Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Palibe Vuto Ngati Nditamangomvera Nyimbo Iliyonse?

Kodi Palibe Vuto Ngati Nditamangomvera Nyimbo Iliyonse?

“M’mawa ndikadzuka ndimaika nyimbo kuti ndizimvera. Ndikakwera galimoto ndimaikanso nyimbo. Ndimachitanso chimodzimodzi ndikabwerera kunyumba, ndikamapuma, ndikamakonza m’nyumba kapena ndikamawerenga. Nthawi zonse ndimakonda kumvera nyimbo.”—Carla.

Kodi nanunso mumakonda kwambiri nyimbo? Ngati zili choncho, nkhaniyi ikuthandizani kudziwa ubwino wa nyimbo komanso mavuto ake. Ikuthandizaninso kuti muzisankha nyimbo mwanzeru.

 Ubwino wake

Kumvera nyimbo tingakuyerekezere ndi kudya chakudya. Tikutero chifukwa chakuti timafunika kudya chakudya chabwino koma mosapitirira malire. N’chimodzimodzinso ndi nyimbo. Taganizirani izi:

  • Nyimbo zingakuthandizeni kuchepetsa nkhawa.

    “Ngati zinthu sizikundiyendera bwino pa tsiku limenelo, ndikhoza kungoika nyimbo zimene ndimakonda n’kuyamba kumva bwino nthawi yomweyo.”​—Mark.

  • Nyimbo zikhoza kukukumbutsani kale lanu.

    “Nthawi zina nyimbo inayake ingandikumbutse zinthu zabwino zimene zinandichitikira m’mbuyomu ndipo zimandisangalatsa kwambiri.”​—Sheila.

  • Nyimbo zingathandize kuti anthu azikhala ogwirizana.

    “Ndinapita kumsonkhano wamayiko wa Mboni za Yehova ndipo tonse pamsonkhanowu tinaimbira limodzi nyimbo yomaliza. Ndinalira chifukwa choona kuti nyimboyo inatithandiza kukhala ogwirizana ngakhale kuti tinkalankhula zilankhulo zosiyanasiyana.”​—Tammy.

  • Nyimbo zingakuthandizeni kuti mukhale ndi makhalidwe abwino.

    “Kuphunzira kuimba chida choimbira nyimbo kungakuthandizeni kukhala wakhama komanso woleza mtima. Munthu sangaphunzire kuimba nyimbo pogwiritsa ntchito chida chinachake kamodzi ndi kamodzi. Choncho kuti muphunzire lusoli muyenera kuchita khama kwambiri.”​—Anna.

Kodi mukudziwa? Buku lalikulu kwambiri m’Baibulo ndi la Masalimo ndipo lili ndi nyimbo zokwana 150.

Muzisankha bwino nyimbo ngati mmene mumachitira ndi chakudya

 Mavuto ake

Nyimbo zina zimakhala zoipa ngati mmene zilili ndi chakudya chothira poizoni. Tiyeni tione chifukwa chake tikutero.

  • Nyimbo zambiri zimalimbikitsa kugonana.

    “Ndimaona kuti pafupifupi nyimbo zonse zotchuka zimakhala zokhudza kugonana. Masiku ano oimba sabisanso chilichonse.”​—Hannah.

    Baibulo limati: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu.” (Aefeso 5:3) Dzifunseni kuti, ‘Kodi nyimbo zimene ndimakonda zimandilepheretsa kutsatira malangizowa?’

  • Nyimbo zina zingakuchititseni kukhala okhumudwa.

    “Nthawi zina ndikavutika kugona ndimamvera nyimbo zimene zimandichititsa kuganizira zinthu zokhumudwitsa. Ndimayamba kuganizira zinthu zoipa kwambiri chifukwa cha nyimbozo.”​—Tammy.

    Baibulo limati: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa.” (Miyambo 4:23) Dzifunseni kuti, ‘Kodi nyimbo zimene ndimamvera zimachititsa kuti ndiziganizira zinthu zokhumudwitsa?’

  • Nyimbo zina zingakuchititseni kukhala wolusa.

    “Nyimbo zimene zimalimbikitsa munthu kukwiya, kudziona kuti ndi wosafunika komanso kudana ndi ena zimakhala zoopsa. Ndimaona kuti ndikamvera nyimbozi ndimasintha kwambiri. Anthu ena m’banja lathu amandiuzanso kuti ndasintha.”​—John.

    Baibulo limati: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe, ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.” (Akolose 3:8) Dzifunseni kuti, ‘Kodi nyimbo zimene ndimamvera zimachititsa kuti ndizikhala wolusa kapena wouma mtima?’

Mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti, muzisankha nyimbo mwanzeru. Mtsikana wina dzina lake Julie amayesetsa kuchita zimenezi. Iye anati: “Nthawi zonse ndimaonanso nyimbo zimene ndimamvetsera ndipo ndikapeza yoipa, ndimaifufuta. Kuchita zimenezi si kophweka koma ndimaona kuti n’kofunika kwambiri.”

Mtsikana wina dzina lake Tara ananena kuti: “Nthawi zina pa wailesi pamamveka nyimbo yogunda bwino. Koma ndikamvera mawu a m’nyimboyo n’kuona kuti si abwino, ndimaona kuti ndi bwino kungosintha. Kuchita zimenezi kumakhala ngati kudziletsa kudya kachakudya kokoma kwambiri pambuyo poti wangoluma kamodzi kokha. Komabe ndikakwanitsa kudziletsa kumvera nyimbo zolimbikitsa kugonana ndikhozanso kupewa kugonana ndi munthu ndisanalowe m’banja. Ndimaona kuti nyimbo zikhoza kundisokoneza kwambiri ngati sindisamala nazo.”