Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa?

 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.” (Aroma 7:21) Kodi inuyo munakhalapo ndi maganizo amenewa? Ngati zili choncho, nkhaniyi ingakuthandizeni kuti musamachite zinthu zoipa zimene mukulakalaka.

 Zimene muyenera kudziwa

 Nthawi zambiri munthu amafuna kuchita zoipa chifukwa chokakamizidwa ndi anzake. Paja Baibulo limanena kuti “kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto15:33) Anzanu komanso zosangalatsa zimene mumakonda zingakuchititseni kuti muyambe kulakalaka zinthu zoipa moti mukhoza ‘kutsatira khamu la anthu pochita zoipazo.’—Ekisodo 23:2.

 “Mukamafunitsitsa kuti anthu ena azikukondani ndiponso kufuna kuti musakhale otsalira, mukhoza kuchita chilichonse chimene anthuwo akufuna.”—Jeremy.

 Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani mungavutike kupewa zoipa ngati mumafunitsitsa kuti anthu ena azikukondani?—Miyambo 29:25.

 Mfundo yofunika kwambiri: Musalole kuti anzanu akukakamizeni kuchita zinthu zoipa.

 Zimene mungachite

 Muzidziwa mfundo zimene mumayendera. Ngati simukudziwa bwino zimene mumakhulupirira, mungakhale ngati chidole chimene chimangochita chilichonse chimene anthu ena akufuna. Choncho ndi bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Tsimikizirani zinthu zonse. Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.” (1 Atesalonika 5:21) Mukadziwa bwino mfundo zimene mumakhulupirira, simungavutike kuzitsatira ndiponso kupewa kuchita chilichonse chosemphana ndi mfundozo.

 Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani mumakhulupirira kuti mfundo za Mulungu ndi zothandiza?

 “Ndaona kuti ndikamatsatira mfundo zimene ndimakhulupirira popanda kugonja ndikayesedwa, anthu ena amandilemekeza kwambiri.”—Kimberly.

 Chitsanzo chabwino cha m’Baibulo: Danieli. Ali wachinyamata, Danieli “anatsimikiza mumtima mwake” kuti azitsatira malamulo a Mulungu.—Danieli 1:8.

Ngati simukudziwa bwino zimene mumakhulupirira, mungayambe kukhala ngati chidole chimene chimangochita chilichonse chimene anthu ena akufuna

 Muzidziwa mavuto anu. Baibulo limanena kuti pali “zilakolako zaunyamata,” kapena kuti zinthu zimene achinyamata amalakalaka kwambiri. (2 Timoteyo 2:22) Zinthuzi zingakhale monga kulakalaka kugonana, kufuna kuti musakhale otsalira komanso kufuna ufulu wosagwirizana ndi msinkhu wanu.

 Zoti muganizire: Baibulo limanena kuti “munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.” (Yakobo 1:14) Kodi ndi zinthu zoipa ziti zomwe inuyo mumalakalaka kwambiri?

 “Muyenera kudzifufuza moona mtima kuti mudziwe mayesero amene angakugonjetseni mosavuta. Muyenera kufufuza mfundo zimene zingakuthandizeni kuti muzipewa kuchita zoipazo ndiponso kulemba mfundo zimene mungatsatire. Izi zingakuthandizeni kuti musadzagonje mukadzayesedwa.”Sylvia.

 Chitsanzo chabwino cha m’Baibulo: Davide. Nthawi zina ankalolera kuchita zinthu zimene anzake ankafuna komanso zimene iye ankalakalaka. Koma Davide ankaphunzirapo kanthu pa zimene ankalakwitsa ndipo ankayesetsa kusintha. Paja iye anapempha Yehova kuti: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.”—Sal. 51:10.

 Musalole kugonja. Baibulo limati: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni.” (Aroma 12:21) Izi zikutanthauza kuti mukhoza kusankha kuchita zinthu zabwino ngakhale mutayesedwa.

 Zoti muganizire: Kodi mungachite chiyani kuti musamagonje mukamayesedwa?

 “Ndimaganizira zimene zingachitike ngati nditagonja poyesedwa. Kodi ndikhala wosangalala? Mwina koma kwa nthawi yochepa chabe. Koma kodi ndipitiriza kukhala wosangalala? Ayi, ndidzanong’oneza bondo. Ndiye kodi ndi bwino kuchita zoipazi? Ayi.”​—Sophia.

 Chitsanzo chabwino cha m’Baibulo: Paulo. Ngakhale kuti Paulo ananena kuti ankalakalaka kuchita zoipa, ankadziletsa. Iye analemba kuti: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo.”—1 Akorinto 9:27.

 Mfundo yofunika kwambiri: Inuyo ndi amene muli ndi udindo wosankha zimene mungachite mukayesedwa.

 Musaiwale kuti zinthu zimene zingayese munthu sizikhalitsa. Mwachitsanzo, mlongo wina wazaka 20 dzina lake Melissa anati: “Zinthu zambiri zimene ndinkayesedwa nazo ndili kusekondale, sindimaziganizira n’komwe panopa. Zimenezi zimanditsimikizira kuti zinthu zimene ndikuyesedwa nazo panopa zidzathanso ndipo m’tsogolo ndidzaona kuti ndinachita bwino kwambiri kudziletsa.”