Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi N’chiyani Chingandithandize Ndikakumana ndi Mavuto?

Kodi N’chiyani Chingandithandize Ndikakumana ndi Mavuto?

Munthu wina aliyense angakumane ndi mavuto. Baibulo limati: ‘Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano ndipo amphamvu sapambana pankhondo chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.’ (Mlaliki 9:11) Choncho nawonso achinyamata amakumana ndi mavuto. Kodi amatani akakumana ndi mavutowo? Tiyeni tione zitsanzo ziwiri.

 REBEKAH

Makolo anga anasiyana ndili ndi zaka 14.

Ndinkavutika kukhulupirira kuti akusiyanadi ndipo ndinkaganiza kuti bambo adzabweranso. Ndinkaona kuti ankakonda kwambiri mayi anga ndipo sangawasiye. Ndinkaonanso kuti inenso sangandisiye.

Zinkandivuta kuuza aliyense zimene zinkachitikazo ndipo sindinkafuna kuziganizira. Zinkandikhumudwitsa kwambiri ngakhale kuti pa nthawiyo sindinkadziwa. Ndinayamba kuda nkhawa kwambiri komanso ndinkavutika kuti ndigone.

Mayi anga anali mnzanga wapamtima koma anamwalira ndi khansa ndili ndi zaka 19.

Ndinadandaula makolo anga atasiyana. Koma ndinavutika kwambiri mayi anga atamwalira. Ndimavutikabe mpaka pano. Ndimadabe nkhawa ndipo tulo sitibwera.

Komabe pali zinthu zingapo zimene zimandithandiza. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 18:1 limanena kuti si bwino kudzipatula. Choncho ndimayesetsa kucheza ndi anthu.

Ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndimayesetsa kuwerenga mabuku athu olimbikitsa omwe amafotokoza za Baibulo. Buku lina limene linandithandiza makolo anga atasiyana ndi lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa. Ndikukumbukira mutu wakuti, “Kodi Ndingasangalale Ngakhale Kuti Ndikuleredwa ndi Bambo Kapena Mayi Okha?” m’Buku Lachiwiri, womwe unandithandiza kwambiri.

Lemba lina limene limandithandiza ndikamada nkhawa ndi Mateyu 6:25-34. M’vesi 27, Yesu anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?”

Tonsefe timakumana ndi mavuto koma chitsanzo cha mayi anga chinandiphunzitsa kuti zimene timachita tikamakumana ndi mavutowo n’zofunika kwambiri. Mayiwo anakumana ndi mavuto aakulu monga kutha kwa banja ndiponso kudwala kwambiri mpaka kumwalira. Komabe anapitiriza kukhala ndi maganizo abwino ndiponso kukhulupirira kwambiri Mulungu. Sindidzaiwala zimene anandiphunzitsa zokhudza Yehova.

Zoti muganizire: Kodi kuwerenga Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza za Baibulo kungakuthandizeni bwanji kuthana ndi mavuto?Salimo 94:19.

 CORDELL

Bambo anga anamwalira ndili ndi zaka 17. Ndinakhumudwa kwambiri ndipo ndinkaona kuti limeneli linali vuto lalikulu kuposa lililonse pa moyo wanga.

Ndinkaona kuti si zoona kuti bambo amwaliradi. Ndinkaganiza kuti, ‘Adzuka mawa.’ Ndinkasowa mtengo wogwira.

Ine ndi achibale anga ndife a Mboni za Yehova ndipo anthu amumpingo wathu anatithandiza kwambiri bambo atamwalira. Iwo ankatipatsa chakudya, kukhala nafe limodzi ndiponso kutilimbikitsa kwambiri. Zimene anachitazi zinanditsimikizira kuti a Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni.—Yohane 13:35.

Lemba limene limandilimbikitsa kwambiri ndi 2 Akorinto 4:17, 18 lomwe limati: “Ngakhale kuti masautso amene tikukumana nawo ndi akanthawi ndipo ndi opepuka, masautsowo akutichititsa kuti tilandire ulemerero umene ukukulirakulira komanso wamuyaya, pamene tikuika maso athu pa zinthu zosaoneka, osati pa zooneka. Pakuti zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.”

Mbali yothera m’lembali inandithandiza kwambiri. Zimene zinachitikira bambo anga ndi zakanthawi koma zimene Mulungu watilonjeza zam’tsogolo ndi zosatha. Bambo atamwalira ndinaganizira kwambiri zimene ndinkachita pa moyo wanga ndipo ndinasintha zolinga zanga.

Zoti muganizire: Kodi kukumana ndi mavuto kungakuthandizeni bwanji kuona zolinga zimene muyenera kukhala nazo?—1 Yohane 2:17.