Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Zithunzi pa Intaneti?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Zithunzi pa Intaneti?

Tayerekezani kuti muli ku holide ndipo mukusangalala kwambiri. Kenako mwaganiza zoti mufotokozere anzanu mmene mukusangalalira. Koma kodi muwauza bwanji? Kodi muwadziwitsa

  1. potumizira aliyense kadi?

  2. polembera aliyense imelo?

  3. poika zithunzi pa intaneti?

Pa nthawi imene agogo anu anali ndi zaka ngati zanu, n’kutheka kuti njira “A” ndi yokhayo imene akanatha kugwiritsa ntchito.

Pamene makolo anu anali ndi zaka ngati zanu, njira “B” ndi imene akanagwiritsa ntchito.

Masiku ano, achinyamata ambiri amene amaloledwa kuika zithunzi pa intaneti amakonda kugwiritsa ntchito njira “C.” Kodi ndi njira imene nanunso mumakonda? Ngati ndi choncho, nkhani ino ikuthandizani kuti mupewe mavuto ena.

 Kodi pali ubwino wotani?

Ndi yachangu. “Ndikasangalala pa ulendo winawake kapena ndi anzanga, ndikhoza kutumizira anzanga zithunzi zimene ndajambula nthawi yomweyo ndikadali wosangalala.”​—Melanie.

Ndi yosavuta. “N’zosavuta kuona zithunzi zatsopano zimene anzanga atumiza kusiyana ndi kugwiritsa ntchito imelo kuti udziwe zimene zikuwachitikira.”​—Jordan.

Imathandiza kulumikizana ndi anthu. “Anzanga ena komanso abale anga amakhala kutali kwambiri. Ndiyeno akamaika zinthunzi zawo pafupipafupi ine n’kumaziona, zimakhala ngati ndikuwaona tsiku lililonse.”​—Karen.

 Kodi pali kuopsa kotani?

Mukhoza kuika chitetezo chanu pangozi. Ngati kamera yanu imatha kusonyeza kumene muli, zithunzi zimene mwatumizazo zikhoza kuulula zinthu zina zimene simumafuna kuti anthu ena adziwe. Webusaiti ina inanena kuti: “Anthu ena amaika zithunzi zawo komanso zinthu zina pa intaneti n’kulembanso kumene ali. Zimenezi zikhoza kupereka mwayi kwa anthu amaganizo olakwika kuti agwiritse ntchito mapulogalamu apadera amene amatha kunena kumene munthuyo ali moti atha kumupeza mosavuta.”​—Digital Trends.

N’zoona kuti akuba ena amachita chidwi kwambiri ndi nyumba zimene kulibe anthu. Malinga ndi zimene webusaiti ya Digital Trends inanena, mbava zitatu zinathyola nyumba 18 eni ake atachoka. Kodi anadziwa bwanji kuti m’nyumbazo mukhala mulibe anthu? Iwo anafufuza mmene anthuwo ayendere pogwiritsa ntchito njira inayake ya pa intaneti. (cybercasing) Akubawo anaba katundu wa ndalama zoposa madola 100,000 a ku United States.

Mukhoza kuona zinthu zolakwika. Anthu ena sachita manyazi kutumiza china chilichonse kuti anthu aone. Mtsikana wina dzina lake Sarah anati: “Pamakhala mavuto ngati munthu akungoona zinthu zimene anthu amene atumiza sakuwadziwa. Zili ngati kuyenda m’malo achilendo popanda kugwiritsa ntchito mapu. N’zodziwikiratu kuti ukhoza kupita kumene samafuna kupita.”

Zikhoza kukuwonongerani nthawi. Mtsikana wina dzina lake Yolanda ananena kuti: “N’zosavuta kumangokhalira kuona zinthu zimene zangotumizidwa kumene komanso kuwerenga zimene anthu alemba. Ukhoza kufika pomaona foni sekondi iliyonse n’cholinga choti uone zinthu zatsopano zimene anthu atumiza.”

Muyenera kukhala munthu wodziletsa ngati muli ndi malo otumizira ena zithunzi a pa intaneti

Mtsikana wina dzina lake Samantha anati: “Ndikufunika kuchepetsa nthawi imene ndimathera pamalo otumizirana zithunzi pa intaneti. Pa nkhani yotumizirana zinthunzi pa intaneti, munthu umafunika kukhala wodziletsa.”

 Zimene mungachite

  • Khalani wotsimikiza kuti muzipewa kuika ndi kuona china chilichonse choipa. Baibulo limanena kuti: “Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.”—Salimo 101:3.

    “Nthawi ndi nthawi ndimaona zinthu zimene anthu ena atumiza, ndipo ndimasiya kuziona ngati ndikuona kuti zimene akutumizazo si zabwino.”Steven.

  • Muzipewa anthu amene satsatira mfundo zimene inuyo mumayendera chifukwa akhoza kukuchititsani kuti mutengere makhalidwe awo. Baibulo limanena kuti: “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akorinto 15:33.

    “Musamangoona zithunzi za anthu chifukwa choti ndi otchuka. Nthawi zambiri kuona zithunzi za anthu oterewa kumachititsa kuti munthu aone zinthu zotukwana, zolaula komanso zina zosakhala bwino.”​—Jessica.

  • Muyenera kudziikira malire kuti musamathere nthawi yochuluka mukuona zinthu pa intaneti kapenanso kuikapo zithunzi. Baibulo limati: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aefeso 5:15, 16.

    “Ndinasiya kuona zinthu za anthu amene amangoika zinthu zambirimbiri pa intaneti. Mwachitsanzo, zimadabwitsa kuti anthu ena akapita kunyanja amajambula zithunzi 20 za chinthu chimodzi n’kuziika pa intaneti. Zimatenga nthawi yambiri kuti munthu umalize kuona zithunzi zonsezo.”—Rebekah.

  • Onetsetsani kuti zithunzi zimene mumaika pa intaneti sizikupangitsa anthu kuona kuti inuyo ndiye munthu wofunika kwambiri. Paulo, yemwe analemba nawo Baibulo, ananena kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.” (Aroma 12:3) Musamaganize kuti anzanu akopeka ndi zithunzi zanu komanso zimene mumachita.

    “Anthu ena amatumiza zithunzi zambirimbiri zoti adzijambula okha. Ngati munthuyo ndi mnzanga, ndiye kuti ndikudziwa mmene amaonekera. Palibe chifukwa choti azichita kundikumbutsa potumiza zithunzi.”Allison.