Wolembedwa ndi Mateyu 6:1-34

  • ULALIKI WAPAPHIRI (1-34)

    • Muzipewa kudzionetsera kuti ndinu olungama (1-4)

    • Mmene tingapempherere (5-15)

      • Pemphero la chitsanzo (9-13)

    • Kusala kudya (16-18)

    • Chuma padziko lapansi komanso kumwamba (19-24)

    • Siyani kuda nkhawa (25-34)

      • Nthawi zonse muziika Ufumu pamalo oyamba (33)

6  “Samalani kuti musamachite zinthu zachilungamo pamaso pa anthu nʼcholinga choti akuoneni.+ Mukamachita zimenezi simudzalandira mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba.  Choncho mukamapereka mphatso zachifundo,* musamalize lipenga ngati mmene amachitira anthu achinyengo mʼmasunagoge ndi mʼmisewu nʼcholinga choti anthu awatamande. Ndithu ndikukuuzani, anthu amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.  Koma iwe ukamapereka mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita,  kuti mphatso zako zachifundo zikhale zachinsinsi. Ukatero Atate wako amene akuona zimene zikuchitika ngakhale kuti iweyo sungathe kuwaona, adzakubwezera.+  Komanso mukamapemphera, musamachite zimene anthu achinyengo amachita.+ Chifukwa iwo amakonda kuima mʼmasunagoge ndi mumphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona.+ Ndithu ndikukuuzani, anthu amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.  Koma iwe ukamapemphera, uzilowa mʼchipinda chako nʼkutseka chitseko ndipo uzipemphera kwa Atate wako amene sungathe kuwaona.+ Ukatero Atate wako amene akuona zimene zikuchitika ngakhale kuti iweyo sungathe kuwaona, adzakubwezera.  Ukamapemphera, usamanene mawu omweomwewo mobwerezabwereza ngati mmene anthu a mitundu ina amachitira. Iwo amaganiza kuti Mulungu awamvetsera akanena mawu ambirimbiri.  Choncho inu musakhale ngati iwowo, chifukwa Atate wanu amadziwa zimene mukufunikira+ musanamupemphe nʼkomwe.  Koma inu muzipemphera chonchi:+ ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu+ liyeretsedwe.*+ 10  Ufumu wanu ubwere.+ Zofuna zanu+ zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.+ 11  Mutipatse chakudya chimene* tikufunikira lero.+ 12  Mutikhululukire zolakwa* zathu chifukwa ifenso takhululukira amene atilakwira.*+ 13  Tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa,*+ koma mutiteteze kwa woipayo.’+ 14  Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani.+ 15  Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukiraninso machimo anu.+ 16  Mukamasala kudya,+ siyani kuonetsa nkhope yachisoni ngati mmene anthu achinyengo aja amachitira. Iwo sasamalira nkhope* zawo kuti anthu ena adziwe kuti akusala kudya.+ Ndithu ndikukuuzani, anthu amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 17  Koma iwe ukamasala kudya, uzisukusula nkhope yako komanso kupaka mafuta mʼmutu mwako, 18  kuti anthu ena asadziwe kuti ukusala kudya, koma Atate wako wokha amene sungathe kuwaona. Ukatero Atate wako amene akuona zimene zikuchitika ngakhale kuti iweyo sungathe kuwaona, adzakubwezera. 19  Siyani kudziunjikira chuma padziko lapansi,+ pomwe njenjete* komanso dzimbiri zimawononga ndiponso pomwe akuba amathyola nʼkuba. 20  Koma unjikani chuma chanu kumwamba,+ kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge+ ndiponso kumene akuba sangathyole nʼkuba. 21  Chifukwa kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhalanso komweko. 22  Nyale ya thupi ndi diso.+ Choncho ngati diso lako likuyangʼana* pachinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala kwambiri. 23  Koma ngati diso lako lili ladyera,*+ thupi lako lonse lidzachita mdima. Choncho ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi wandiweyani! 24  Kapolo sangatumikire ambuye awiri, chifukwa akhoza kudana ndi mmodzi nʼkukonda winayo,+ kapena angakhale wokhulupirika kwa mmodzi nʼkunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.+ 25  Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Siyani kudera nkhawa za moyo wanu,+ kuti mudzadya chiyani kapena kuti mudzamwa chiyani kapenanso kudera nkhawa za matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo si wofunika kwambiri kuposa chakudya ndipo kodi thupi si lofunika kwambiri kuposa chovala?+ 26  Yangʼanitsitsani mbalame zamumlengalenga,+ pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola kapenanso kusunga chakudya mʼnyumba zosungiramo zinthu. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame? 27  Ndi ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pangʼono pokha* chifukwa cha kuda nkhawa?+ 28  Komanso nʼchifukwa chiyani mukudera nkhawa nkhani ya zovala? Phunzirani mmene maluwa akutchire amakulira. Sagwira ntchito ndiponso sawomba nsalu. 29  Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo+ mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. 30  Ndiye ngati Mulungu amaveka chonchi zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha mawa nʼkuzisonkheza pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo achikhulupiriro chochepa inu? 31  Choncho musamade nkhawa+ nʼkumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapenanso, ‘Tivala chiyani?’+ 32  Chifukwa anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi. 33  Choncho nthawi zonse muziika Ufumu ndi mfundo zolungama za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.+ 34  Musamadere nkhawa za mawa,+ chifukwa mawalo lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Mavuto a tsiku lililonse ndi okwanira pa tsikulo.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “lizionedwa kuti ndi lopatulika; lizionedwa kuti ndi loyera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate umene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngongole.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ali nafe ngongole.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Musatilowetse mʼmayesero.”
Kapena kuti, “amasiya kudzisamalira.”
Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
Mʼchilankhulo choyambirira, “likulunjika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “loipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.