Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?

Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?

“Ndimaona anzanga ena akubwera m’kalasi popanda kunyamula makope, kenako amangomvetsera nyimbo uku aphunzitsi akuphunzitsa. Koma akalephera mayeso amadandaula. Ndiye pali anthu ena ngati ineyo, amene amawerenga mwawafawafa, koma mayeso akabwera amalephera. Sindikudziwa kuti zimenezi zimachitika chifukwa chiyani. Zimakhala zopweteka kwambiri kulephera mayeso pambuyo poti wakhala mawiki ambiri ukuchezera kuwerenga.”—Yolanda.

Kodi nanunso mumamva ngati Yolanda? Kunena zoona kulephera m’kalasi kumakhala kowawa kwambiri.

Achinyamata ena amene amalephera kusukulu, amafika potaya mtima ndipo amasiya kulimbikira m’kalasi. Pomwe ena amafika posiya sukulu. Mwina mungaone kuti njira yabwino ndi kusiya kulimbikira kapena kusiya sukulu, koma pali njira yabwino kwambiri yothetsera vuto limeneli. Tiyeni tikambirane mfundo 6 zimene zingakuthandizeni kuti muzikhoza bwino m’kalasi.

 Zimene mungachite

  • Muzipezeka m’kalasi. Mfundo imeneyi ingaoneke ngati yosathandiza, koma mukamathawa m’kalasi mukhoza kumangolephera.

    “Kusukulu kwathu, ana amene amathawa m’kalasi alibe nazo ntchito ngati atalephera ndipo siziwayendera bwino.”—Matthew.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Agalatiya 6:7.

  • Musamalole kuti zinthu zizikupitani m’kalasi. Kungopezeka m’kalasi ndi poyambira pabwino. Koma mukakhala m’kalasimo, muziyesetsa kuti zinthu zisamakupiteni. Ndi bwinonso kumalemba notsi. Ndipo muzimvetsetsa zimene aphunzitsi akunena. Ngati n’zololeka, muzifunsa mafunso m’kalasi.

    “Ndimakonda kufunsa mafunso ambiri m’kalasi chifukwa ndimaona kuti aphunzitsi amafotokoza bwino zinthu akazindikira kuti wophunzira wina sakumvetsa.”—Olivia.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.”—Luka 8:18.

  • Musamabere Mayeso. Kubera mayeso ndi chinyengo. Ndipo anthu kusukulu amabera mayeso m’njira zosiyanasiyana. Ena amangokopera zimene anzawo alemba. Kuchita zimenezi ndi chinyengo ndipo sikungakuthandizeni ngakhale pang’ono.

    “Ngati simukumvetsa zinthu zina, musamangokopera mayankho amene anzanu alemba. Kubera mayeso sikungakuthandizeni ngakhale pang’ono. Tikutero chifukwa chakuti m’malo moti muphunzire kuthana ndi mavuto panokha, mumazolowera kudalira anthu ena.”—Jonathan.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake.”—Agalatiya 6:4.

  • Muzilemberatu homuweki mukangofika kunyumba. Ngati n’kotheka muzilemberatu homuweki musanayambe kupuma kapena kuchita zinthu zina. a Mukatero, mukhoza kupeza mpata wochita zinthu zina momasuka.

    “Ndinkalemberatu homuweki yanga, ndipo izi zinathandiza kuti ndizikhoza bwino kusukulu. Ndikafika kunyumba ndinkalakalaka kugona kapena kumvetsera nyimbo. Koma ndinkayesetsa kumaliza kaye homuweki yanga kenaka n’kumapuma.”—Calvin.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

  • Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Musamachite manyazi kupempha ena kuti akuthandizeni. Mwachitsanzo, mukhoza kupempha malangizo kwa makolo anu. Mungapemphenso aphunzitsi anu kuti akuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muzikhoza m’kalasi. Nthawi zina mukhoza kupemphanso anthu amene amakuphunzitsani patitayimu kuti akuthandizeni.

    “Muzipita kukakumana ndi aphunzitsi anu. Muziwapempha kuti akuthandizeni kumvetsa zimene amaphunzitsa komanso kuti muzikhoza bwino m’kalasi. Aphunzitsiwo adzasangalala kwambiri kumva kuti mukuchita bwino m’kalasi ndipo adzakuthandizani.”—David.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Aphungu akachuluka [zolingalira] zimakwaniritsidwa.”—Miyambo 15:22.

  • Muzigwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene ulipo. M’mayiko ena, mayeso amakhala ndi mafunso owonjezera amene angathandize kuti mukhoze bwino. Mukhoza kudziperekanso kuti mupange ma pulojekiti ena amene angathandize kuti mukhoze bwino. Ngati mwalephera mayeso, mukhoza kupempha aphunzitsi anu kuti mulembenso.

    Kuyesetsa kuti muzikhoza m’kalasi kuli ngati kuphunzira kuimba gitala. Munthu akachita khama, zimamuyendera bwino.

    “Ngati ndikufuna kukhoza bwino phunziro linalake, ndimapempha aphunzitsi ngati pali pulojekiti inayake yoti ndipange kapena ngati ndingalembenso mayesowo.”—Mackenzie.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.

a Kuti mupeze mfundo zina zokuthandizani mukamawerenga, onani nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa . . . Ndingatani Kuti Ndimalize Homuweki yanga?