Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

N’chifukwa Chiyani Sindikuyenera Kutsanzira Khalidwe la Anthu Omwe Amaonetsedwa M’mafilimu, pa TV ndi M’magazini?​—Gawo 2: Ya Anyamata

N’chifukwa Chiyani Sindikuyenera Kutsanzira Khalidwe la Anthu Omwe Amaonetsedwa M’mafilimu, pa TV ndi M’magazini?​—Gawo 2: Ya Anyamata

 Kodi ndi anthu otani amene tikukambirana m’nkhaniyi?

 Taonani mawu otsatirawa ndipo kenako muyankhe mafunsowo.

Mbali Yoyamba 1

Mbali Yachiwiri 2

Osamvera

Aulemu

Odzikonda

Okhulupirika

Ovuta

Achifundo

Aulesi

Olimbikira ntchito

Ochita zinthu motayirira

Odalirika

Achinyengo

Oona mtima

  1.   Kodi ndi mawu a mbali iti omwe mukuona kuti akufotokoza khalidwe la anyamata amene amaonetsedwa m’mafilimu, m’ma TV, komanso amene amajambulidwa m’magazini?

  2.   Nanga ndi mawu a mbali iti omwe akufotokoza khalidwe limene inuyo mukufuna mutamadziwika nalo?

 N’kutheka kuti mwayankha funso loyambalo kuti “mbali yoyamba,” ndipo pa funso lachiwiri mwayankha kuti “mbali yachiwiri.” Ngati mwayankha choncho, ndiye kuti zili bwino. Tikutero chifukwa zikusonyeza kuti mumafunitsitsa mutakhala munthu wabwino wosiyana ndi anthu amene amasonyezedwa m’mafilimu, m’ma TV, ndi m’magazini. N’chifukwa chiyani tikutero?

  •   Mafilimu ndi ma TV nthawi zambiri amasonyeza kuti anyamata ayenera kukhala ankhanza komanso osamvera. Buku lina linanena kuti anyamata otchuka amene amasonyezedwa pa TV, m’mafilimu komanso m’zamasewero amakhala “adzitho komanso ooneka ovuta . . . Amafuna kusonyeza kuti mnyamata ayenera kukhala wovuta komanso wosamvera.”​—Why Boys Don’t Talk​—and Why It Matters

     Zoti muganizire. Kodi kukhala munthu wovuta kungakuthandizeni kuti anthu azikonda kucheza nanu, kugwira nanu ntchito komanso kuti mudzakhale mwamuna wabwino? Munthu wina akakuputani, kodi mungasonyeze kuti ndinu mwamuna weniweni komanso wamphamvu chifukwa chobwezera kapena chifukwa chougwira mtima?

     Baibulo limati: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu, ndipo munthu wolamulira mtima wake amaposa munthu wogonjetsa mzinda.”—Miyambo 16:32.

    Ngati mumatha kuugwira mtima mukaputidwa, ndiye kuti ndinu wamphamvu kuposa msilikali

  •   Mafilimu ndi ma TV amasonyeza kuti anyamata ndi okonda zachiwerewere. Mnyamata wina wazaka 17 dzina lake Chris ananena kuti: “Pa TV ndi m’mafilimu nthawi zambiri amasonyeza anyamata akusintha atsikana kuposa mmene amasinthira zovala.” Mnyamata winanso wazaka 18 dzina lake Gary ananena kuti. “Pa TV ndi m’mafilimu amasonyeza kuti mnyamata weniweni ndi amene amakonda zachiwerewere.” Zimene ananena anyamatawa ndi zoona. Mwachitsanzo, m’mafilimu ena amasonyeza ngati kuti cholinga cha anyamata pa moyo ndi kuchita mapate, kumwa mowa komanso kuchita chiwerewere.

     Zoti muganizire: Kodi inuyo mumafuna kuti muzidziwika kuti ndinu wakhalidwe limeneli? Kodi mwamuna weniweni ndi amene amalemekeza akazi kapena ndi amene amaona kuti akazi analengedwa kuti azigonedwa ndi amuna basi?

     Baibulo limati: “Aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake m’njira yoyera kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana, ngati chimene anthu a mitundu ina osadziwa Mulungu ali nacho.”—1 Atesalonika 4:4, 5.

  •   Mafilimu ndi ma TV amasonyeza kuti anyamata ndi osadalirika. Mafilimu ndiponso mapulogalamu ambiri a pa TV omwe ndi otchuka, amasonyeza anyamata kuti ndi aulesi komanso osadalirika. Mwina ndiye chifukwa chake akuluakulu ena sadalira kwambiri anyamata. Gary, yemwe tamutchula kumayambiriro uja ananena kuti: “Nditafika zaka 16, ndinkavutika kupeza maganyu chifukwa anthu ambiri m’dera lathu ankakonda kupatsa maganyu azimayi okhaokha. Ankaona kuti anyamata onse ndi osadalirika.”

     Zoti muganizire: Kodi n’zoona kuti anyamata ndi osadalirika? Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu wodalirika?

     Baibulo limati: “Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono. M’malomwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.”—1 Timoteyo 4:12.

 Zimene muyenera kudziwa

  •   Mukhoza kutengera mosavuta makhalidwe amene mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV amalimbikitsa. Mwachitsanzo, mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV akhoza kukupangitsani kuona kuti mukufunika kutengera masitayilo a masiku ano kuti mutchuke. Mnyamata wina wazaka 17 dzina lake Colin ananena kuti: “Mapulogalamu otsatsa malonda a pa TV amasonyeza zimene anyamata ayenera kuvala komanso amasonyeza atsikana akuwagomera chifukwa cha zimene avalazo. Munthu ukangoona zimenezi umalakalaka utagula zovalazo. Ineyo kangapo konse ndinagula zovala chifukwa chotengeka ndi zimenezi.”

     Zoti muganizire: Kodi mumagula zovala zimenedi inuyo mukuona kuti n’zoyenera kapena chifukwa chongofuna kufanana ndi anzanu? Kodi ndani amene amapindula mukamaononga ndalama kugula zovala pongofuna kuti musaoneke wotsalira?

     Baibulo limati: “Musamatengere nzeru za nthawi ino.”—Aroma 12:2.

  •   Kutengera zochita za anthu oonetsedwa m’mafilimu ndi pa TV kungapangitse kuti atsikana asamakopeke nanu kwambiri. Taonani zimene atsikana ena ananena:

    •  “Ndingakonde mnyamata amene amasonyeza mmene iyeyo alilidi osati amene amangotengera zochita za anthu ena. Anyamata amene amayesetsa kuoneka ngati mashasha amandiseketsa kwambiri.”​—Anna.

    •  “Anthu otsatsa malonda amapangitsa anyamata kuganiza kuti akufunika kugula zipangizo zamakono kapena kumaoneka mogometsa kuti atsikana aziwafuna. Koma atsikana akamakula, amayamba kuchita chidwi ndi makhalidwe a amuna komanso mmene amachitira zinthu ndi anthu. Mwachitsanzo, atsikana amakonda anyamata amene ndi oona mtima komanso okhulupirika.”​—Danielle.

    •  “Nthawi zambiri anyamata ooneka bwino amakhala odzikonda komanso onyada. Ine anthu otere sandisangalatsa ndipo sindifuna kucheza nawo. Mnyamata akakhala wooneka bwino kwambiri koma wakhalidwe loipa sindikopeka naye.”​—Diana.

     Zoti muganizire: Baibulo limati Samueli “anali kukula ndi kukondedwa kwambiri ndi Yehova komanso anthu.” (1 Samueli 2:26) Kodi ndi makhalidwe ati amene mukufunika kukhala nawo kuti nanunso mukhale ngati Samueli?

     Baibulo limati: “Pitirizani kuchita chamuna.”—1 Akorinto 16:13.

 Zimene mungachite

  •   Muziganiza kaye musanatengere zimene mumaona m’mafilimu ndi pa TV. Baibulo limati: “Chilichonse cha m’dziko, monga chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake, sizichokera kwa Atate, koma kudziko.”—1 Yohane 2:16.

     Mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV amasonyeza makhalidwe amenewa ngati abwinobwino. Choncho musamangothamangira kutengera zimene mumaona. Cholinga cha anthu amene amapanga mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV nthawi zambiri chimakhala kufuna kupanga ndalama basi.

  •   Muzichita zimene mukudziwa kuti ndi zabwino. Baibulo limati: “Muvale umunthu watsopano umene Mulungu amapereka, kutanthauza kuti mwa kudziwa zinthu molondola, muchititse umunthu wanu kukhala watsopano mogwirizana ndi chifaniziro cha Mulungu.” Choncho musamatengere zimene mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV amalimbikitsa.​—Akolose 3:10.

     Kuti mukwanitse kutsatira malangizo amenewa, ganizirani makhalidwe amene mukufuna kukhala nawo omwe munasankha kumayambiriro kwa nkhani ino aja. Mungachite bwino kuyamba panopa kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amenewa komanso kuwasonyeza kwambiri.

  •   Muzicheza ndi anthu oyenera. Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” (Miyambo 13:20) Kodi kumene mumakhala kuli anthu amene amasonyeza kuti ndi anzeru? Anthu otere akhoza kukhala a m’banja mwanu monga bambo anu kapena ankolo anu. Ena akhoza kukhala anyamata anzanu kapena anthu odziwana nawo omwe amachita zinthu mwanzeru. Anyamata a Mboni za Yehova amatha kucheza ndi anyamata komanso azibambo achitsanzo chabwino omwe ali nawo mu mpingo umodzi. M’Baibulo mulinso anthu omwe anali zitsanzo zabwino monga Tito, yemwe anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa achinyamata.​—Tito 2:6-8.

     Yesani izi: Gwiritsani ntchito buku lakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo kuti muphunzire za anthu otchulidwa m’Baibulo amene anapereka chitsanzo chabwino kwa anyamata. Anthu ake ndi monga Abele, Nowa, Abulahamu, Samueli, Eliya, Yona, Yosefe ndi Petulo.