Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndizidya Zakudya Zopatsa Thanzi?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizidya Zakudya Zopatsa Thanzi?

N’zosakayikitsa kuti mumadziwa zoti kusowa zakudya za magulu onse kukhoza kuwononga thanzi lanu. Ndipo munthu amene sadya zakudya zopatsa thanzi ali wamng’ono amachitanso zomwezo akadzakula. Choncho ndibwino kuti mukhale ndi chizolowezi chomadya zakudya zopatsa thanzi panopa.

 Kodi zakudya zopatsa thanzi ndi zotani?

Baibulo limatiuza kuti ‘tizichita zinthu mosapitirira malire,’ ndipo zimenezi zikuphatikizapo kudya. (1 Timoteyo 3:11) Choncho poganizira mfundoyi, ndibwino kudziwa kuti . . .

  • Tiyenera kudya zakudya za magulu onse. Pali magulu 5 a zakudya omwe ndi mkaka, mapuloteni, zipatso, masamba, ndi zakudya za m’gulu la chimanga ndi mpunga. Anthu ena amasiya kudya zakudya zina poopa kunenepa. Koma zimenezi zingachititse kuti thupi lanu lizisowekera zinthu zina zofunika.

    Tayesani izi: Fufuzani kapena funsani dokotala wanu kuti mudziwe ubwino wa zinthu zosiyanasiyana zomwe zimapezeka mu zakudya. Mwachitsanzo:

    Makabohaidireti angakupatseni mphamvu. Mapulotini amathandiza kuti thupi lanu lizilimbana ndi matenda komanso lizikula bwino. Zakudya zina za mafuta mukazigwiritsa ntchito moyenera, zingakuthandizeni kukhala amphamvu ndiponso kupewa matenda a mtima.

    “Ndimayesetsa kudya zakudya za magulu onse. Ndipotu sikulakwa kudyako switi imodzi kapena tizakudya tina tongosangalatsa m’kamwa. Koma sibwino kuti munthu azingokhalira kudya zinthu zimenezi. Umafunika kuti nthawi zonse uzidziikira malire n’cholinga choti uzidya za magulu onse.”—Brenda.

    Chakudya chimene chikusowekera zinthu zofunika m’thupi chili ngati mpando umene ukusowekera mwendo umodzi

  • Tizipewa kupitirira malire. Zimenezi zingaphatikizepo kusadya mokwanira, kudya kwambiri kapenanso kusiyiratu kudya zakudya zomwe munkazikonda.

    Tayesani izi: Onani mmene mwakhala mukudyera kwa mwezi umodzi. Ndiyeno dzifunseni kuti, ndi maulendo angati omwe munachita zinthu zomwe zatchulidwa pamwambazi? Nanga ndi zinthu ziti zimene mungasinthe n’cholinga choti muzidya moyenera?

    “M’mbuyomu, panali masiku ena omwe ndinkakonda kudya zakudya zopatsa mphamvu kwambiri pamene masiku ena ndinkayesetsa kuzipewa. Kenako ndinasiya kuganizira kwambiri kuchuluka kwa chakudya chopatsa mphamvu chimene ndikudya. Ndinkangoyesetsa kuti ndikangokhuta ndizisiya kudya. Zinanditengera nthawi ndithu koma panopa ndikuona kuti ndimadya moyenera.”—Hailey.

 Ndingatani kuti ndizidya zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse?

  • Muzidziwiratu zakudya zomwe mukufuna kudya. Baibulo limanena kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” (Miyambo 21:5) Choncho kuti muzidya zakudya zopatsa thanzi muyenera kumadziwiratu zakudya zoyenera.

    “Kuti uzidya zakudya zabwino umafunika kukonzekera, ndipo nthawi zambiri zakudya zopatsa thanzi zimayenera kukonzedwa kunyumba. Ngakhale kuti zingaoneke zovuta, pamapeto pake zimathandiza ndipo zingachititse kuti musamawononge ndalama.”—Thomas.

  • Muzidya zakudya zopatsa thanzi m’malo mwa zosafunika. Baibulo limanena kuti: “Usunge nzeru zopindulitsa.” (Miyambo 3:21) Nzeru zopindulitsa zidzakuthandizani kupeza njira zopezera kapena kukonzera chakudya chabwino.

    “Tsiku lililonse ndinkasinthanitsa chakudya chimodzi chosafunika kwenikweni ndi chakudya chopatsa thanzi. Mwachitsanzo, m’malo modya switi ndinkadya apozi. Pasanapite nthawi, ndinayamba kudya zakudya zambiri zopatsa thanzi m’malo mwa zosafunika.”—Kia.

  • Musamayembekezere zimene simungakwanitse. Baibulo limanena kuti: “Ukadye chakudya chako mokondwera.” (Mlaliki 9:7) Kudya zakudya zopatsa thanzi sikukutanthauza kuti muzidya zakudya zosasangalatsa zokhazokha kapena kuti muziganizira kwambiri chakudya chilichonse chomwe mukudya. Ngakhale mutakhala kuti mukufuna kuchepetsa thupi, muzikumbukira kuti cholinga chanu n’kukhalabe wa thanzi. Choncho musamayembekezere zimene simungakwanitse.

    “Posachedwapa ndinachepetsa thupi langa ndi makilogalamu osachepera 14. Komabe pa nthawiyi sindinakhalepo osadya, ndinkadyabe zakudya zoyenera komanso sindinkadziimba mlandu ndikadya zakudya zina zotsekemera. Ndinazindikira kuti kuchepetsa thupi kumatenga nthawi ndipo ndinkangofunika kusintha zinthu pa moyo wanga.”—Melanie.