatsa ufulu wambiri. Koma panopa amandikhulupirira chifukwa ndimagwiritsa ntchito moyenera ufulu umene amandipatsa. Ndimawauza zoona zokhazokha ponena za kumene ndikupita komanso anthu amene ndikuyenda nawo. Ndipotu ndimachita kuwauza ndekha makolo anga zimene ndikufuna kuchita asanandifunse n’komwe.”

 Marina: “Pa moyo wanga wonse, makolo anga ndinawanamiza maulendo awiri, ndipo anadziwa kuti ndikunama pa nthawi ziwiri zonsezo. Kungoyambira nthawi imeneyo, ndimayesetsa kuwauza zoona zokhazokha. Mwachitsanzo, ndimawauza mosawabisira kalikonse pa nkhani ya zimene ndikuchita, komanso ndikapita koyenda ndi anzanga, ndimawaimbira foni n’kuwadziwitsa zimene ndikuchita. Zimenezi zachititsa kuti ayambe kundikhulupirira kwambiri.”

Kodi mumayamba kuchita zinthu ziti pakati pa ntchito zapakhomo ndi kuchita zosangalatsa?

 Kodi inuyo mukufuna makolo anu atamakupatsani ufulu wambiri ngati mmene zilili ndi Richard komanso Marina? Ngati zili choncho, onaninso bwinobwino mmene mumachitira zinthu pa mbali zotsatirazi:

 KUNYUMBA KWANU

  • Kodi mumagwira mokhulupirika mpaka kumaliza ntchito imene makolo anu akupatsani?

  •   Kodi nthawi zonse mumatsatira lamulo limene makolo anu anakupatsani loti muzifika pakhomo kunja kusanade?

  •   Kodi mumalemekeza makolo anu komanso abale anu?

 Kodi ndi mfundo iti pa mfundo zimenezi, ngati ilipo, imene mukuona kuti mukufunika kuyesetsa kusintha kuti muzichita bwino zinthu?

 Baibulo limati: “Muzimvera makolo anu.”—Aefeso 6:1.

 SUKULU

  • Kodi mumalemba ndi kumaliza homuweki yanu pa nthawi yake?

  •   Kodi mukuyesetsa kuchita khama kuti muzikhoza bwino kusukulu?

  •   Kodi mumawerenga mwakhama nthawi zonse?

 Kodi ndi mfundo iti pa mfundo zimenezi, ngati ilipo, imene mukuona kuti mukufunika kuyesetsa kusintha kuti muzichita bwino zinthu?

 Baibulo limati: “Nzeru zimateteza.” (Mlaliki 7:12) Maphunziro abwino angakuthandizeni kuti mukhale ndi nzeru.

 MBIRI YANU

  • Kodi mumachita zinthu moona mtima ndi makolo anu komanso anthu ena?

  •   Kodi mungathe kugwiritsa ntchito ndalama mwanzeru?

  •   Kodi mbiri yanu ikusonyeza kuti ndinu munthu wodalirika?

 Kodi ndi mfundo iti pa mfundo zimenezi, ngati ilipo, imene mukuona kuti mukufunika kuyesetsa kusintha kuti muzichita bwino zinthu?

 Baibulo limati: ‘Valani umunthu watsopano.’ (Aefeso 4:24) Mungakwanitse kusintha khalidwe lanu kuti mbiri yanu ikhale yabwino.

 Mungachite izi: Onani mbali imene mukufunika kusintha kuti muzichita zinthu m’njira yabwino kwambiri. Ndiyeno funsani malangizo kwa anthu amene mukuona kuti amachita bwino pa mbali imeneyo. Lembani mfundo zofunika zimene mukufuna kutsatira kuti musinthe pa mbaliyo, ndipo mwezi uliwonse muziona zimene mwachita potsatira mfundozo. Kenako lembani mfundo zimene mwachita bwino pozitsatira komanso zimene zakuvutani kuzitsatira. Mwezi ukatha, onaninso zimene mwachita potsatira mfundozo.