Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?

Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?

 Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Elaine anati: “Nditaona kuti anzanga akusukulu ali ndi anzawo ambirimbiri owatsatira pa intaneti ndinaganiza kuti, ‘Ee, koma ndiye ndi otchukatu.’ Kunena zoona, ndinkawachitira nsanje.”

 Kodi inunso munayamba mwamvapo choncho? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani kuti musamakhumudwe chifukwa chakuti sindinu wotchuka pa intaneti.

 Kodi kukhala wotchuka kuli ndi mavuto otani?

 Pa Miyambo 22:1, Baibulo limati: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.” Choncho sikulakwa kufuna kukhala ndi mbiri yabwino ngakhalenso kufuna kuti anthu ena azikukonda.

 Komabe, nthawi zina kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuti anthu azikukonda kungachititse munthu kuyamba kuganiza kuti angakhale wosangalala pokhapokha ngati ali wotchuka. Kodi zimenezi zingakhale ndi vuto lililonse? Onya wazaka 16 angayankhe kuti inde. Taonani zimene ananena:

 “Ndaonapo anthu ena akuchita zinthu zachibwana kusukulu kwathu monga kudumpha pamalo ena ake aatali kwambiri n’cholinga choti atchuke.”

 Pofuna kuti anthu ena azichita nawo chidwi, ena amadzijambula akuchita zinthu zachibwana kenako n’kuziika pa intaneti. Mwachitsanzo, achinyamata ambiri amaposita pa intaneti mavidiyo osonyeza iwowo akudya mankhwala omwe amagwiritsidwa ntchito m’mashini ochapira, koma zinthu zimenezo n’zoti munthu sayenera kuchita.

 Baibulo limati: “Musachite chilichonse ndi mtima . . . wodzikuza.”​—Afilipi 2:3.

 Zoti muganizire:

  •   Kodi inuyo mumaona kuti kukhala wotchuka pa intaneti n’kofunika?

  •   Kodi mungaike moyo kapena thanzi lanu pangozi n’cholinga choti anzanu akuoneni kapenanso kukutamani?

 Kunamizira kukhala wotchuka

 Si nthawi zonse pamene anthu amachita zinthu zoika moyo wawo pangozi n’cholinga choti akhale otchuka. Mtsikana wina wazaka 22 dzina lake Erica anafotokoza njira inanso imene anthu ena amagwiritsa ntchito pofuna kuti atchuke. Iye anati:

 “Anthu ena amakonda kuposita zithunzi zambirimbiri zosonyeza mmene moyo wawo ukuyendera kuti azioneka ngati amacheza ndi anthu ambirimbiri. Zimenezi zimachititsa kuti azioneka ngati ndi otchuka.

 Cara wazaka 15 ananena kuti anthu ena amakonda kuchita zinthu mwachinyengo n’cholinga choti aoneke ngati otchuka. Iye anati:

 “Ndaonapo anthu akujambulitsa zithunzi zooneka ngati ali kuphwando linalake koma chonsecho ali kunyumba kwawo.”

 Matthew wazaka 22 akuvomereza kuti nayenso anachitapo zimenezi. Iye anati:

 “Ndinapositapo chithunzi n’kusonyeza ngati ndili ku Mount Everest, koma chonsecho sindinayambe ndapitapo ku Asia.”

 Baibulo limati: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

 Zoti muganizire:

  •   Ngati mumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, kodi mumachita zinthu mwachinyengo n’cholinga choti mutchuke?

  •    Kodi mumaposita zithunzi zosonyezadi mmene inuyo mulili kapenanso kulemba ndemanga zogwirizana ndi mfundo zimene mumayendera pa moyo wanu?

 Kodi kukhala ndi anthu ambiri okutsatira komanso okonda zinthu zomwe umaposita pa intaneti kuli ndi phindu?

 Anthu ambiri amaganiza kuti angakhale otchuka pa intaneti ngati ali ndi anthu ambiri owatsatira komanso okonda zimene amaposita. Matthew, yemwe tamutchula kale uja, akuvomereza kuti nayenso ankaganiza chonchi. Iye anati:

 “Ndinkafunsa anthu kuti, ‘Muli ndi anthu angati amene amakutsatirani pa intaneti?’ kapenanso kuti, ‘Ndi anthu ochuluka bwanji amene amakonda zimene mumaposita pa intaneti?’ Kuti ndiwonjezere chiwerengero cha anthu onditsatira, ndinayamba kutsatira anthu osiyanasiyana poganiza kuti nawonso ayamba kunditsatira. Ndinayamba kamtima kofuna kukhala wotchuka ndipo ndikamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, maganizo amenewa ankangokulirakulirabe.”

Kukhala otchuka pa intaneti kuli ngati kudya chakudya chosapatsa thanzi. Chimakoma kwa nthawi yochepa koma sichimakhutitsa.

 Mariya wazaka 25, ananena kuti anthu ena amadziona kuti ndi osafunika kapenanso kuti ndi ofunika potengera kuchuluka kwa anthu omwe amawatsatira pa intaneti komanso amene amakonda zimene amaposita. Iye anati:

 “Mtsikana akaika chithunzi chake pa intaneti, koma anthu ochepa okha ndi amene amulembera kuti achikonda, iye amayamba kudziona ngati wosaoneka bwino. N’zoona kuti maganizo amenewa ndi olakwika, koma ndi mmene anthu ambiri amamvera. Kuchita zimenezi kuli ngati kudzivutitsa wekha pa intaneti.”

 Baibulo limati: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.”​—Agalatiya 5:26.

 Zoti muganizire:

  •   Ngati mumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, kodi mumaona kuti amakuchititsani kuti muzikonda kudziyerekezera ndi anthu ena?

  •    Kodi mumadera nkhawa kwambiri kuchuluka kwa anthu amene akukutsatirani m’malo moganizira za anthu amene angakhale anzanu enieni?