Yesaya 33:1-24

  • Chiweruzo komanso chiyembekezo kwa anthu olungama (1-24)

    • Yehova ndi Woweruza, Wotipatsa Malamulo komanso Mfumu (22)

    • Palibe amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala” (24)

33  Tsoka kwa iwe amene umawononga ena koma iwe sunawonongedwe,+Iwe amene umachitira ena zachinyengo pamene iwe sunachitiridwe zachinyengo. Ukadzangomaliza kuwononga ena, iwenso udzawonongedwa.+ Ukadzangomaliza kuchitira ena zachinyengo, iwenso udzachitiridwa zachinyengo.   Inu Yehova, tikomereni mtima.+ Chiyembekezo chathu chili pa inu. Tilimbitseni ndi dzanja lanu+ mʼmawa uliwonse.Mukhale chipulumutso chathu pa nthawi yamavuto.+   Mitundu ya anthu yathawa itamva phokoso lalikulu. Inu mukanyamuka, mitundu ya anthu imamwazikana.+   Mofanana ndi dzombe lanjala limene limawononga chilichonse, zinthu zimene inu munalanda anthu ena zidzalandidwaAnthu adzathamanga ngati chigulu cha dzombe kudzazitenga.   Yehova adzakwezedwa,Chifukwa amakhala pamalo apamwamba. Iye adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo.   Mʼmasiku anu, iye adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.Chimene amaona kuti ndi chamtengo wapataliNdi chipulumutso chake chachikulu,+ nzeru, kudziwa zinthu komanso kuopa Yehova.+   Taonani! Anthu awo otchuka akulira mofuula mʼmisewu.Amithenga amtendere akulira mopwetekedwa mtima.   Mʼmisewu ikuluikulu mulibe aliyense.Palibe munthu aliyense amene akuyenda mʼnjira. Iye* waphwanya pangano,Wakana mizindaNdipo sakusamala za munthu aliyense.+   Dzikolo likulira* ndipo lafota. Lebanoni wachita manyazi+ ndipo wawola. Sharoni wakhala ngati chipululuNdipo Basana ndi Karimeli akuyoyola masamba awo.+ 10  Yehova wanena kuti: “Tsopano ndinyamuka,Tsopano ndidzikweza.+Tsopano ndidziika pamwamba. 11  Munali ndi pakati pa udzu wouma ndipo mwabereka mapesi. Mzimu wanu udzakupserezani ngati moto.+ 12  Mitundu ya anthu idzakhala ngati zinthu zimene zimatsalira laimu akawotchedwa. Iwo adzayaka ndi moto ngati minga zimene zasadzidwa.+ 13  Inu amene muli kutali, imvani zimene ndikufuna kuchita. Ndipo inu amene muli pafupi, vomerezani kuti ndine wamphamvu. 14  Anthu ochimwa mu Ziyoni akuchita mantha.+Anthu ampatuko akunjenjemera kwambiri. Akufunsa kuti: ‘Ndi ndani wa ife amene angakhale pamene pali moto wowononga?+ Ndi ndani wa ife amene angakhale pafupi ndi moto umene sungazimitsike?’ 15  Ndi amene amayenda mʼchilungamo nthawi zonse,+Amene amalankhula zoona,+Amene amakana kupeza phindu pochita zinthu mosaona mtima komanso mwachinyengo,Amene manja ake amakana chiphuphu, mʼmalo mochilandira,+Amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi,Ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zinthu zoipa. 16  Iye adzakhala pamalo okwera.Malo ake othawirako otetezeka* adzakhala mʼmatanthwe movuta kufikamo.Iye adzapatsidwa chakudyaNdipo madzi ake sadzatha.”+ 17  Maso ako adzaona ulemerero wa mfumu.Adzaona dziko lakutali. 18  Mumtima mwako udzaganizira mozama za chinthu choopsa kuti: “Kodi mlembi ali kuti? Kodi ali kuti amene ankapereka msonkho uja?+ Kodi amene ankawerenga nsanja uja ali kuti?” 19  Anthu achipongwe simudzawaonanso,Anthu amene chilankhulo chawo nʼchovuta kumva,*Anthu achibwibwi amene simungamvetse zimene akulankhula.+ 20  Taonani Ziyoni, mzinda umene timachitiramo zikondwerero zathu.+ Maso anu adzaona kuti Yerusalemu ndi malo okhalamo abata,Tenti imene sidzachotsedwa.+ Zikhomo zake sizidzazulidwaNdipo zingwe zake sizidzadulidwa. 21  Koma kumeneko, Yehova WolemekezekaAdzakhala malo a mitsinje ndi a ngalande zikuluzikulu kwa ife.Malo amene sitima zankhondo sizidzapitakoKomanso amene sitima zikuluzikulu sizidzadutsako. 22  Chifukwa Yehova ndi Woweruza wathu,+Yehova ndi Wotipatsa Malamulo,+Yehova ndi Mfumu yathu.+Iye ndi amene adzatipulumutse.+ 23  Zingwe zanu zidzakhala zosamanga.Sizidzalimbitsa mtengo wautali wapasitima kapena kutambasula chinsalu chake. Pa nthawi imeneyo adzagawana zinthu zambirimbiri zimene analanda adani awo.Ngakhale anthu olumala adzatenga katundu wambiri amene alanda adani awo.+ 24  Ndipo palibe munthu wokhala mʼdzikolo amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala.”+ Anthu okhala mʼdzikolo adzakhululukidwa machimo awo.+

Mawu a M'munsi

Apa akunena mdani.
Mabaibulo ena amati, “lauma.”
Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼchozama.”