Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?

Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?

 Kodi makolo anu amakulolani kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti? Ngati amakulolani, nkhaniyi ikuthandizani kuganizira mbali zitatu zofunika izi:

Patsamba lino mupeza izi

 Kodi zikumandivuta kupeza nthawi yochita zinthu zina chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?

 Kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kuli ngati kukwera hatchi yamphamvu kwambiri. Mungathe kuilamulira kapena ingakulamulireni.

 “Ndikalowa pa intaneti ndimaganiza kuti ndingokhalapo kwa nthawi yochepa chabe, koma ndimangozindikira kuti ndakhalapo maola ambirimbiri! Malo ochezera a pa intaneti akhoza kutikomedwetsa komanso kutitayira nthawi.”​—Joanna.

 Kodi mukudziwa? Malo ochezera pa intaneti ndi okomedwetsa chifukwa ndi mmene anawapangira basi. Anthu amene anapanga mawebusaiti amenewa amadziwa mfundo yakuti kuti webusaiti ikakhala yotchuka kwambiri anthu ambirinso amalowapo ndipo otsatsa malonda amalipiranso ndalama zochuluka.

 Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zina ndimalephera kusunga nthawi chifukwa chokomedwa ndi kuona zinthu zosiyanasiyana pamalo ochezera a pa intaneti? Kodi ndingagwiritse ntchito nthawiyi kuchita zinthu zina zofunikira?’

 Zimene mungachite. Dziikireni malire pa nthawi imene mumakhala pamalo ochezera a pa intaneti ndipo muzichokapo nthawiyo ikakwana.

Dziikireni malire pa nthawi imene mumakhala pamalo ochezera a pa intaneti

 “Ndinaika malire a nthawi pafoni panga kuti nthawiyo ikakwana mapulogalamu ena amene ndimagwiritsa ntchito azitsekeka okha. Ndinachita zimenezi kwa kanthawi ndipo zinandithandiza kuti ndizigwiritsa ntchito bwino nthawi yanga pamalo ochezera a pa intaneti.”​—Tina.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”​—Aefeso 5:16.

 Kodi ndikumalephera kugona chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?

 Akatswiri ambiri amanena kuti achinyamata amafunika azigona maola osachepera 8, koma ambiri amagona maola ochepa kuposa pamenepa. Chimodzi mwa zinthu zimene zikuchititsa zimenezi ndi kugwiritsa ntchito malo ochezera pa intaneti.

 “Ndisanagone ndimakonda kuona zomwe zabwera pafoni panga, kenako ndimangozindikira kuti padutsa maola ambiri ndikuona zithunzi zimene anthu aika pamalo ochezera. Ndikuona kuti limeneli ndi vuto lomwe ndikufunika kusintha.”​—Maria.

 Kodi mukudziwa? Kusagona mokwanira kungayambitse nkhawa komanso matenda amaganizo. Pulofesa wina woona zamaganizo a anthu, dzina lake Jean Twenge, ananena kuti chimodzi mwa zinthu zinthu zimene zimapangitsa kuti anthu asamamve bwino m’thupi komanso kuti asamasangalale ndi kusagona mokwanira. Iye ananenanso kuti “m’kupita kwa nthawi” munthu amene amavutika akhoza kupezeka ndi “matenda aakulu ovutika maganizo.” a

 Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimagona maola angati usiku uliwonse?’ ‘Kodi ndimangokhalira kuona zinthu pamalo ochezera a pa intaneti pa nthawi imene ndikufunikira kupuma kapena kugona?’

 Zimene mungachite. Muziyesetsa kuika zipangizo zanu zamakono patali ndi bedi lanu mukamafuna kugona. Ngati n’zotheka, muzisiya kuyang’ana pasikirini yapazipangizo zanu kudakali maola awiri musanakagone. Ngati mukufuna kuti alamu ikudzutseni m’mawa, yesani kugwiritsa ntchito alamu yomwe sili mufoni kapena tabuleti yanu.

Muzisiya kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kudakali maola angapo mukamafuna kugona

 “Nthawi zina ndimagona mochedwa kwambiri kumangoyang’ana zinthu zomwe zabwera pafoni panga. Limeneli ndi vuto limene ndikuyesetsa kuti ndithane nalo. Ndikufunika ndichita zinthu monga munthu wamkulu zomwe zikuphatikizapo kumachita zinthu mwanzeru. Ndikufuna ndizigona mwamsanga n’cholinga choti tsiku lotsatira ndizichita zinthu zakupsa.”​—Jeremy.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

 Kodi malo ochezera a pa intaneti akumandisokoneza maganizo?

 Kafukufuku wina anasonyeza kuti pafupifupi hafu ya atsikana akusekondale omwe anachita nawo kafukufukuyu ananena kuti “amakhala okhumudwa pafupipafupi kapenanso kusowa chiyembekezo.” Nthawi zina malo ochezera a pa intaneti ndi amene amapangitsa kuti azimva choncho. Dr. Leonard Sax b ananena kuti: “Ukamakhala nthawi yaitali uli pamalo ochezera a pa intaneti, umayamba kudziyerekezera ndi anthu ena ndipo zimenezi zimapangitsa kuti uzivutika ndi maganizo.”

 “Ndi zofala kwambiri kuona achinyamata akudziyerekezera ndi anthu ena ndipo malo ochezera a pa intaneti amachititsa vutoli kukula kwambiri. Ukhoza kuona zithunzi za anthu ena kwa maola ochuluka n’kuyamba kuyerekezera moyo wako ndi wa anthuwo, kapenanso ungayambe kumasirira zimene anzako akuchita n’kumaona kuti ukumanidwa zinazake.”​—Phoebe.

 Kodi mukudziwa? Ngakhale kuti kucheza pa intaneti kungakuthandizeni kulumikizana ndi anzanu, koma sikungafanane ndi kucheza nawo pamasom’pamaso. Dr. Nicholas Kardaras analemba kuti: “Tikamacheza ndi anthu pazipangizo zamakono sitimasangalala ngati mmene timasangalalira tikamacheza ndi anthu pamasom’pamaso. Sitingakhutire kuti tachezadi ndi mnzathu.” c

 Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimamva kuti ndili ndekhandeka pambuyo poona zomwe anzanga akuchita?’ ‘Kodi ndimaona kuti moyo wanga ndi wobowa ndikayerekezera ndi zithunzi zimene anzanga amaika pamalo ochezera a pa intaneti?’ ‘Kodi ndimakhumudwa ngati anthu ochepa okha ndi amene alemba kuti akonda zomwe ndaika pamalo ochezera?’

 Zimene mungachite. Yesani kupumira kaye kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kwa masiku, mawiki kapenanso mwezi. Wonjezerani nthawi yomwe mumacheza ndi anzanu pamasom’pamaso kapenanso kuwaimbira foni. Kenako muone ngati mwayamba kukhala ndi nkhawa zochepa komanso osangalala pa nthawi yomwe mwasiya kaye kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti.

Kodi mungathe kuwonjezera nthawi yomwe mumacheza ndi anzanu pamasom’pamaso?

 Pamene ndinkagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti ndinkangokhalira kuganizira zimene anthu ena akuchita. Koma nditadilita mapulogalamu amenewa ndinamva ngati ndatula chimtolo cholemera, kenako ndinkapeza nthawi yambiri yochitira zinthu zofunika kwambiri.”​—Briana.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Koma aliyense payekha ayese zochita zake kuti aone kuti ndi zotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi zimene akuchitazo, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”​—Agalatiya 6:4.

a Kuchokera m’buku lakuti, iGen.

b Kuchokera m’buku lakuti, Why Gender Matters.

c Kuchokera m’buku lakuti, Glow Kids.