Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndizitani Munthu Wina Akandidzudzula?

Kodi Ndizitani Munthu Wina Akandidzudzula?

 Dzifunseni kuti

Nthawi zina anthufe timafunika kudzudzulidwa kapena kuti kulangizidwa kuti tigwire bwino ntchito kapena tisinthe mmene timaonera zinthu. Mwachitsanzo, taganizirani izi:

  1. Aphunzitsi anu akudzudzulani chifukwa choti simunakhoze bwino mayeso. Ndiye akuuzani kuti: “Muwerenge kwambiri kuti mudzakhoze bwino teremu yotsatira.”

    Kodi mungatani pamenepa?

    1. Kukana. (‘Aphunzitsi amenewa amandida.’)

    2. Kuvomereza. (‘Ndilimbikira kwambiri teremu yotsatira.’)

  2. Mwangomaliza kumene kukonza kuchipinda kwanu, koma amayi anu akuuzani kuti sikukuoneka bwino.

    Kodi mungatani pamenepa?

    1. Kukana. (‘Amavuta awa.’)

    2. Kuvomereza. (‘Ndikanathadi kukonzako bwino kuposa pamenepa.’)

  3. Mng’ono wanu akukuuzani kuti sasangalala ndi zoti muzingomulamulira ngati ndinu bwana.

    Kodi mungatani pamenepa?

    1. Kukana. (‘Kodi iyeyu amadziona ngati ndani?’)

    2. Kuvomereza. (‘Akunenadi zoona, ndikufunika kumachita zinthu momuganizira.’)

Achinyamata ena amakhala ngati tambula yagalasi yomwe sichedwa kusweka moti akangodzudzulidwa ngakhale pa zinthu zazing’ono, amakwiya kwambiri. Kodi inunso mumatero? Ngati ndi choncho, zinthu sizingakuyendereni bwino chifukwa kulangizidwa ndi mwayi waukulu ndipo zomwe mungauzidwezo zingakuthandizeni panopa komanso m’tsogolo.

Musamathawe malangizo chifukwa choti simukufuna kuwamva

 N’chifukwa chiyani ndiyenera kudzudzulidwa?

  • Ndinu wopanda ungwiro. Baibulo limanena kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yakobo 3:2) N’chifukwa chake timafunika malangizo nthawi zina.

    “Nthawi zonse ndimakumbukira kuti ndife anthu opanda ungwiro, ndipo nthawi zambiri timalakwitsa zinthu. Choncho ndikapatsidwa malangizo, ndimayesetsa kuwatsatira kuti ndisadzachitenso zomwe ndinalakwitsazo.”—David.

  • Mukhoza kukonza zolakwikazo. Baibulo limanena kuti: “Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.” (Miyambo 9:9) Izi zikusonyeza kuti kutsatira malangizo amene mwapatsidwa kukhoza kukuthandizani.

    “Poyamba munthu wina akandidzudzula sindinkamva bwino. Ndinkaona kuti wandichititsa manyazi. Koma panopa ndimasangalala wina akandidzudzula ndipo nthawi zina ndimachita kupempha kuti andiuze pamene ndikufunika kukonza.”—Selena.

N’zosavuta kupempha munthu wina kuti atiuze zimene talakwitsa. Koma ngati atayamba kutiuza yekha, zimakhala zowawa. Mtsikana wina dzina lake Natalie, atapatsidwa malangizo amene sankayembekezera ananena kuti: “Ndinadabwa nazo kwambiri ndipo zinandikhumudwitsa. M’malo mondiyamikira pa zimene ndinayesetsa kuchita, anandidzudzula.”

Kodi munakumanapo ndi zinthu ngati zimenezi? Nanga mungatani mutakumana nazo?

 Ndizitani wina akamandidzudzula?

  • Muzimvetsera.

    Baibulo limanena kuti: “Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu, ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.” (Miyambo 17:27) Ngati munthu wina akukulangizani, musamamudule mawu, musamayankhe mwaukali kapena kulankhula zinthu zimene mungadzanong’oneze nazo bondo.

    “Ndikapatsidwa malangizo, ndinkayamba kuganiza zodziikira kumbuyo. Koma ndaona kuti ndibwino kuti ndiziwagwiritsa ntchito kuti ulendo wina ndisadzalakwitsenso.”—Sara.

  • Muziganizira kwambiri malangizowo osati munthu yemwe wawaperekayo.

    N’zosavuta kuyamba kuona zolakwa za munthu yemwe wakudzudzulani. Koma ndi bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yakobo 1:19) Munthu akamakudzudzulani pamakhala kuti pali zinthu zina zomwe mwalakwitsadi. Choncho musamathawe malangizo chifukwa choti simukufuna kuwamva.

    “Makolo anga akamandilangiza ndinkakwiya kwambiri ndipo ndinkawauza kuti ‘ndikudziwa kale zomwe mukunenazo.’ Koma ndikamvetsera komanso kutsatira malangizowo zinthu zimandiyendera bwino.”—Edward.

  • Muzidziona moyenera.

    Mukapatsidwa malangizo sizitanthauza kuti ndinu olephera. Zimangosonyeza kuti inunso mumalakwitsa ngati mmene aliyense amachitira. Ndipo munthu amene akukulangizaniyo amafunikanso kudzudzulidwa nthawi zina. Baibulo limanena kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha.”Mlaliki 7:20.

    “Nthawi ina mnzanga anandipatsa malangizo omwe ndinkawaona kuti anali osafunikira. Ndinamuthokoza chifukwa cha malangizowo koma ndinakhumudwa kwambiri. Patapita nthawi ndinazindikira kuti zina mwa zimene anandiuzazo zinali zoona. Ndimaona kuti malangizowo anandithandiza kukonza zinthu zolakwika zomwe mwina ndikanatha kuzinyalanyalaza.”—Sophia.

  • Muzikhala ndi cholinga choti mukonze zinthu.

    Baibulo limanena kuti “munthu aliyense womvera chidzudzulo ndi wochenjera.” (Miyambo 15:5) Mukamavomereza malangizo omwe mwapatsidwa, simungakhumudwe koma mukhoza kungoyesetsa kukonza zomwe mwalakwitsazo. Kuti mukwanitse zimenezi, konzani ndandanda yabwino ndipo pakapita miyezi ingapo, onani zomwe mwakwanitsa kukonza.

    “Umafunika kukhala woona mtima wina akamakudzudzula chifukwa ngati ndiwe woona mtima, suvutika kuvomereza zomwe walakwitsa, kupepesa kenako n’kuona zomwe ungachite kuti ukonze zinthu.”—Emma.

Mfundo yofunika kwambiri: Baibulo limanena kuti: “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.” (Miyambo 27:17) Choncho mukamamvetsera wina akamakudzudzulani pa zomwe mwalakwitsa, zikhoza kukuthandizani panopa komanso mukadzakula.