Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zogonana?

Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zogonana?

“Ndimangozindikira kuti ndayamba kuganiza zogonana mpaka kulephera kuganizako zina. Zimangokhala ngati ndasinthanitsa ubongo wanga ndi wa wina.”—Vera.

“Ndimaona kuti n’zosatheka kudzigwira ndikayamba kuganizira zokhudza kugonana. Bolanso kuphunzira kuuluka ngati mbalame kukhoza kukhala kophweka.”—John.

Kodi nanunso mumavutika ndi maganizo ofuna kugonana ngati mmene zilili ndi Vera ndi John? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikhoza kukuthandizani.

 Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

Mnyamata wina dzina lake Alex ananena kuti: “Ankolo anga anandiuza kuti Mulungu sakanandipatsa chilakolako cha kugonana, akanakhala kuti safuna kuti ndizichikhutiritsa.”

Zina mwa zimene ankolo a Alex ananena zinali zoona, chifukwa n’zoona kuti Mulungu ndi amene anatipatsa chilakolako cha kugonana, koma pa zifukwa zoyenera. Anthufe tilipobe mpaka pano chifukwa chakuti anthu amagonana n’kumabereka ana. Ndiye kodi pali chifukwa choyesetsera kuti musamaganizire kwambiri zogonana? Taganizirani zifukwa ziwiri izi:

  • Baibulo limaphunzitsa kuti cholinga cha Mulungu n’choti mwamuna ndi mkazi okwatirana okha ndi omwe ayenera kumagonana.—Genesis 1:28; 2:24.

    Ngati simunakwatire ndipo mumalemekeza lamulo la Mulunguli, kumangoganizira kwambiri zogonana kukhoza kukukhumudwitsani. Zimenezi zingachititse kuti ngati mutapeza mpata mugonanedi ndi munthu. Ndipotu anthu ambiri amene anachitapo zimenezi amadziimba mlandu.

  • Ngati mumapewa kuganizira kwambiri zogonana, mumaphunzira khalidwe lofunika kwambiri la kudziletsa.1 Akorinto 9:25.

Khalidweli ndi lofunika kwambiri kuti zinthu zizikuyenderani bwino panopa komanso m’tsogolo. Kafukufuku wina anasonyeza kuti ana odziletsa, akakula sakhala ndi mavuto ambiri okhudza thanzi, nkhawa chifukwa chosakasaka ndalama kapenanso kuphwanya malamulo a boma. a

 N’chifukwa chiyani si zophweka kuchotsa maganizo amenewa?

Kupewa kuganizira zogonana n’kovuta chifukwa tikamakula thupi limatulutsa mahomoni omwe amawonjezera chilakolako cha kugonana. Kuwonjezera pamenepo, tikukhala m’dziko lomwe zosangalatsa zambiri zimalimbikitsa chiwerewere.

“Mapulogalamu ambiri a pa TV amasonyeza ngati palibe vuto kugonana ndi munthu wina usanalowe m’banja. Zimenezi zingakupangitse kuyamba kuganizira kwambiri zogonana, n’kumaona kuti zilibe vuto lililonse.”—Ruth.

“Ndikakhala kuntchito, ndimamva anthu akukambirana zinthu zopanda pake zokhudza kugonana ndipo kamtima kamayamba dyokodyoko kuti ndimve zambiri. Anthu amachititsa kuti khalidwe la chiwerewere lizioneka ngati labwino moti zimakhala zovuta kuliona kuti ndi loipa.”—Nicole.

“Ukamaona zithunzi pa intaneti, n’zosavuta kuti utsegule zithunzi zosayenera. Ukangoona chithunzi chimodzi cholaula, zimakhala zovuta kuti uchiiwale. Paja chaona maso mtima suiwala.”—Maria.

Zinthu zomwe tatchulazi zingakupangitseni kumva ngati mmene mtumwi Paulo ankamvera. Iye analemba kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.”—Aroma 7:21.

Musalole kuti maganizo olakwika amange chisa pamutu panu

 Zimene mungachite

Muziganizira zinthu zina. Mukayamba kuganiza zogonana, muzipeza zochita zina. Zingaphatikizepo zimene mumakonda, masewera olimbitsa thupi kapenanso chilichonse chomwe chingapangitse kuti musiye kuganiza zolakwikazo. Mtsikana wina dzina lake Valerie ananena kuti: “Kuwerenga Baibulo n’kothandiza kwambiri chifukwa muli mfundo zapamwamba ndipo ukamaganizira mfundozo, sukhala ndi nthawi yoganizira zinthu zina zopanda pake.”

N’zoona kuti nthawi zina mukhoza kukhala ndi maganizo ofuna kugonana. Koma dziwani kuti ndi udindo wanu kusankha kuti muwagwiritsa ntchito bwanji. Ngati mutafuna, mukhoza kuchotsa maganizo oterowo.

“Ndikangoyamba kuganizira zokhudza kugonana, ndimachotsa maganizo olakwikawo n’kuyamba kuganizira zinthu zina. Ndimaonanso chimene chandipangitsa kuyamba kuganizira zolakwikazo. Ngati ili nyimbo kapena chithunzi, ndimachifufuta nthawi yomweyo.”—Helena.

Lemba lothandiza: “Zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, . . . pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afilipi 4:8.

Muzicheza ndi anthu abwino: Ngati anthu omwe mumacheza nawo amangokhalira kukambirana zogonana, zingakuvuteni kuti musamaganize zoipa.

“Zaka zapitazi, ndimavutika kwambiri ndi maganizo olakwika ndipo chifukwa chachikulu chimene chinkachititsa zimenezi ndi anthu ocheza nawo. Ukamacheza ndi anthu omwe amakonda kukambirana zinthu zolakwika, umayamba kuona kuti palibe vuto lililonse kuchita zomwe ukuganizazo.”—Sarah.

Lemba lothandiza: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miyambo 13:20.

Muzipewa zosangalatsa zosayenera. Palibe angatsutse kuti zosangalatsa zambiri masiku ano zimakhala ndi mbali zina zolimbikitsa chiwerewere. Nicole ananena kuti: “Kwa ine, nyimbo ndi zomwe zili ndi mphamvu kwambiri. Zimandichititsa kukhala ndi chilakolako champhamvu chogonana mpaka kufika poti ndimaona kuti n’zovuta kupirira.”

“Ndinayamba kuonera mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV okhudza zogonana. Sindinkadziwa kuti zikundisokoneza, koma ndinapezeka kuti ndayamba kuganizira kwambiri zogonana. Zinali zosavuta kudziwa kuti maganizo amenewa akubwera bwanji. Nditangosiya kuonera zinthu zolakwikazo, ndinasiyanso kuganizira kwambiri zogonana. Ndimaona kuti kusankha bwino zosangalatsa kumathandiza kuti usavutike kusiya kuganizira zinthu zosayenera.”—Joanne.

Lemba lothandiza: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu.”—Aefeso 5:3.

Mfundo yofunika kwambiri: Anthu ena amaona kuti n’zosatheka mpang’ono pomwe kupewa kuganizira zogonana. Koma Baibulo limanena kuti n’zotheka kupeweratu kuganizira zinthu zolakwika.

Lemba lothandiza: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.”—Aefeso 4:23.

a Anthu okwatirana amafunikanso kukhala odziletsa, choncho ndi nzeru kuyesetsa kuti mukhale ndi khalidwe limeneli musanakwatire.