Kalata Yoyamba ya Petulo 5:1-14

  • Wetani gulu la nkhosa za Mulungu (1-4)

  • Mukhale odzichepetsa komanso atcheru (5-11)

    • Muzitula nkhawa zanu zonse kwa Mulungu (7)

    • Mdyerekezi ali ngati mkango wobangula (8)

  • Mawu omaliza (12-14)

5  Choncho, ine monga mkulu mnzanu, amene ndinaona mmene Khristu anavutikira komanso ndikuyembekezera kudzalandira nawo ulemerero umene udzaonekere,+ ndikupempha akulu amene ali pakati panu kuti:  Wetani gulu la nkhosa za Mulungu+ zomwe zili mʼmanja mwanu. Monga oyangʼanira, muzigwira ntchito yanu, osati mokakamizika koma mofunitsitsa monga atumiki a Mulungu.+ Muziigwira ndi mtima wonse, osati chifukwa chofuna kupindulapo kenakake.+  Musamachite zinthu ngati mafumu pakati pa anthu a Mulungu,*+ koma muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.+  Ndipo mʼbusa wamkulu+ akadzaonekera, mudzalandira mphoto* yosawonongeka yomwe ndi yaulemerero.+  Chimodzimodzinso inu achinyamata, muzigonjera amuna achikulire.*+ Komanso nonsenu muzichita zinthu modzichepetsa, chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu odzikuza. Koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+  Choncho dzichepetseni pamaso pa Mulungu wathu wamphamvu* kuti adzakukwezeni nthawi yake ikadzakwana.+  Muzichita zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse,+ chifukwa amakufunirani zabwino.+  Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru+ chifukwa mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.*+  Choncho mukhale ndi chikhulupiriro cholimba ndipo mulimbane naye,+ podziwa kuti abale anu padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.+ 10  Mukavutika kwa nthawi yochepa, Mulungu yemwe amasonyeza kukoma mtima konse kwakukulu, amenenso anakuitanani kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu komanso kuti mulandire ulemerero wosatha,+ adzamalizitsa kukuphunzitsani. Iye adzakupatsani mphamvu,+ adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika+ komanso adzakulimbitsani. 11  Mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Ame. 12  Ndakulemberani kalata yachiduleyi kudzera mwa Silivano,*+ mʼbale amene ndikumuona kuti ndi wokhulupirika. Ndakulemberani zimenezi kuti ndikulimbikitseni ndi kukutsimikizirani kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu. 13  Mayi* amene ali ku Babulo, yemwe Mulungu anamusankha mwapadera ngati inuyo, komanso mwana wanga Maliko,+ akupereka moni. 14  Patsanani moni mwachikondi.* Nonse amene muli ogwirizana ndi Khristu, mukhale ndi mtendere.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “pakati pa anthu omwe ndi cholowa cha Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chipewa chachifumu chosawonongeka.”
Kapena kuti, “akulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.”
Kapena kuti, “ngati mkango wobangula umene ukufunafuna winawake woti umumeze.”
Yemwe amadziwikanso kuti Sila.
Mawu akuti “mayi,” nʼkutheka kuti akutanthauza mpingo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “popsopsonana mwachikondi.”