Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi ndi Bwino Kulonjeza Kuti Ndikhala Wodzisunga Mpaka Ndidzalowe M’banja?

Kodi ndi Bwino Kulonjeza Kuti Ndikhala Wodzisunga Mpaka Ndidzalowe M’banja?

 N’chifukwa chiyani anthu amalonjeza kuti akhala odzisunga?

Anthu ena amalemba kapena kulonjeza kuti sadzagonana ndi munthu mpaka atalowa m’banja.

Anthu anayamba kuchita zimenezi kwambiri mu 1990 pamene tchalitchi china chinachititsa msonkhano ku United States. Tchalitchichi chinayambitsa pulogalamu yotchedwa kuti, “Chikondi Chenicheni Chimadikira.” Pa msonkhanowu ankakambirana malangizo a m’Baibulo komanso kumalimbikitsa achinyamata kuti azikhala odziletsa mpaka atadzalowa m’banja.

Kodi zimenezi n’zothandizadi?

 Anthu amayankha zosiyanasiyana pa nkhaniyi.

  • A Christine C. Kim ndiponso a Robert Rector, anachita kafukufuku ndipo anati: “Zimene tapeza zikusonyeza kuti kulimbikitsa achinyamata kuchita zimenezi kukuthandiza kuti achinyamata ambiri azikhalabe odzisunga mpaka atalowa m’banja.”

  • Bungwe la Guttmacher linatulutsa zotsatira za kafukufuku wina yemwe anasonyeza kuti “zochita za achinyamata amene analonjeza kuti sadzagonana ndi munthu mpaka atalowa m’banja, sizikusiyana ndi zochita za amene sanalonjeze.”

N’chifukwa chiyani anthuwa anapeza zinthu zosiyana chonchi?

  • Anthu ena amene anachita kafukufukuyu ankayerekezera anthu amene sakhulupirira zinthu zofanana pa nkhani ya kugonana.

  • Pomwe ena ankayerekezera anthu omwe amakhulupirira zofanana pa nkhani ya kugonana.

Pothirira ndemanga zimene ochita kafukufuku wachiwiri uja anachita, Dr.  Janet Rosenbaum yemwe ndi katswiri pa nkhani ya moyo wa achinyamata ananena kuti: “Pamene zaka 5 zinkatha, zinali zovuta kudziwa kuti anthu amene analonjeza aja ndi ati, chifukwa zochita zawo sizinkasiyana.”

Njira imene imathandizadi

 N’zoona kuti anthu amene amalimbikitsa achinyamata kulonjeza kuti akhala odzisunga amakhala ndi zolinga zabwino. Koma vuto ndi lakuti samaphunzitsa anthuwo kukhala ndi makhalidwe abwino kuti akhale odzisunga. Mayi Rosenbaum aja ananenanso kuti “anthu amene amalonjeza kuti sadzagonana ndi munthu mpaka atalowa m’banja, amangochita zimenezi mwa chiphamaso. Sikuti munthu angakhale wodzisunga chifukwa choti walonjeza koma ngati akufunadi kuchita zimenezo kuchokera mumtima.”

Baibulo ndi limene lingathandizedi achinyamata kupewa kugonana mpaka atalowa m’banja. Angachite zimenezi ngati akugwiritsa ntchito ‘mphamvu zawo za kuzindikira, pophunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheberi 5:14) Wachinyamata akakhala wodzisunga amapewa mavuto ambiri monga kutenga mimba kapena matenda. Komanso amasonyeza kuti akulemekeza Mulungu amene anayambitsa zoti anthu azikwatirana.​—Mateyu 5:19; 19:4-6.

Malangizo amene amapezeka m’Baibulo amatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu. (Yesaya 48:17) Kunena zoona, n’zotheka kuti aliyense azitsatira lamulo la Mulungu lonena kuti, “thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Nthawi ikadzafika yoti achinyamatawo akwatire kapena kukwatiwa, adzasangala kwambiri ndipo sadzanong’oneza bondo chifukwa cha zimene anachita ali wachinyamata.