Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandilola Kupita Kokasangalala?

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandilola Kupita Kokasangalala?

Taganizirani zotsatirazi:

Mukufuna kupita kokasangalala koma mukukayikira ngati makolo anu angakuloleni. Kodi mungasankhe kuchita chiyani?

  1.  OSAPEMPHA, KUNGOPITA

  2.  OSAPEMPHA, OSAPITA

  3.  KUPEMPHA N’KUONA ZOMWE AYANKHE

 1. OSAPEMPHA, KUNGOPITA

 Cholinga chanu: Kugometsa anzanu powasonyeza kuti palibe aliyense amene amakuuzani zochita. Mukuona kuti mumadziwa zambiri kuposa makolo anu, ndipo mumaona kuti makolo anu saganiza bwino.—Miyambo 14:18.

 Zotsatira zake: Anzanu angaone kuti inuyo ndi wochangamuka, komabe angaonenso kuti mumachita zinthu mwachiphamaso. Angaone kuti ngati mumapusitsa makolo anu, ndiye kuti mutha kuwapusitsanso iwowo. Ngati makolo anu atadziwa, angakhumudwe kwambiri ndipo angaone kuti mwawapusitsa, ndipo mwina akhoza kukupatsani chilango.—Miyambo 12:15.

 2. OSAPEMPHA, OSAPITA

 Cholinga chanu: Mukuganizira zimene zikachitike kokasangalalako ndipo mukuona kuti sizikugwirizana ndi mfundo zimene mumayendera, kapena mukuona kuti anthu ena amene aitanidwa si amakhalidwe abwino. (1 Akorinto 15:33; Afilipi 4:8) Kapena mukufuna kupita, koma mukuopa kupempha makolo anu.

 Zotsatira zake: Ngati simukufuna kupita chifukwa chakuti mukuona kuti si bwino kutero, mungawayankhe anzanuwo molimba mtima. Koma ngati simukufuna kupita chifukwa chakuti mukuopa kupempha makolo anu, mukhoza kungokhala ndwii panyumba n’kumadzimvera chisoni kuti anzanu onse akusangalala kupatulapo inu nokha.

 3. KUPEMPHA N’KUONA ZOMWE AYANKHE

 Cholinga chanu: Mukudziwa kuti makolo anu ali ndi udindo wokuuzani zochita ndipo mumaona kuti zimene amanena n’zothandiza. (Akolose 3:20) Mumakonda makolo anu ndipo simukufuna kuwakhumudwitsa pochita zinthu mwamseri. (Miyambo 10:1) Komanso kupempha kungakupatseni mpata wofotokoza bwinobwino maganizo anu.

 Zotsatira zake: Makolo anu adzaona kuti mumawakonda komanso mumawalemekeza. Ndipo ngati ataona kuti pempho lanu ndi lomveka, akhoza kukulolezani kupita.

N’chifukwa Chiyani Makolo Angakukanizeni?

Mofanana ndi anthu opulumutsa anzawo pangozi, makolo anu amadziwa zambiri zimene zingathe kukuvulazani

 Chifukwa choyamba tingachiyerekezere motere: Mutakhala kuti mukusambira m’nyanja, mwachidziwikire mungakonde kusambira pamalo pamene pali anthu amene amateteza anthu omwe akusambira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti pamene inuyo mukusambira m’madzi simungathe kuona bwino ngati kukubwera zinazake zoopsa. Koma oteteza anthu aja amakhala pamalo oti akhoza kuona bwinobwino chilichonse chimene chikuchitika. Mofanana ndi zimenezi, makolo anu akhoza kuona zoopsa zimene inuyo simungathe kuziona, chifukwa chakuti amadziwa zambiri komanso aona zambiri m’moyo. Mofanana ndi oteteza anthu amene akusambira aja, cholinga cha makolo anu n’chongokuthandizani kupewa zinthu zoopsa, osati kukuletsani kusangalala ndi moyo.

 Chifukwa chachiwiri: Makolo anu amafunitsitsa kukutetezani. Iwo amakulolezani kapena kukukanizani kuchita zinthu zina chifukwa cha chikondi. Mukawapempha chinachake, iwo amayamba kaye adzifunsa ngati kukulolezani kuchita chinthucho sikungakubweretsereni mavuto enaake pambuyo pake. Choncho, iwo angakulolezeni pokhapokha ngati atatsimikizira kuti zimene mwapemphazo sizikuikani pa mavuto.

Zimene Zingathandize Kuti Makolo Anu Asamakukanizeni Nthawi Zonse

Zimene mungachite

 Chilungamo: Dzifunseni kuti: ‘Kodi chifukwa chenicheni chimene ndikufuna kupitira kumeneko n’chiyani? Kodi zimene zikachitike kumeneko zimandisangalatsadi kapena ndikungofuna kusangalatsa anzanga? Kodi ndikufuna kupita chifukwa chakuti mtsikana kapena mnyamata amene ndimamufuna apitanso?’ Kenako auzeni makolo anu zoona zokhazokha. Pa nthawi ina nawonso anali achinyamata ndiponso amakudziwani bwino kwambiri. Ngakhale mutawabisira, iwo angadziwebe zolinga zanu. Choncho angasangalale ngati mutawauza chilungamo, ndipo angakuthandizeni pokuuzani zinthu zanzeru. (Miyambo 7:1, 2) Koma ngati simukuwauza chilungamo, makolo anu angaleke kukudalirani ndipo zimenezi zingachititse kuti azikukanizani zinthu zambiri.

 Nthawi imene mwawauzira: Musamapemphe makolo anu zinthu akangofika kunyumba kuchokera kuntchito kapena pamene akuchita zinthu zina. Muziwapempha nthawi imene alibe zochita zambiri. Komabe musamawapemphe nthawi itatha kale n’kuwaumiriza kuti akuyankheni msangamsanga. Makolo anu sangasangalale ngati simuwapatsa nthawi yokwanira yoganizira zimene mwawapemphazo. Iwo angasangalale ngati mutamawapempha zinthu nthawi idakalipo.

 Muzifotokoza zinthu momveka bwino: Musawasiye m’malere. Afotokozereni bwinobwino zimene mukufuna kuchita. Mwachitsanzo, iwo sangakuloleni kuchoka ngati mutayankha kuti, “Sindikudziwa,” atakufunsani mafunso otsatirawa: “Kodi kukakhala ndani ndi ndani?” “Kodi kukakhala munthu wamkulu aliyense?” kapenanso, “Kodi mukamaliza nthawi yanji?”

 Musamakayikire zolinga zawo. Musamaone makolo anu ngati adani anu. M’malomwake, muziwaona kuti ali kumbali yanu, chifukwa zoona zake n’zakuti iwo alidi kumbali yanu. Mukamaona kuti makolo anu ali kumbali yanu, simungalimbane nawo ndipo iwo angamakumvetseni kwambiri.

 Asonyezeni makolo anu kuti ndinu munthu wokhwima maganizo pomvera zimene akukuuzani. Mukamawamvera, amakulemekezani ndipo tsiku lina mukadzawapemphanso, zidzakhala zosavuta kuti akulolezeni.